Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

TSANZILANI CIKHULUPILILO CAO | YOSEFE

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”

YOSEFE anali kuyenda m’kanjila ka mkati mwandende mmene munali mdima kucokela ku nchito yakalavulagaga imene anali kugwila. Iye anali kutuluka thukuta kwambili moti linali kucita kugwa. Kunja kunali kotentha kwambili cakuti m’ndende munali ngati m’ng’anjo yamoto. Mavuto amenewa anacititsa kuti iye awadziŵe kwambili malo amenewo. Panthawiyo, iye analibenso kwina kopita koma kungokhala m’ndende. N’zoona kuti anthu ena anali kumulemekeza. Koma monga mkaidi, iye anali kukhala movutika ndithu.

Mwacionekele, nthawi zambili iye anali kukumbukila mmene zinthu zinalili pamene anali kupita ku mapili a ku Hebroni kukadyetsa nkhosa za atate ake. Panthawi ina ali ndi zaka pafupifupi 17, atate ake, a Yakobo, anam’tuma kuyenda ulendo wa makilomita ambili kucoka kunyumba kwao. Koma popeza kuti tsopano ali m’ndende, iye alibenso ufulu woyenda. Abale ake anali kumuda kwambili cifukwa ca nsanje cakuti anamugulitsa monga kapolo. Anthu amene anamugula anapita naye ku Iguputo, ndipo kumeneko anayamba kutumikila m’nyumba ya Potifara. Potifara anali kumudalila kwambili Yosefe, koma Yosefe tsopano ali m’ndende cifukwa cakuti mkazi wa Potifara anamunamizila kuti anafuna kumugwililila. *—Genesis caputala 37 ndi 39.

Tsopano Yosefe ali ndi zaka 28, ndipo wakhala m’ndende pafupifupi zaka 10. Kunena mwacidule, umoyo wake sukuyenda bwino ngati mmene anali kuyembekezela. Mwina iye akudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzacoka m’ndende muno? Kodi ndidzawaonanso atate anga okondedwa kapena mng’ono wanga, Benjamini? Kodi ndidzakhala m’ndende muno mpaka liti?’

Kodi inunso munamvapo ngati mmene Yosefe anamvelela? Nthawi zina umoyo umakhala wosiyana kwambili ndi mmene tinali kuganizila pamene tinali acicepele. Ndipo mavuto amangokhala ngati sadzatha moti zimakhala zovuta kupilila. Tiyeni tione zimene tingaphunzilepo pa cikhulupililo ca Yosefe.

“YEHOVA ANAPITILIZABE KUKHALA NDI YOSEFE”

Yosefe anali kudziŵa kuti Mulungu wake, Yehova, sanamuiwale ndipo mwacionekele zimenezi zinamuthandiza kupilila. Ngakhale pamene Yosefe anali m’ndende m’dziko lacilendo, Yehova anali kumudalitsa. Baibulo limati: “Yehova anapitilizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha. Ndipo anacititsa mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.” (Genesis 39:21-23) Cifukwa cakuti Yosefe anali kugwila nchito mwakhama, Mulungu anapitilizabe kumudalitsa. Yosefe ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili cifukwa codziŵa kuti Yehova anali naye nthawi zonse.

Kodi Yehova anafuna kuti Yosefe akhale m’ndende kwa moyo wake wonse? N’zoonekelatu kuti Yosefe sanali kudziŵa yankho lake, koma n’zosakaikitsa kuti iye anali kupemphela kwa Mulungu za nkhaniyi. Monga mmene zimakhalila nthawi zambili, yankho linabwela m’njila yosayembekezeka. Tsiku lina, m’ndendemo munacitika congo pamene anthu aŵili ogwila nchito kwa mfumu Farao anawabweletsa m’ndendemo. Wina anali wopelekela cikho wa mfumu Farao ndipo wina anali wophika mkate.—Genesis 40:1-3.

Mkulu wa asilikali anaika Yosefe kuti azilondela amuna aŵiliwo amene poyamba anali ndi udindo wapamwamba. * Usiku wina, iwo analota maloto odabwitsa. Yosefe atawaona m’mawa, anadziŵa kuti cinacake sicinali bwino. Conco anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciani nkhope zanu zili zacisoni lelo?” (Genesis 40:3-7) Mwina kukoma mtima kwa Yosefe n’kumene kunapangitsa kuti akaidiwo amasuke ndi kumufotokozela mavuto ao. Yosefe sanali kudziŵa kuti zimene amuna amenewo adzamufotokozela zidzasintha kwambili umoyo wake. Ngati Yosefe sakanawasonyeza kukoma mtima, mwina io sakanamufotokozela vuto lao. Zimene Yosefe anacita zingatilimbikitse kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndimakhulupilila Mulungu mwa kudela nkhawa anthu ena?’

Yosefe anali kukomela mtima akaidi anzake ndi kuwacitila ulemu

Akaidiwo anafotokoza kuti anali ndi nkhawa cifukwa cakuti analota maloto odabwitsa, koma panalibe munthu wowamasulila. Aiguputo anali kukhulupilila kwambili maloto, ndipo anali kudalila kwambili anthu amene anali kudzicha omasulila maloto. Amuna aŵiliwo sanadziŵe kuti maloto ao anacokela kwa Yehova, Mulungu wa Yosefe. Koma Yosefe anali kudziŵa. Iye anawauza kuti: “Kodi Mulungu sindiye amamasulila maloto? Tandifotokozelani malotowo.” (Genesis 40:8) Mau amene Yosefe anakamba ndi othandizanso masiku ano kwa anthu onse okonda kuphunzila Baibulo. Mofanana ndi Yosefe, munthu aliyense wokonda kupemphela afunika kukhala wodzicepetsa ndi kudalila Mulungu kuti amvetsetse Mau Ake.—1 Atesalonika 2:13; Yakobo 4:6.

Mkulu wa opelekela cikho ndiye anayamba kufotokozela Yosefe loto lake. Iye anakamba kuti anaona mtengo wa mpesa umene unali ndi nthambi zitatu, ndipo unabeleka mphesa. Kenako mphesazo zinapsa, ndipo wopelekela cikhoyo anazifinyila m’cikho ca Farao. Mothandizidwa ndi Yehova, Yosefe anazindikila mwamsanga tanthauzo la lotolo. Yosefe anauza wopelekela cikho kuti nthambi zitatuzo zinali kuimila masiku atatu. Iye ananena kuti pakapita masiku atatu, Farao adzatulutsa wopelekela cikhoyo ndi kumubwezela pa nchito yake yakale. Pamene nkhope ya wopelekela cikho inaoneka kuti yamasuka, Yosefe anamupempha kuti: “Conde, udzandikomele mtima pondichula kwa Farao.” Kenako Yosefe anafotokoza kuti anacita kumuba kwao, ndiponso kuti anamuika m’ndende popanda colakwa ciliconse.—Genesis 40:9-15.

Mkulu wa ophika mkate ataona kuti Yosefe wamasulila zabwino pa loto la wopelekela cikho, nayenso anapempha Yosefe kuti amasulile loto lake. Mkulu wa ophika mkateyo anakamba kuti anaona mbalame zikudya mkate umene unali munsengwa zitatu zimene zinali pa mutu pake. Mulungu anathandizanso Yosefe kudziŵa tanthauzo la loto limeneli. Koma tanthauzo la loto la mkulu wa ophika mkateyo silinali labwino. Yosefe anati: “Kumasulila kwake ndi uku: Nsengwa zitatuzo zikuimila masiku atatu. Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa n’kukudula mutu. Adzakupacika pamtengo, ndipo mbalame zidzadya nyama yako ndithu.” (Genesis 40:16-19) Mofanana ndi atumiki a Mulungu onse okhulupilika, Yosefe analengeza mauthenga ocokela kwa Mulungu onsewa—uthenga wabwino komanso uthenga waciweluzo.—Yesaya 61:2.

Patapita masiku atatu, zimene Yosefe anakamba zinacitikadi. Farao anacita cikondwelelo cokumbukila kubadwa kwake, comwe atumiki a Mulungu sacita. Pa cikondweleloco, Farao anaweluza atumiki ake aŵiliwo. Iye anapha mkulu wa ophika mkate ndi kubwezela pa nchito mkulu wa wopelekela cikho uja, monga mmene Yosefe anakambila. Koma cifukwa conyalanyaza, mkulu wa opelekela cikho anaiŵala zimene Yosefe anamuuza.—Genesis 40:20-23.

“YEMWE ANENE . . .NDI MULUNGU OSATI INE”

Zaka ziŵili zathunthu zinapita. (Genesis 41:1) Mwacionekele zimenezi zinamufooketsa kwambili Yosefe. Mwina iye anaganiza kuti adzatuluka m’ndendeyo pamene Yehova anamuthandiza kudziŵa tanthauzo la loto la mkulu wa opelekela cikho ndi la mkulu wa ophika mkate. Tsiku lililonse akadzuka m’maŵa, mwina Yosefe anali kuyembekezela kuti atuluka m’ndendemo. Koma masiku anali kungopita, zinthu osasintha. N’zoonekelatu kuti zaka ziŵili zimenezo zinali zovuta kwambili kwa Yosefe kupilila. Koma iye sanasiye kukhulupilila Yehova Mulungu wake. M’malo mokhumudwa, iye apitilizabe kupilila, ndipo anakhalabe wokhulupilika panthawi yovutayi.—Yakobo 1:4.

M’masiku ovuta ano, tonse tifunika kukulitsa mzimu wa kupilila. Tifunika kudalila Mulungu kuti tikhale olimba mtima, oleza mtima, ndiponso kuti tikhalebe ndi mtendele wa m’maganizo pamene tikulimbana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku. Monga mmene Mulungu anathandizila Yosefe, iye angatithandize kuti tisataye mtima koma kuti tikhalebe ndi ciyembekezo colimba.—Aroma 12:12; 15:13.

Ngakhale kuti wopelekela cikho uja anamuiŵala Yosefe, Yehova sanamuiŵale. Usiku wina, Mulungu anacititsa kuti Farao alote maloto aŵili odabwitsa. M’loto loyamba, mfumuyo inaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo, ndipo ng’ombezo zinali zokongola m’maonekedwe ndi zonenepa. Kenako anaonanso ng’ombe zina 7 zonyansa ndi zowonda. Ng’ombe zowondazo zinayamba kudya zonenepa zija. Pambuyo pake, Farao analota loto lina. Iye analota ngala za tirigu 7 zazikulu bwino zikutuluka paphesi limodzi. Kenako anaona ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyambazo. Ngalazo zinali zonyala ndi zowauka, ndipo zinameza ngala 7 zazikulu bwino zija. Kutaca m’mawa, Farao anavutika kwambili maganizo. Cotelo anaitanitsa ansembe onse amatsenga ndi amuna anzelu onse a mu Iguputo kuti amasulile malotowo. Koma onse analephela. (Genesis 41:1-8) Mwina anthuwo anasowelatu conena kapena anali kumasulila zinthu zotsutsana. Mulimonse mmene zinalili, Farao anagwilitsidwa mwala. Komabe, iye anali kufunitsitsa kudziŵa tanthauzo la malotowo.

Kenako, wopelekela cikho uja anakumbukila Yosefe. Cikumbumtima cake citamuvuta, anauza Farao kuti iye ndi mkulu wa ophika mkate analota maloto m’ndende zaka ziŵili zapitazo, ndipo mnyamata wina wanzelu amene ali m’ndendemo anamasulila malotowo. Mwamsanga, Farao anatuma anthu kuti akaitane Yosefe kundendeko.—Genesis 41:9-13.

Ganizilani mmene Yosefe anamvelela pamene anthu ocokela kwa Farao anabwela kudzamuitana. Mwamsanga iye anameta bwinobwino tsitsi ndi kusintha zovala. Iye ayenela kuti anacotsa tsitsi lonse cifukwa cakuti ndiye cinali cikhalidwe ca Aiguputo. N’zosacita kufunsa kuti iye anapemphela kwambili kwa Yehova kuti amuthandize kuyankha mwanzelu zimene angafunsidwe. Patapita nthawi yocepa, iye analowa m’nyumba yacifumu yolemekezeka ndi kuimilila pamaso pa Farao. Baibulo limati: “Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: ‘Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulila. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulila.’” Yankho limene Yosefe anapeleka linasonyezanso kuti iye anali kukhulupilila Mulungu ndiponso anali wodzicepetsa. Iye anati: “Yemwe anene uthenga wokhudza moyo wa inu Farao ndi Mulungu osati ine.”—Genesis 41:14-16.

Modzicepetsa, Yosefe anauza Farao kuti: “Yemwe anene . . .ndi Mulungu osati ine”

Yehova amakonda anthu odzicepetsa ndi okhulupilika. Conco n’zosadabwitsa kuti anathandiza Yosefe kudziŵa tanthauzo la maloto amene amuna anzelu ndi ansembe analephela kumasulila. Yosefe anafotokoza kuti maloto aŵili a Farao anali ndi tanthauzo limodzi. Iye anena kuti popeza kuti Farao analota kaŵili malotowo, ndiye kuti Yehova anatsimikiza mtima kucita zimenezo. Ng’ombe zonenepazo ndi ngala 7 zooneka bwino zinali kuimila zaka 7 zimene zinali kudzakhala ndi cakudya cambili. Koma ng’ombe zowonda ndi ngala zopanda kanthu zinali kuimila zaka 7 za njala zimene zinali kudzabwela pambuyo pa zaka za cakudya cambili. Iye ananenanso kuti cakudya conse ca m’dzikolo cidzatha cifukwa ca njalayo.—Genesis 41:25-32.

Farao anakhutila ndi mmene Yosefe anamasulila malotowo. Nanga n’ciani cimene Farao anafunika kucita? Yosefe anafotokoza zimene Farao angacite. Iye anakamba kuti Farao apeze munthu “wozindikila ndi wanzelu” kuti aziyang’anila nchito yosonkhanitsa cakudya pa nthawi ya zokolola zambili ndi kucisunga bwino, ndipo kenako adzacigaŵile kwa anthu osowa cakudya panthawi ya njala. (Genesis 41:33-36) Yosefe anali wa luso ndi wodziŵa zinthu kwambili, ndipo ndiye anali woyenela kugwila nchito imeneyo. Koma iye sanadzionetsele. Yosefe anaona kuti kudzionetsela n’kosayenela cifukwa cakuti anali wodzicepetsa ndiponso anali ndi cikhulupililo. Ngati timakhulupililadi Yehova, tidzapewa mtima wofunafuna udindo wapamwamba. Tingakhale ndi mtendele wa m’maganizo ngati tisiya zonse m’manja mwa Mulungu cifukwa iye ndi wamphamvu.

‘KODI PANGAPEZEKENSO MUNTHU WINA MONGA UYU?’

Farao ndi atumiki ake anaona kuti zimene Yosefe anakamba n’zanzelu. Komanso mfumuyo inadziŵa kuti Mulungu wa Yosefe ndiye anamuthandiza kukamba mau anzelu amenewo. Iye anafunsa atumiki ake m’bwalo la mfumu kuti: ‘Kodi pangapezekenso munthu wina monga uyu, wokhala ndi mzimu wa Mulungu?’ Kenako anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziŵitsa zonsezi, palibenso munthu wina wozindikila ndi wanzelu ngati iwe. Iweyo ukhala woyang’anila nyumba yanga, ndipo anthu anga onse azimvela iweyo. Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”—Genesis 41:38-41.

Farao anasunga lonjezo lake, ndipo patapita nthawi yocepa anaveka Yosefe malaya amtengo wapatali. Farao anapatsanso Yosefe cheni cagolide, mphete yacifumu, galeta laciŵili laulemu, ndi ulamulilo wopita kulikonse m’dzikolo kukagwila nchito yake yosonkhanitsa cakudya. (Genesis 41:42-44) Conco, pa tsiku limodzi cabe Yosefe anacoka m’ndende ndi kukakhala m’nyumba ya mfumu. Patsikulo, iye anauka monga mkaidi wonyozeka koma anagona monga wolamulila waciŵili kwa Farao. Pamenepa n’zoonekelatu kuti iye anadalitsidwa cifukwa cokhulupilila Yehova Mulungu. Pa zaka zonsezo, Yehova anaona mavuto onse amene mtumiki wake anali kukumana nao. Iye anathetsa mavuto a Yosefe panthawi yoyenela ndiponso m’njila yoyenela. Colinga ca Yehova sicinali kungothetsa mavuto amene Yosefe anali kukumana nao, koma anali kufunanso kuti adzateteze mtundu wa Isiraeli mtsogolo. M’nkhani yotsatila, tidzaona mmene Mulungu anacitila zimenezi.

Mukakumana ndi mavuto aakulu, kapena ngati anthu ena anakucitilani zinthu zopanda cilungamo, ndipo vutolo likupitilizabe, musataye mtima. Kumbukilani Yosefe. Iye anapitilizabe kukhulupilila Mulungu, kukhala wokoma mtima, wodzicepetsa, ndiponso wopilila. Pa cifukwa cimeneci Yehova anamudalitsa panthawi yake.

^ par. 4 Onani nkhani yakuti “Tengelani Citsanzo Cao” m’magazini ya Nsanja ya Mlonda ya September-October 2014.

^ par. 10 Kale anthu a ku Iguputo anali kudya makeke ndi mikate ya mitundu yosiyanasiyana yoposa 90. Conco, mkulu wa atumiki a Farao ophika mikate anali ndi udindo wapamwamba. Komanso mkulu wa opeleka cikho anali kuyang’anila atumiki a Farao amene anali kuonetsetsa kuti vinyo wopita kwa Farao unali wokoma ndiponso wosaipitsidwa ndi mankhwala amene angaphe mfumu. Panthawiyo, vuto la kupha mafumu kapena kuwacitila ciwembu linali lofala. Motelo, nthawi zambili wopelekela cikho anali kukhalanso mlangizi wodalilika wa mfumu.