Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pakachitika Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi

Pakachitika Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi

Andrew, yemwe amakhala ku Sierra Leone, anati: “Matope komanso madzi atasefukira kumene tinkakhala, katundu wathu yense anawonongeka. Tinasowa chochita ndipo tinkaona kuti palibenso chabwino.”

David wa ku Virgin Islands, yemwe kwawo kunawomba mphepo yamkuntho, ananena kuti: “Mphepoyo itatha tinabwerera kunyumba ndipo tinapeza kuti zinthu zathu zonse zawonongeka. Tinasowa chonena ndipo mwana wanga wamkazi anangogwada n’kuyamba kulira.”

ANTHU amene ngozi zamwadzidzidzi zinawachitikirapo angathe kumvetsa mmene munthu amamvera zoterezi zikachitika. Ena amasokonezeka maganizo, amakhala ndi nkhawa, amalephera kugona ndipo ena amalephera kuvomereza zimene zachitikazo. Enanso amakhumudwa n’kumaona kuti alibenso tsogolo.

Ngati inunso katundu wanu yense wawonongeka chifukwa cha ngozi zoterezi, mungayambe kuona kuti simungathe kupirira ndipo palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Komabe Baibulo limafotokoza kuti pali chifukwa chokhalira ndi moyo ndipo mungathe kukhala ndi chiyembekezo choti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino.

BAIBULO LIMATITHANDIZA KUONA KUTI PALI CHIFUKWA CHOKHALIRA NDI MOYO

Lemba la Mlaliki 7:8 limanena kuti: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.” Ngozi yamwadzidzidzi ikangokuchitikirani, mukhoza kumaona kuti palibenso chiyembekezo chakuti zinthu zikhalanso bwino. Koma mukaleza mtima n’kumayesetsa kuti muyambirenso kukhala bwinobwino, moyo wanu ukhoza kuyambiranso kuyenda bwino.

Baibulo limanena za nthawi imene ‘sikudzamvekanso kulira kokweza mawu kapena kulira kwachisoni.’ (Yesaya 65:19) Zimenezi zidzachitika Ufumu wa Mulungu ukadzasintha dzikoli n’kukhala paradaiso. (Salimo 37:11, 29) Nthawi imeneyo sikudzachitikanso ngozi ngati za kusefukira kwa madzi kapena mphepo yamkuntho. Sitidzakumbukiranso mavuto komanso zinthu zochititsa mantha zomwe tinakumana nazo chifukwa cha ngozi zimenezi, popeza Mulungu Wamphamvuyonse akulonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”​—Yesaya 65:17.

Tangoganizani! Mlengi wa zinthu zonse wakonza zokupatsani “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino” mu Ufumu womwe waukhazikitsa. (Yeremiya 29:11) Kodi kudziwa zimenezi kungathandizedi munthu kuona kuti pali chifukwa chokhalira ndi moyo? Sally, yemwe tamutchula munkhani yoyamba ija, anafotokoza kuti: “Kukumbukira zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzatichitire m’tsogolomu, kungatithandize kuti tiziiwalako zakale n’kumapirira mavuto amene tikukumana nawo.”

Mungachite bwino kuphunzira zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu posachedwapa. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa kuti ngakhale mutakumana ndi mavuto chifukwa cha ngozi zamwadzidzidzi, mungathe kupirira n’kumayembekezera nthawi imene sikudzakhalanso ngozi zoterezi. M’Baibulo mulinso malangizo amene angakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita mukakumana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi. Taonani ena mwa malangizo amenewa.