Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | ELDAR NEBOLSIN

Katswiri Woimba Piyano Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri Woimba Piyano Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Eldar Nebolsin amakhala ku Uzbekistan ndipo ndi woimba wodziwika padziko lonse kuti amaimba bwino piyano. Iye anaimbapo ku London, Moscow, St. Petersburg, New York, Paris, Rome, Sydney, Tokyo, ndi ku Vienna. Eldar anakulira ku Soviet Union ndipo sankakhulupirira Mulungu. Koma kenako anadziwa kuti kuli Mulungu ndiponso kuti Mulunguyo ndi amene analenga anthu. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za luso lake loimba.

Kodi munayamba bwanji kuimba?

Makolo anga onse amaimba piyano ndipo anayamba kundiphunzitsa ndili ndi zaka 5. Kenako ndinakaphunziranso kusukulu ina yophunzitsa kuimba mu mzinda wa Tashkent.

Tatiuzeni vuto limene limakhalapo munthu akamaimba limodzi ndi oimba ena.

Gulu lililonse limakhala losiyana ndi linzake. Gulu la oimbawa limakhala lalikulu kwambiri ndipo limaimba mogwirizana potsatira zimene mtsogoleri wawo akuwauza. Choncho zimakhala zovuta kuti munthu woimba piyano agwirizane bwinobwino ndi oimba enawo komanso motsatira zimene mtsogoleri akufuna. Zili ngati mmene zimakhalira anthu awiri akamalankhulana. Ayenera kumayankhizana, m’malo moti wina azingolankhula yekha. Nthawi zambiri timangokhala ndi mpata woyeserera kamodzi kapena kawiri kokha kuti tithe kuzolowera kuimbira limodzi.

Kodi mumakonzekera kwa nthawi yaitali bwanji?

Pafupifupi maola atatu patsiku. Sindimangophunzira mmene ndingaimbire nyimbo zovuta, koma ndimaphunziranso mmene nyimboyo anailembera ndipo ndimachita zimenezi popanda kuiimba. Chinthu china chimene ndimachita pa nthawiyi ndi kuphunzira nyimbo zina zopekedwa ndi munthu amene anapeka nyimbo imene ndikufuna kuimbayo. Zimenezi zimandithandiza kuidziwa bwino nyimbo imene ndikufuna ndikaimbeyo.

Kodi mumadziwa bwanji kuti uyu amaimba bwino piyano?

Zimene amachita ndi piyanoyo. Choyenera kudziwa n’choti zimene zimachitika mkati mwa piyano ndi zofanana ndi zimene zimachitika tikamaimba ng’oma. Munthu akadina batani la piyano phokoso lake limangomveka kamodzi kenako limayamba kuchepa mpaka kusiyiratu.  Izi ndi zosiyana ndi zida zoimba ndi pakamwa kapena mawu a munthu chifukwa phokoso lake likhoza kumangolirabe kwa kanthawi kapenanso kumawonjezereka. Zimakhala zovuta kuti ukamaimba piyano, uichititse kuti phokoso lake lisathe msanga. Koma woimbayo angachite zimenezi mwa kuyendetsa zala pang’ono komanso kuponda kachitsulo kamene kali mbali yakumanja kwa piyanoyo komwe kamathandiza kuti phokoso lisathe msanga komanso kuti lizimveka mosiyanasiyana. Munthu woimba akazolowera zimenezi, amatha kupangitsa kuti piyanoyo izimveka ngati chitoliro, lipenga kapena ngati zipangizo zingapo akuziimbira limodzi. Komanso amatha kuipangitsa kuti izimveka ngati mawu a munthu.

Ndi zoonekeratu kuti mumakonda nyimbo, si choncho?

Ee, ndi zoona. Ndimakonda nyimbo chifukwa ndimaona kuti nyimbo zimatha kusonyeza mmene munthu akumvera ndipo nthawi zina imasonyeza zinthu zomwe n’zovuta kuzifotokoza ndi mawu.

Nanga ndi chani chinakupangitsani kuyamba kuganizira za Mulungu?

Kunyumba kwathu kunali mabuku ambirimbiri omwe bambo anga anabweretsa kuchokera ku Moscow. Buku lomwe linkandichititsa chidwi kwambiri ndi limene linali ndi nkhani za m’Baibulo ndipo linkafotokoza mmene zinthu zinalengedwera komanso zimene zinachitikira Aisiraeli. Buku lina lomwe ndinawerenga ndi la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. * Bukuli linandichititsa chidwi chifukwa linkafotokoza mfundo za m’Baibulo momveka bwino. Ndinatenga bukuli pamene ndinkapita ku Spain mu 1991 ndipo ndinaliwerenga kambirimbiri. Ndinapeza mfundo zogwira mtima komanso zokhala ndi umboni wosatsutsika zothandiza munthu kukhala ndi chikhulupiriro.

Mfundo yomwe inandichititsa chidwi kwambiri ndi lonjezo la m’Baibulo lakuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Ndinaona kuti mfundo imeneyi ndi yomveka. Komabe pa nthawiyi n’kuti ndisanakumane ndi wa Mboni aliyense. Koma ndinali nditatsimikiza mtima kuti ndikadzakumana nawo, ndidzawapempha kuti azindiphunzitsa Baibulo.

Ndiye munakumana bwanji ndi a Mboni za Yehova?

Patapita masiku angapo, ndinaona azimayi awiri atanyamula Mabaibulo m’manja. Zimene ankachita zinkagwirizana ndi zomwe ndinawerenga m’buku lija. Iwo ankalalikira ngati mmene Akhristu akale ankachitira. Posakhalitsa ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Masiku ano ndimasangalala kwambiri kuthandiza anthu ena kuphunzira za Mlengi wathu.

Popeza poyamba simunkakhulupirira Mulungu, n’chiyani chinakupangitsani kusintha maganizo?

Nyimbo ndi zimene zinandithandiza. Chifukwa, mosiyana ndi zinyama, pafupifupi munthu aliyense amasangalala ndi nyimbo. Munthu akhoza kuimba nyimbo yosonyeza mulimonse mmene akumvera mumtima mwake. Mwachitsanzo, ikhoza kusonyeza kuti wasangalala kapena wakhumudwa. Mwachibadwa timafuna kuvina tikamva kugunda kwa nyimbo. Koma kodi nyimbo ndi zofunika kuti tipitirize kukhala ndi moyo? Popeza anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina amanena kuti zamoyo zamphamvu n’zokhazo zimene zimapitiriza kukhala ndi moyo, kodi tingati nyimbo zimatithandiza kukhala ndi mphamvu? Ndikukayika. Ndimaona kuti n’zosamveka kunena kuti ubongo wa munthu, womwe umatha kupeka nyimbo komanso kudziwa kuti nyimbo iyi ndi yokoma, unangosanduka kuchokera ku zinthu zina. Mfundo yomveka bwino pamenepa ndi yakuti, ubongo wathu unachita kulengedwa ndi Mulungu, yemwe ndi wanzeru komanso wachikondi.

Baibulo lili ngati nyimbo yokoma, yopekedwa mwaluso, yomwe ili ndi uthenga wofunika wopita kwa anthu onse

Kodi n’chiyani chinakuthandizani kukhulupirira zoti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu?

M’Baibulo muli mabuku ang’onoang’ono okwana 66 olembedwa ndi anthu 40 ndipo panatenga zaka 1,600 kuti mabuku onsewa alembedwe. Choncho ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anatsogolera polemba Baibulo kuti nkhani zake zikhale zogwirizana?’ Yankho lomveka limene ndinkapeza linali lakuti, Mulungu ndi amene anatsogolera polemba Baibulo. M’maganizo mwanga ndimaona kuti Baibulo lili ngati nyimbo yokoma, yopekedwa mwaluso, yomwe ili ndi uthenga wofunika wopita kwa anthu onse.

^ ndime 15 Masiku ano a Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mukhoza kupeza bukuli pa webusaiti ya www.pr418.com.