Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba

Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba

“Ndinayamba kumangokhumudwa popanda chifukwa chenicheni. Zimenezi zinkandiliritsa chifukwa ndinkangoona ngati ndikupenga.”—Anatero Rondro, * yemwe ali ndi zaka 50.

“Ndikamadzuka m’mawa katundu ankakhala ali mbwee. Zinkandivuta kuti ndipeze pamene ndasiya zinthu. Zinthu zimene sindinkavutika kuchita m’mbuyo monsemu zinayamba kundivuta ndipo sindinkadziwa kuti zimenezi zikuchitika chifukwa chiyani.”—Anatero Hanta, yemwe ali ndi zaka 55.

AZIMAYI amenewa sikuti ankadwala koma anali atafika msinkhu wosiya kusamba. Zimenezi ndi zachibadwa ndipo zimachitikira mkazi aliyense akafika msinkhu woti sangaberekenso. Ngati ndinu mzimayi, kodi mwatsala pang’ono kufika msinkhu umenewu kapena munafika kale? Kaya muli msinkhu uti, mukhoza kupirira mavuto amene amabwera munthu akamasiya kusamba ngati inuyo komanso mwamuna wanu mutadziwa zimene mungachite.

Zinthu Zimasintha

Madokotala amanena kuti ngati mzimayi wadumpha miyezi 12 osasamba ndiye kuti wafika msinkhu wosiya kusamba. Azimayi ambiri amayamba kusiya kusamba akakwanitsa zaka 40, pomwe ena amayamba akakwanitsa zaka 60.

Nthawi zambiri mzimayi amasiya kusamba pang’onopang’ono. Chifukwa cha kusintha kwadzidzidzi kumene kumachitika m’thupi mwake, mzimayi akhoza kudumphitsa mwezi osasamba, kuyamba kusamba pa nthawi yosiyana ndi nthawi zonse, kapena kutaya magazi ambiri pa nthawi yosamba. Koma azimayi ena amasiya kusamba kamodzin’kamodzi.

Buku lina linati: “Zimene zimachitikira mzimayi akamasiya kusamba sizimakhala zofanana kwa mzimayi aliyense. Koma azimayi ambiri amene akusiya kusamba amamva kutentha, ndipo nthawi zambiri pambuyo pake amamvanso kuzizira kwambiri.” (Menopause Guidebook) Zimenezi zimapangitsa kuti azivutika kugona komanso azifooka. Koma kodi zimenezi zimachitika kwa nthawi yaitali bwanji? Buku lina linanena kuti “azimayi ena amamva zimenezi  kwa chaka chimodzi kapena ziwiri ndipo zimawachitikira pa nthawi imene akuyamba kusiya kusamba. Ena amavutika ndi zimenezi kwa zaka zambiri, koma ndi ochepa omwe zimawachitikira kwa moyo wawo wonse.” *The Menopause Book.

Chifukwa cha kusintha kumene kumachitika m’thupi, azimayi ena amakhumudwakhumudwa, zomwe zimachititsa kuti azilira, aziiwalaiwala, komanso azilephera kuchita chinthu chimodzi kwa nthawi yaitali. Buku lija linanenanso kuti: “Sikuti mzimayi aliyense amavutika ndi zinthu zonsezi.” (The Menopause Book) Pali azimayi ena omwe savutika n’komwe ndi zimenezi, kapena amangovutika pang’ono.

Zimene Zingakuthandizeni

Kusintha zinthu zina kukhoza kukuthandizani kuti musamavutike kwambiri. Mwachitsanzo, anthu amene amasuta fodya angachite bwino kusiyiratu kusutako n’cholinga choti asamamve kutentha. Azimayi ambiri amasiya kumwa mowa, kudya zatsabola, kapena zotsekemera, chifukwa zakudya zimenezi n’zimene zimachititsa kuti azimva kutentha. Komabe ndi bwino kumadya zakudya zopatsa thanzi komanso zakasinthasintha.

Kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandizenso kuchepetsa mavuto omwe azimayi amsinkhu umenewu amakumana nawo. Mwachitsanzo, kungathandize kuti munthu asamavutike kugona, asamakhumudwekhumudwe, azikhala ndi mafupa olimba komanso azikhala ndi thanzi labwino. *

Muzimasuka Kufotokoza Mavuto Anu

Rondro, yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Palibe chifukwa chobisira mavuto omwe mukukumana nawo. Mukamafotokoza mavuto anu momasuka kwa abale anu, sangadandaule kwambiri akaona zimenezi zikukuchitikirani.” Ndipotu, akhoza kumakumvetsani kwambiri. Lemba la 1 Akorinto 13:4 limati: “Chikondi n’choleza mtima.”

Azimayi ena amaonanso kuti pemphero limawathandiza kwambiri ndipo pemphero ndi lothandizanso kwa azimayi omwe amadandaula chifukwa choona kuti sangaberekenso. Baibulo limatitsimikizira kuti: “[Mulungu] amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:4) Mfundo inanso yolimbikitsa ndi yakuti vuto losiya kusamba lidzatha. Vutoli likadzatha, azimayi onse adzakhala ndi thanzi labwino komanso azidzasangalala kwa zaka zambirimbiri.

^ ndime 2 Mayina asinthidwa.

^ ndime 8 Matenda ena, monga chithokomiro komanso mankhwala ena angachititsenso kuti azimayi azimva kutentha. Ngati mumamva kutentha ndi bwino kutsimikizira kaye kuti simukumva kutenthako chifukwa cha zinthu zimenezi m’malo mofulumira kuganiza kuti mukuyamba kusiya kusamba.

^ ndime 12 Pofuna kuthandiza anthu amene ali ndi mavuto osiyanasiyana obwera chifukwa cha kusiya kusamba, madokotala amatha kuwapatsa mankhwala oti asamakhumudwekhumudwe komanso akhoza kuwalangiza zinthu zoyenera kudya. Magazini ya Galamukani! siisankhira anthu mankhwala.