Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinasangalala Ndi Mayankho Omveka Bwino a m’Baibulo

Ndinasangalala Ndi Mayankho Omveka Bwino a m’Baibulo
  • CAKA COBADWA: 1948

  • DZIKO: HUNGARY

  • MBILI YANGA: NDINALI KUFUNITSITSA KUDZIŴA MAYANKHO A MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI

KUKULA KWANGA:

Ndinabadwila ku Hungary, mumzinda wa Székesfehérvár, umene wakhalapo kwa zaka zoposa 1,000. Ndimamva cisoni ndikaganizila zinthu zambili zimene zinaonongeka cifukwa ca nkhondo yaciŵili ya padziko lonse.

Pamene ndinali mwana, ndinali kukhala ndi ambuye anga. Ndinali kuwakonda kwambili ambuye anga makamaka aakazi, a Elisabeth. Iwo anandithandiza kuti ndizikhulupilila kwambili Mulungu. Kuyambila pamene ndinali ndi zaka zitatu, madzulo alionse ndinali kupemphela nao limodzi pemphelo limene ena amalicha Pemphelo la Ambuye. Komabe, sindinali kudziŵa tanthauzo la pemphelo limeneli mpaka nditakwanitsa zaka 20.

Pamene ndinali mwana ndinali kusamalidwa ndi ambuye anga cifukwa cakuti makolo anga anali kuseŵenza masana ndi usiku kuti apeze ndalama zakuti adzagulile nyumba yabwino. Koma pa Ciwelu caciŵili mwezi ulionse, tonse tinali kudyela pamodzi cakudya monga banja. Ndinali kusangalala kwambili pa nthawi imene tinali kudyela pamodzi.

Mu 1958, makolo anga anakwanitsa zimene anali kufuna. Iwo anagula nyumba kuti tonse atatu tizikhalamo. Conco ndinayamba kukhala ndi makolo anga, ndipo ndinakondwela kwambili. Komabe, patangopita miyezi 6, zinthu zinasintha. Atate anga anamwalila ndi matenda a kansa.

Ndinasokonezeka maganizo kwambili. Nthawi ina ndinapemphela kuti: “Mulungu, ndinakupemphani kuti muwacilitse atate. Ndikuwafuna. N’cifukwa ciani simunayankhe mapemphelo anga?” Ndinali kufunitsitsa kudziŵa kumene atate anali. Ndinali kudzifunsa kuti: ‘Kodi apita kumwamba? Kodi sindidzawaonanso?’ Ndinali kukhumbila ana ena amene anali ndi atate ao.

Kwa zaka zambili, ndinali kupita kumanda pafupifupi tsiku lililonse. Ndinali kugwada pamanda a atate anga ndi kupemphela kuti: “Conde Mulungu, ndiuzeni kumene kuli atate.” Komanso ndinali kupemphela kuti andithandize kudziŵa colinga ca moyo.

Pamene ndinali ndi zaka 13, ndinaganiza zophunzila Cijelemani. Ndinali kuganiza kuti ndingapeze mayankho a mafunso anga m’mabuku oculuka a Cijelemani amene amafotokoza zinthu mozama. Mu 1967, ndinayamba kuphunzila cinenelo cimeneci mumzinda wa Jena, umene unali mbali ya East Germany. Ndinali kuŵelenga kwambili mabuku olembedwa ndi akatswili a ku Germany a nzelu za anthu, makamaka amene amafotokoza cifukwa cake anthufe tinakhalapo. Ngakhale kuti ndinapeza mfundo zina zosangalatsa, sindinakhutile. Conco, ndinapitiliza kupemphela kuti ndipeze mayankho okhutilitsa.

MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:

Mu 1970, ndinabwelela ku Hungary, ndipo kumeneko ndinakumana ndi Rose amene anadzakhala mkazi wanga. Panthawiyo, dziko la Hungary linali kulamulidwa ndi boma la Cikomyunizimu. Patapita nthawi yocepa kucokela pamene tinakwatilana, ine ndi mkazi wanga tinathawila ku Austria. Colinga cathu cinali cakuti tidzapite ku Sydney, m’dziko la Australia, kumene amalume anali kukhala.

Patapita nthawi yocepa ndili ku Austria, ndinapeza nchito. Tsiku lina, munthu amene ndinali kugwila naye nchito anandiuza kuti ndingapeze mayankho a mafunso anga onse m’Baibulo. Iye anandipatsa mabuku angapo ofotokoza Baibulo. Ndinaŵelenga mabuku onsewo m’kanthawi kocepa cabe, ndipo ndinafuna kudziŵa zambili. Motelo ndinalembela kalata a Mboni za Yehova, amene anali kufalitsa mabukuwo, kuti anditumizile mabuku ena.

Pa tsiku loyamba lokumbukila cikwati cathu, kunyumba kwathu kunabwela mnyamata wa Mboni. Iye anabweletsa mabuku amene ndinapempha ndi kundipempha kuti tiziphunzila Baibulo, ndipo ndinavomela. Popeza kuti ndinali kufunitsitsa kuphunzila, tinali kuphunzila kaŵili pamlungu, ndipo phunzilo lililonse linali kutenga maola pafupifupi anai.

Ndinasangalala ndi mfundo za m’Baibulo zimene a Mboni anali kundiphunzitsa. Ndinadabwa kwambili pamene io anandionetsa dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo langa la Cihangare. Pa zaka zonse 27 zimene ndinali kupita kuchalichi, sindinamveko dzina la Mulungu ngakhale kamodzi. Ndinasangalala ndi mayankho omveka bwino a m’Baibulo. Mwacitsanzo, ndinaphunzila kuti akufa sadziŵa ciliconse. Iwo amakhala ngati ali mtulo tofa nato. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:11-15) Ndinaphunzilanso zimene Baibulo limalonjeza zakuti m’dziko latsopano “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndikuyembekezela kudzaonananso ndi atate anga, cifukwa cakuti m’dziko latsopano, ‘mudzakhala kuuka.’—Machitidwe 24:15.

Mkazi wanga, Rose, nayenso anali wofunitsitsa kuphunzila Baibulo. Conco, tinayamba kuphunzilila pamodzi. Tinapita patsogolo mwamsanga, cakuti tinatsiliza kuphunzila buku lophunzilila m’miyezi iŵili cabe. Komanso tinali kupezeka pa misonkhano yonse ya Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu. Tinakondwela kwambili ndi makhalidwe a Mboni za Yehova monga cikondi, mgwilizano ndiponso kudzipeleka kwao pothandiza ena.—Yohane 13:34, 35.

Mu 1976, ine ndi mkazi wanga anatilola kuloŵa m’dziko la Australia. Titangofika kumeneko, tinafufuza kumene kunali a Mboni za Yehova. Titawapeza, io anatilandila ndi manja aŵili. Mu 1978, tinakhala a Mboni za Yehova.

MAPINDU AMENE NDAPEZA:

Ndinapeza mayankho a mafunso amene anali kundivutitsa kwa nthawi yaitali. Mwa kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, ndapeza Atate wabwino koposa. (Yakobo 4:8) Ndipo ndimasangalala kwambili ndi ciyembekezo codzaonananso ndi atate anga m’dziko latsopano.—Yohane 5:28, 29.

Mu 1989, ine ndi mkazi wanga tinaganiza zobwelela ku Hungary kuti tikauzeko mabwenzi, acibale ndiponso anthu ena zimene tinali kukhulupilila. Takhala ndi mwai wophunzitsa Baibulo anthu ambilimbili. Ndipo anthu oposa 70 mwa anthu amenewa anayamba kutumikila Yehova, kuphatikizapo amai anga okondedwa.

Kwa zaka 17, ndinali kupemphela kuti ndipeze mayankho a mafunso anga. Tsopano papita zaka zina 39, ndipo sindinasiye kupemphela. Koma masiku ano popemphela ndimanena kuti, “Zikomo kwambili Atate wanga wakumwamba cifukwa coyankha mafunso amene ndinali nao pamene ndinali mwana.”