Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kusankhana Mitundu

Kusankhana Mitundu

Kodi mitundu ya anthu inachokera kuti?

“Adamu anatcha mkazi wake dzina lakuti Hava, chifukwa anali kudzakhala mayi wa munthu aliyense wamoyo.”—Genesis 3:20.

ZIMENE AKATSWIRI AMANENA

Nthambi ya bungwe la United Nations ya UNESCO, inanena kuti: “Mitundu yonse ya anthu inachokera ku mtundu umodzi ndipo makolo athu ndi amodzi.”—Declaration on Race and Racial Prejudice, 1978.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu analenga anthu awiri, Adamu ndi Hava, ndipo anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Choncho, Adamu ndi Hava ndi amene anabereka anthu onse. Kenako chigumula chinapha anthu onse amene anali padziko lapansi, kupatulapo Nowa, mkazi wake, ana awo aamuna atatu komanso akazi a ana awowo. Baibulo limanena kuti anthu tonsefe tinachokera kwa ana a Nowa.—Genesis 9:18, 19.

 Kodi pali mtundu wapamwamba kuposa mitundu ina?

“Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.”Machitidwe 17:26.

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

M’zaka za m’ma 1900, anthu ena anayamba kutsatira mfundo zolimbikitsa kusankhana mitundu. Mwachitsanzo, gulu la Nazi linkanena kuti mtundu wawo ndi wapamwamba chifukwa ali ndi majini enaake osiyana ndi a anthu ena onse. Komatu nthambi ya bungwe la United Nations tatchula ija, inanenanso kuti: “Anthu a mitundu yonse ndi ofanana chifukwa anachokera kwa kholo limodzi.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Lemba la Machitidwe 10:34, 35 limanena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” Pa chifukwa chimenechi, palibe munthu amene anganene kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa wina.

Yesu anatchula mfundo imene Akhristu ayenera kutsatira pamene ananena kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mateyu 23:8) Iye anapempherera ophunzira ake kuti akhale ogwirizana komanso kuti “akhale mu umodzi weniweni,” osati ogawanika chifukwa cha kusiyana mitundu.—Yohane 17:20-23; 1 Akorinto 1:10.

Kodi kusankhana mitundu kudzatha?

“M’masiku otsiriza, phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika ndipo . . . , mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.”Yesaya 2:2.

ZIMENE ANTHU ENA AMAGANIZA

Chifukwa choti kusankhana mitundu kukungopitirirabe, anthu ambiri amakayikira ngati zimene maboma akuchita pa vutoli zingathandizedi. Anthu ena afika poganiza kuti kusankhana mitundu sikudzatha.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu sadzalola kuti kusankhana mitundu kukhalepo mpaka kalekale. Mu Ufumu wake, anthu ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse,” azidzamutumikira mogwirizana ndiponso azidzakondana kwambiri. (Chivumbulutso 7:9) Ufumu wa Mulungu suli mumtima mwa munthu koma ndi boma limene lidzabweretsa madalitso ambiri padziko lapansi. Dziko lapansili ndi malo amene Mulungu anakonza kuti anthu onse azikhalapo popanda kusankhana mitundu. *

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 wa buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.