Wolembedwa na Mateyo 24:1-51

  • CIZINDIKILO CA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-51)

    • Nkhondo, njala, zivomezi (7)

    • Uthenga wabwino udzalalikidwa (14)

    • Cisautso cacikulu (21, 22)

    • Cizindikilo ca Mwana wa munthu (30)

    • Mtengo wa mkuyu (32-34)

    • Mofanana na masiku a Nowa (37-39)

    • Khalanibe maso (42-44)

    • Kapolo wokhulupilika na woipa (45-51)

24  Tsopano pamene Yesu anali kucoka pa kacisi, ophunzila ake anafika kwa iye kuti amuonetse zimango za pa kacisipo.  Iye anawauza kuti: “Kodi mukuziona zinthu zonsezi? Ndithu nikukuuzani kuti, pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”  Iye atakhala pansi mu Phili la Maolivi, ophunzila ake anamufikila mwamseli n’kumufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, nanga cizindikilo ca kukhalapo* kwanu komanso ca cimalizilo ca nthawi ino* cidzakhala ciyani?”  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni,  cifukwa ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili.  Mudzamva phokoso la nkhondo komanso mbili za nkhondo. Zimenezi zisadzakucititseni mantha. Pakuti ziyenela kucitika koma mapeto adzakhala asanafikebe.  “Mtundu udzaukilana na mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina, komanso kudzakhala njala na zivomezi m’malo osiyana-siyana.  Zinthu zonsezi ni ciyambi ca masautso.*  “Ndiyeno anthu adzakupelekani kuti mukazunzidwe ndipo adzakuphani. Ndiponso mitundu yonse idzakudani cifukwa ca dzina langa. 10  Cina, anthu ambili adzapunthwa ndipo adzapelekana na kudana. 11  Kudzabwela aneneli ambili onyenga ndipo adzasoceletsa anthu ambili. 12  Ndiponso cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzacepa. 13  Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka. 14  Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti udzakhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika. 15  “Cotelo, mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko, cimene mneneli Danieli ananena, citaimilila pa malo oyela (woŵelenga adzazindikile). 16  Amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila ku mapili. 17  Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kuti akatenge katundu m’nyumba mwake. 18  Ndipo munthu amene adzakhale ku munda asadzabwelele kuti akatenge covala cake cakunja. 19  Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! 20  Pitilizani kupemphela kuti musadzathaŵe m’nyengo yozizila kapena pa tsiku la Sabata. 21  Cifukwa panthawiyo kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka pano, ndipo sicidzacitikanso. 22  Kukamba zoona masikuwa akanapanda kucepetsedwa, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwawo masikuwo adzacepetsedwa. 23  “Cotelo munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Ali uko!’ musakakhulupilile. 24  Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli onyenga. Ndipo adzacita zizindikilo zamphamvu na zodabwitsa kuti asoceletse anthu, ndipo ngati n’kotheka ngakhale osankhidwawo. 25  Onani! Ine nakucenjezelanitu. 26  Conco, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu! Iye ali ku cipululu,’ musakapiteko. Akadzanena kuti ‘Ali m’zipinda zamkati,’ musadzakhulupilile. 27  Pakuti monga mmene mphenzi imang’animila kucokela kum’maŵa mpaka kumadzulo, ni mmenenso zidzakhalile na kukhalapo* kwa Mwana wa munthu. 28  Kulikonse kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zimasonkhana kumeneko. 29  “Cisautso ca m’masiku amenewo cikadzangotha, dzuŵa lidzacita mdima ndipo mwezi sudzawala. Nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 30  Kenako cizindikilo ca Mwana wa munthu cidzaonekela kumwamba. Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni. Iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela pa mitambo ya kumwamba ali na mphamvu komanso ulemelelo waukulu. 31  Iye adzatumiza angelo ake na kulila kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinayi. Kucokela kumalekezelo a mlengalenga mpaka kumalekezelo ake ena. 32  “Tsopano phunzilam’poni kanthu pa fanizo ili la mtengo wa mkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka na kutulutsa masamba, mumadziŵa kuti dzinja layandikila. 33  Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zonsezi mudzadziŵe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni. 34  Ndithu nikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha wonse, mpaka utaona zinthu zonsezi zitacitika. 35  Kumwamba na dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi. 36  “Ponena za tsikulo na ola lake palibe amene adziŵa. Ngakhale angelo a kumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi. 37  Pakuti monga zinalili m’masiku a Nowa, ni mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo* kwa Mwana wa munthu. 38  M’masiku amenewo Cigumula cisanacitike anthu anali kudya na kumwa, amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’Cingalawa. 39  Anthuwa ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka Cigumula cinafika n’kuwakokolola onsewo. Umu ni mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo kwa Mwana wa munthu. 40  Pa nthawiyo amuna aŵili adzakhala m’munda, ndipo mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa. 41  Akazi aŵili adzakhala akupela pa mphelo. Mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa. 42  Conco khalani maso cifukwa simukudziŵa tsiku limene Mbuye wanu adzabwela. 43  “Koma dziŵani ici: Ngati mwininyumba angadziŵe nthawi imene mbala ikubwela usiku,* angakhalebe maso ndipo sangalole kuti mbalayo ithyole n’kuloŵa m’nyumba mwake. 44  Mwa ici, inunso khalani wokonzeka cifukwa Mwana wa munthu adzabwela pa ola limene inu simukuliganizila. 45  “Ndani maka-maka amene ali kapolo wokhulupilika ndiponso wanzelu, amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake a pakhomo, na kuwapatsa cakudya cawo pa nthawi yoyenela? 46  Kapoloyo adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwela adzamupeza akucita zimenezo! 47  Ndithu nikukuuzani kuti adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse. 48  “Koma ngati kapolo woipayo mumtima mwake anganene kuti, ‘Mbuye wanga akucedwa,’ 49  n’kuyamba kumenya akapolo anzake, ndiponso kudya na kumwa pamodzi na zidakwa zenizeni, 50  mbuye wa kapoloyo adzabwela pa tsiku limene iye sakuliyembekezela, komanso pa ola limene sakulidziŵa. 51  Pamenepo adzamupatsa cilango coŵaŵa kwambili, ndipo adzamuponya ku malo a anthu onyenga. Kumeneko azikalila na kukuta mano.

Mawu a m'Munsi

Mawu ake enieni, “zoŵaŵa za pobeleka.”
Kapena kuti, “amene wapilila.”
Kapena kuti, “akanadziŵa kuti mbala ibwela pa ulonda uti.”