Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muyenera kukambirana momasuka komanso zinthu zisanafike poipa

Mungatani Ngati Munthu Amene Mumamukonda Akudwala Matenda Oti Sachira?

Mungatani Ngati Munthu Amene Mumamukonda Akudwala Matenda Oti Sachira?

MAYI ena dzina lawo a Doreen sanakhulupirire amuna awo a Wesley atapezeka ndi chotupa choopsa cha muubongo. * Pa nthawiyi n’kuti amuna awowo ali ndi zaka 54 zokha. Madokotala ananena kuti a Wesley amwalira pakangotha miyezi yochepa. A Doreen anati: “Atatiuza zimenezi sindinakhulupirire. Kwa milungu ingapo ndinkalephera kuchita zinthu bwinobwino. Ndinkangoona ngati ndikulota. Sindinkayembekezera kuti zimenezi zingatichitikire.”

Anthu ambiri amamva ngati mmene Mayi Doreen anamvera zoterezi zikachitika. Koma tiyenera kukumbukira kuti aliyense akhoza kupezeka ndi matenda oopsa oti sangachire. Ambiri amadzipereka kusamalira wachibale amene wapezeka ndi vuto lotereli ndipo tiyenera kuwayamikira. Komabe kusamalira munthu amene ali ndi matenda oti sachira si kophweka. Ndiye kodi munthu amene akuyang’anira wodwala wotereyu angatani kuti azitha kumusamalira bwino komanso kumulimbikitsa? Nanga angalimbane bwanji ndi nkhawa zimene amakhala nazo pa nthawi yonse imene akusamalira wodwalayo? Ndiponso kodi ayenera kuyembekezera zotani masiku oti munthuyo amwalire akamayandikira? Koma choyamba tiyeni tikambirane mmene zinthu zilili masiku ano zimene zikuchititsa kuti kudwazika munthu amene ali ndi matenda oti sachira, kuzikhala kovuta kwambiri.

ZIMENE ZIKUCHITIKA MASIKU ANO

Masiku ano madokotala apeza njira zamakono zimene zikuchititsa kuti anthu odwala asamafe msanga. Koma zaka 100 zapitazo, ngakhale m’mayiko olemera, anthu ambiri sankakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Zinali choncho chifukwa anthu akatenga matenda kapena akachita ngozi ankafa mofulumira. Komanso zipatala zinali zochepa ndipo ambiri ankangosamalidwa kunyumba ndi achibale mpaka kumwalira.

Koma masiku ano madokotala akugwiritsa ntchito njira zamakono zomwe zikuchititsa kuti munthu amene akudwala asamwalire msanga. Mwachitsanzo, anthu amene ali ndi matenda amene poyamba munthu ankafa nawo pasanapite nthawi yaitali, masiku ano akumakhala ndi moyo kwa nthawi ndithu. Izi zili choncho chifukwa panopa kuli njira komanso mankhwala otalikitsa moyo. Komabe sikuti zimenezi zimachititsa kuti munthu achire. Nthawi zambiri wodwalayo amakhala ndi mavuto ambiri moti amafunika kumusamalira pa chilichonse. Ndipotu kusamalira munthuyo sikhala nkhani yamasewera.

Masiku ano ambiri amapita ndi odwala kuchipatala ndipo izi zikuchititsa kuti anthu ambiri azifera kuchipatala osati panyumba. Komanso ambiri sakhalapo munthu akamamwalira ndipo ena sanaonepo munthu akumwalira. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri amada nkhawa ndi zimene zingachitikire wachibale wawo amene akudwala matenda oti sachira, choncho sadziwa kuti angamamusamalire bwanji. Ndiye kodi n’chiyani chingawathandize?

MUYENERA KUKONZEKERATU

Monga taonera m’chitsanzo cha Mayi Doreen chija, anthu ambiri amasowa mtengo wogwira munthu amene amamukonda akapezeka ndi matenda oti sachira. Amakhala ndi nkhawa, mantha komanso chisoni. Komabe kodi n’chiyani chingawathandize kukonzekeratu zomwe zingachitike? Mtumiki wina wokhulupirika wa Mulungu anapemphera kuti: “Tisonyezeni mmene tingawerengere masiku athu kuti tikhale ndi mtima wanzeru.” (Salimo 90:12) Apa mfundo ndi yakuti, muyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu kuchokera pansi pa mtima. Muzimupempha kuti akuthandizeni ‘kuwerengera masiku’ mwanzeru. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mudziwe zoyenera kuchita pa masiku amene munthuyo angakhale ndi moyo.

Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kukonzekera bwino. Ngati wodwalayo akutha kulankhula ndipo sangadandaule kukambirana nkhaniyo, ndi bwino kumupempha kuti asankhiretu munthu woti azidzamusankhira zochita akamadzalephera kulankhula. Muyeneranso kukambirana momasuka ngati akufuna kuti adzagonekedwe m’chipatala, adzapatsidwe thandizo linalake kapena akadzasiya kupuma adzamuthandize kuti ayambirenso. Izi zingathandize kuti pasadzakhale kusamvetsetsana komanso kuti achibale asadzadziimbe mlandu poganiza kuti sanamusankhire zimene iye ankafuna. Kukambirana moona mtima komanso kuchita zimenezi zinthu zisanafike poipa, kungathandize achibale kuti aziganizira kwambiri zimene angachite posamalira wodwalayo. Baibulo limati: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima, koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.”​—Miyambo 15:22.

KODI MUNGATHANDIZE BWANJI?

Nthawi zambiri, ntchito yaikulu ya munthu amene akusamalira matenda imakhala kulimbikitsa wodwalayo. Muyenera kutsimikizira wodwalayo kuti mumamukonda kwambiri ndipo simumusiya yekha. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzimuwerengera nkhani kapena kumuimbira nyimbo zolimbikitsa komanso zosangalatsa. Odwala ambiri amalimbikitsidwa wachibale akawagwira dzanja n’kumawalankhula mwachikondi ndi mawu apansipansi.

Ndi bwinonso kuuza wodwalayo munthu aliyense amene wabwera kudzamuona, kaya pomuuza dzina lake kapena kufotokoza zinthu zina zimene zingathandize kuti amudziwe. Lipoti lina linati: “Wodwala angalephere kuchita zinthu zina komabe amatha kumva, ngakhale akamaoneka ngati wagona. Choncho si bwino kulankhula zinthu zimene simukanalankhula zikanakhala kuti munthuyo ali m’maso.”

Ngati ndi zotheka, muzipemphera ndi wodwalayo. Baibulo limati pa nthawi ina mtumwi Paulo ndi anzake anali pa mavuto aakulu moti zoti angakhale ndi moyo sizinkadziwika. Kodi n’chiyani chinawathandiza? Paulo anachonderera anzake kuti: “Inunso mungathandizepo mwa kutiperekera mapembedzero anu.” (2 Akorinto 1:8-11) Choncho pemphero lochokera pansi pa mtima limathandiza kwambiri pa nthawi ya mavuto komanso pamene wina akudwala.

MUYENERA KUVOMEREZA NGAKHALE KUTI N’ZOVUTA

Zimakhala zowawa kwambiri ngati munthu ukudziwa kuti wachibale amene akudwala sachira. Anthufe sitinalengedwe kuti tizifa, n’chifukwa chake zimativuta kuvomereza. (Aroma 5:12) Mpake kuti Mawu a Mulungu amati imfa ndi “mdani.” (1 Akorinto 15:26) Choncho si zachilendo kuti anthufe sitifuna n’komwe kuganiza zoti wachibale wathu amwalira.

Komabe kukonzekereratu kungathandize kuti tisakhale ndi mantha kwambiri koma tizingoyesetsa kuchita zinthu zomwe zingathandize kuti tisamadandaule kwambiri. Zinthu zina zimene zingachitike zatchulidwa m’bokosi lakuti, “ Zimene Wodwala Amachita Kukatsala Milungu Yochepa Kuti Amwalire.” Sikuti zimene zatchulidwazi zimachitikira wodwala aliyense komanso sikuti nthawi zonse zimachitika m’ndondomeko yomweyi. Komabe odwala ambiri amasonyeza zina mwa zizindikiro zimenezi.

Wodwalayo akamwalira, muyenera kudziwitsa munthu amene munakambirana naye kale ndipo anavomera kuti adzakuthandizani. Tiyenera kudziwa kuti pamafunika kulimbikitsa anthu a m’banja la womwalirayo komanso onse amene akhala akusamalira matendawo. Tingawauze mfundo yoti m’bale wawoyo sakumvanso ululu uliwonse chifukwa Mlengi wathu amatitsimikizira kuti “akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlaliki 9:5.

YEHOVA NDI AMENE ANGAKUTHANDIZENI KWAMBIRI

Ndi bwino kuphunzira kuti tizilandira thandizo lililonse limene tapatsidwa

Muyenera kudalira Yehova kuti akuthandizeni pa nthawi ya matendayo komanso pamene wodwalayo wamwalira. Yehova angakuthandizeni pogwiritsa ntchito anthu ena, omwe angachite zinthu kapena kulankhula mawu olimbikitsa. Mayi Doreen aja anati: “Ndinaphunzira kuti ndizilandira thandizo lililonse limene munthu wandipatsa. Ndipotu anthu ambiri anatithandiza. Ine ndi mwamuna wanga tinkadziwa kuti zonsezi zinkachokera kwa Yehova. Zinali ngati Yehova akutiuza kuti: ‘Ndili nanu pa nthawi yovutayi ndipo sindikusiyani.’ Sindidzaiwala zimene zinachitikazi.”

Yehova Mulungu ndi amene angatithandize kwambiri pa nthawi ya mavuto. Iye ndi amene anatilenga ndipo amamvetsa mavuto athu komanso chisoni chomwe tili nacho. Yehova amafunitsitsa kutipatsa zonse zimene zingatithandize kuti tipirire ndipo ali ndi mphamvu yochita zimenezi. Chosangalatsa n’chakuti watilonjeza kuti posachedwapa athetsa imfa ndipo aukitsa anthu mamiliyoni ambiri amene ali m’manda. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Zikadzatero aliyense adzaona kuti mawu amene mtumwi Paulo analemba akwaniritsidwa. Mawu ake ndi akuti: “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”​—1 Akorinto 15:55.

^ ndime 2 Mayina asinthidwa.