Wolembedwa na Mateyo 10:1-42

  • Atumwi 12 (1-4)

  • Malangizo a ulaliki (5-15)

  • Ophunzila a Yesu adzazunzidwa (16-25)

  • Opani Mulungu osati anthu (26-31)

  • Lupanga osati mtendele (32-39)

  • Kulandila ophunzila a Yesu (40-42)

10  Conco, anaitana ophunzila ake 12 na kuwapatsa ulamulilo pa mizimu yonyansa, kuti aziitulutsa komanso kuti azicilitsa anthu matenda a mtundu uliwonse na zofooka zilizonse.  Maina a atumwi 12 amenewo ni awa: Simoni wochedwanso Petulo, na Andireya m’bale wake; Yakobo mwana wa Zebedayo na Yohane m’bale wake;  Filipo na Batulomeyo; Thomasi na Mateyo wokhometsa misonkho; Yakobo mwana wa Alifeyo; Tadeyo;  Simoni Kananiya;* na Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapeleka Yesu.  Yesu anatumiza amuna 12 amenewa na kuwapatsa malangizo akuti: “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina. Komanso musaloŵe mu mzinda uliwonse wa Asamariya.  M’malo mwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosocela za nyumba ya Isiraeli.  Pamene mukupita, muzilalikila kuti: ‘Ufumu wa kumwamba wayandikila.’  Cilitsani odwala, ukitsani akufa, yeletsani akhate, tulutsani ziŵanda. Munalandila kwaulele, pelekani kwaulele.  Musanyamule golide kapena siliva kapena kopa m’zikwama zanu za ndalama. 10  Musanyamulenso cola ca zakudya za paulendo kapena zovala ziŵili,* kapena nsapato, kapenanso ndodo, pakuti wanchito ayenela kulandila cakudya cake. 11  “Mukaloŵa mu mzinda kapena m’mudzi uliwonse, funa-funani mmenemo amene ali woyenelela, ndipo mukhalebe mmenemo mpaka nthawi yocoka. 12  Mukaloŵa m’nyumba, pelekani moni kwa a m’nyumbayo. 13  Ngati nyumbayo ni yoyenelela, mtendele umene mukuifunila ukhale pa iyo. Koma ngati si yoyenelela, mtendele wanu mubwelele nawo. 14  Kulikonse kumene munthu sakakulandilani kapena kumvetsela mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mu mzinda umenewo, kutumulani fumbi ku mapazi anu. 15  Ndithu nikukuuzani kuti pa Tsiku la Ciweluzo, cilango ca Sodomu na Gomora cidzakhala cocepelako poyelekezela na ca mzinda umenewo. 16  “Tamvelani! Nikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Conco khalani ocenjela ngati njoka, koma oona mtima ngati nkhunda. 17  Samalani na anthu cifukwa adzakupelekani ku makhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge awo. 18  Ndiponso adzakupelekani kwa abwanamkubwa na mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo komanso kwa anthu a mitundu ina. 19  Komabe akakupelekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukakambile kapena zimene mukakambe, cifukwa zimene mukakambe mudzapatsidwa nthawi yomweyo. 20  Pakuti amene adzakamba si inuyo panokha ayi, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzela mwa inu. 21  Komanso m’bale adzapeleka m’bale wake kuti aphedwe, tate adzapeleka mwana wake, ndipo ana adzaukila makolo awo n’kuwapeleka kuti aphedwe. 22  Anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile* mpaka mapeto adzapulumuka. 23  Akakuzunzani mu mzinda wina, thaŵilani ku mzinda wina. Ndithu nikukuuzani kuti Mwana wa munthu adzafika musanatsilize kuzungulila mizinda yonse ya Isiraeli. 24  “Wophunzila saposa mphunzitsi wake, ndipo kapolo saposa mbuye wake. 25  N’zokwanila kwa wophunzila kukhala ngati mphunzitsi wake, komanso kwa kapolo kukhala ngati mbuye wake. Ngati anthu akucha mutu wa banja kuti Belezebule,* kuli bwanji a m’banja lake? Kodi sadzawacha maina oipa kuposa pamenepa? 26  Conco musawaope, pakuti palibe cobisika cimene sicidzaoneka. Ndipo palibe cinsinsi cimene sicidzadziŵika. 27  Zimene nakuuzilani mu mdima, zikambeni poyela. Ndipo mawu oŵeleŵesa amene mwamva, alalikileni pa mitenje ya nyumba. 28  Musamaope amene amapha thupi koma sangaphe moyo.* M’malo mwake, muziopa amene angathe kuwononga zonse ziŵili, moyo na thupi lomwe mu Gehena.* 29  Mpheta ziŵili amazigulitsa kakhobili kamodzi kocepa mphamvu, si conco kodi? Koma palibe ngakhale imodzi imene ingagwe pansi Atate wanu osadziŵa. 30  Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu amaliŵelenga lonse. 31  Conco musaope; ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili. 32  “Aliyense wonivomela pamaso pa anthu, inenso nidzamuvomela pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba. 33  Koma aliyense wonikana pamaso pa anthu, inenso nidzamukana pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba. 34  Musaganize kuti n’nabweletsa mtendele pa dziko lapansi. Sin’nabweletse mtendele koma lupanga. 35  Pakuti n’nabwela kudzacititsa magaŵano pakati pa mwana wamwamuna na atate ake, mwana wamkazi na amayi ake, komanso mkazi wokwatiwa na apongozi ake aakazi. 36  Kukamba zoona, adani a munthu adzakhala anthu a m’banja lake lomwe. 37  Munthu aliyense wokonda kwambili atate ake kapena amayi ake kuposa ine, si woyenela ine. Ndipo aliyense wokonda kwambili mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi kuposa ine, si woyenela ine. 38  Ndiponso aliyense wosalandila mtengo wake wozunzikilapo* na kunitsatila, si woyenela ine. 39  Aliyense woyesa kupulumutsa moyo wake adzautaya, ndipo aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza. 40  “Munthu aliyense amene wakulandilani, walandilanso ine, ndipo aliyense amene walandila ine, walandilanso Iye amene ananituma. 41  Munthu aliyense wolandila mneneli poona kuti ni mneneli, adzalandila mphoto ya mneneli. Ndipo aliyense wolandila munthu wolungama poona kuti ni munthu wolungama, adzalandila mphoto ya munthu wolungama. 42  Aliyense wopatsa mmodzi wa ana aang’ono awa ngakhale kapu cabe ya madzi ozizila kuti amwe cifukwa ni wophunzila wanga, ndithu nikukuuzani kuti mphoto yake siidzatayika ngakhale pang’ono.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “wokangalika.”
Kapena kuti, “covala cosinthila.”
Kapena kuti, “amene wapilila.”
Dzina la Satana, kalonga, kapena kuti wolamulila wa ziŵanda.
Kutanthauza ciyembekezo codzakhalanso na moyo m’tsogolo.