Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KUCHEZA NDI | FAN YU

Katswiri Wopanga Mapulogalamu a Pakompyuta Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri Wopanga Mapulogalamu a Pakompyuta Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

A FAN YU anayamba maphunziro a masamu payunivesite ina mumzinda wa Beijing ku China. Pa nthawiyo sankakhulupirira zoti kuli Mulungu komanso ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma panopa a Fan Yu amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa ndi Mulungu. Olemba Galamukani! anacheza nawo kuti adziwe zimene amakhulupirira ndipo umu ndi mmene anachezera nawo.

Mungatiuzeko za moyo wanu?

Ndinabadwa m’chaka cha 1959 mumzinda wa Fuzhou womwe uli m’chigawo cha Jiangxi ku China. Pamene ndinkakwanitsa zaka 8, n’kuti zinthu m’dziko lathu zitasintha kwambiri pa nkhani zandale. Bambo anga anali katswiri wa zomangamanga ndipo nthawi ina anauzidwa kuti akamange njanji kudera lina lakutali, kuchipululu. Tinkangoonana nawo kamodzi pa chaka. Kwa nthawi yonseyi ndinkakhala ndi mayi anga omwe ankaphunzitsa papulayimale ina ndipo tinkakhala pasukulu pomwepo. Mu 1970, tinasamukira ku Liufang. Mudziwu unali m’boma la Linchuan ndipo unali wosauka kwambiri moti tinkavutika kupeza chakudya.

Banja lanu linali la chipembedzo chanji?

Bambo anga sanali m’chipembedzo chilichonse komanso analibe chidwi ndi nkhani zandale koma mayi anga anali achipembedzo Chachibuda. Kusukulu tinkaphunzitsidwa kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina ndipo ndinkazikhulupirira kwambiri.

N’chifukwa chiyani munayamba kukonda masamu?

Ndinayamba kukonda masamu chifukwa choti amakuchititsa kuganiza kwambiri komanso kufufuza mayankho pogwiritsa ntchito umboni. Mu 1976 ndinapita kuyunivesite ndipo n’kuti a Mao Tse-tung, omwe anali mtsogoleri wa dziko la China atangomwalira kumene. Nditapita kuyunivesite ndinasankha kuphunzira kwambiri zamasamu. Nditalandira digirii, ntchito yanga yoyamba inali yofufuza mmene mphamvu za maatomu zimagwirira ntchito ndipo ntchito imeneyi inkafunika munthu wodziwa zamasamu.

Kodi munamva bwanji mutawerenga Baibulo kwa nthawi yoyamba?

Mu 1987 ndinapita ku United States kuti ndikapeze digirii yapamwamba payunivesite ina ya ku Texas. Ndinkadziwa kuti anthu ambiri a ku America amakhulupirira Mulungu komanso amawerenga Baibulo. Ndinkamvanso kuti m’Baibulo muli nkhani zothandiza moti ndinaganiza zoliwerenga.

Nditaliwerenga kwa nthawi yoyamba ndinkaona kuti zomwe ndinkawerengazo zikumveka zothandiza. Koma kenako ndinasiya kuliwerenga nditaona kuti sindikumvetsa mfundo zina.

Ndiye n’chiyani chinakuchititsani kuti muyambirenso kuwerenga Baibulo?

Ndinali ndisanamvepo zoti kuli mlengi moti ndinaganiza zoyamba kufufuza pandekha za nkhaniyi

Mu 1990, mayi wina wa Mboni za Yehova anafika panyumba yathu n’kundionetsa malemba a m’Baibulo osonyeza mmene moyo udzakhalire m’tsogolo. Mayiyu anapempha banja lina kuti lizidzandiphunzitsa Baibulo. Kenako mkazi wanga Liping, anayambanso kuphunzira Baibulo. Liping ankaphunzitsa sayansi pasukulu ina ya sekondale ku China ndipo nayenso sankakhulupirira zoti kuli Mulungu. Pamene tinkaphunzira Baibulo, tinaphunzira mmene moyo unayambira. Ndinali ndisanamvepo zoti kuli mlengi moti ndinaganiza zoyamba kufufuza pandekha za nkhaniyi.

Ndiye munafufuza bwanji?

Chifukwa choti ndinaphunzira masamu, ndinazolowera kufufuza umboni wosonyeza mmene zinthu zimachitikira. Ndinali nditaphunziranso mfundo yoti zamoyo sizingakhalepo zokha popanda mapulotini. Popeza asayansi ena amanena kuti mapulotiniwo anangopangika paokha, ndinkadabwa kuti zimenezi zingatheke bwanji. Mapulotini anapangidwa mogometsa kwambiri. Maselo a zinthu zamoyo amakhala ndi mapulotini a mitundu yosiyanasiyana ndipo pulotini iliyonse imagwira ntchito inayake yapadera. Mofanana ndi akatswiri ena asayansi, ndinazindikira kuti mapulotini sangapangike paokha ngakhale zitavuta bwanji. Pa mabuku onse onena zoti zamoyo zinachita kusintha, sindinawerengepo buku lililonse lomwe limafotokoza momveka bwino kuti mapulotini angapangike bwanji okha. Chifukwa cha zimenezi, ndinangoona kuti zoona zake n’zoti pali winawake amene anazilenga.

N’chiyani chinakuchititsani kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?

Pamene ndinkaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, ndinadziwa kuti m’Baibulo muli maulosi ndipo ena anakwaniritsidwa. Ndinayambanso kuona kuti mfundo za m’Baibulo zomwe ndinkaphunzira zinkandithandiza. Nthawi zina ndinkadzifunsa kuti: ‘Zinatheka bwanji kuti anthu amene analemba Baibulo kalekale alembe zinthu zomwe ndi zothandizabe masiku ano?’ Choncho ndinazindikira kuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu.

Nanga panopo n’chiyani chimakuchititsanibe kutsimikiza zoti kuli Mlengi?

Ndikaona zinthu zambiri za m’chilengedwechi, ndimatsimikiza kuti pali winawake amene anazilenga. Panopa ndimapanga mapulogalamu a pakompyuta ndipo nthawi zambiri ndimagoma ndi mmene ubongo wathu umagwirira ntchito. Mwachitsanzo, ubongo wathu umatha kudziwa mawu a munthu m’njira yodabwitsa kwambiri. Anthufe timatha kudziwa zimene munthu wina akutanthauza ngakhale atakhala kuti sanamalizitse zimene akulankhula komanso akachita zinthu zina monga kuseka, kutsokomola kapenanso kuchita chibwibwi. Timathanso kumva zimene munthu akulankhula ngakhale patakhala zinthu zosokoneza ngati phokoso kapena kulira kwa foni. Timadziwanso kumene munthu amachokera chifukwa cha mmene akulankhulira. Mwina mukhoza kuganiza kuti zimenezi si zodabwitsa. Koma akatswiri opanga mapulogalamu a pakompyuta akulephera kukonza pulogalamu yoti izitha kuchita zinthu ngati zimenezi. Ngakhale kompyuta yapamwamba kwambiri imene imatha kuzindikira mawu a munthu singathe kuchita zinthu ngati mmene ubongo umachitira.

Anthufe tikamva mawu a munthu winawake, ubongo wathu umatha kuzindikira munthu amene akulankhulayo, mmene akumvera mumtima komanso kuzindikira dera limene munthuyo amachokera chifukwa cha mmene akutchulira mawuwo. Akatswiri opanga mapulogalamu a pakompyuta akuchita kafukufuku wofuna kudziwa mmene angapangire makompyuta amene angamazindikire mawu, ngati mmene ubongo wa munthu umachitira. Pamenepatu akatswiriwa sakudziwa kuti akungofufuza zinthu zodabwitsa zimene Mulungu anapanga kale.