Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 1

Mapindu a Kudziletsa

Mapindu a Kudziletsa

KODI KUDZILETSA KUMATANTHAUZA CIANI?

Kudziletsa kumatanthauza kukwanitsa

  • kuyembekezela moleza mtima zinthu zina

  • kuugwila mtima

  • kutsiliza nchito imene siikukondweletsani

  • kuika zofuna za ena patsogolo

N’CIFUKWA CIANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?

Ana amene ni odziletsa kwambili, amakwanitsa kukaniza mayeselo olo kuti angaoneke othandiza kwa kanthawi. Koma ana amene sakwanitsa kweni-kweni kudziletsa, kaŵili-kaŵili akakula amakhala

  • aciwawa

  • ovutika maganizo

  • okoka fodya kapena kumwa moŵa mwaucidakwa, kapenanso kuseŵenzetsa amkolabongo

  • osakonda kudya zakudya zamagulu onse

Kafuku-fuku wina anapeza kuti aja amene anali odziletsa pamene anali ana, sakhala na mavuto ambili okhudza thanzi komanso nkhawa ya zandalama. Ndipo savutika kutsatila malamulo a boma. Pambuyo pa kafuku-fuku umenewo, Pulofesa wina dzina lake Angela Duckworth wa pa Yunivesiti ya Pennsylvania anati: “Sipangakhale pomveka kukamba kuti kukhala wodziletsa n’koipa.”

HMMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KUDZILETSA

Mukati ayi, azikhaladi ayi.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Mateyu 5:37.

Nthawi zina mwana angayambe kulila kapena kuvuta ngakhale pakati pa anthu, n’colinga cofuna kuti makolo ake asinthe maganizo pa zimene akamba. Ngati kholo ligonja mwana wawo akacita zimenezi, ndiye kuti amuphunzitsa kuti kuvuta kapena kulila ni njila yabwino yakuti kholo lake lisinthe maganizo, kuti ayi wawo akhale inde.

Koma ngati kholo limatsimikizila kuti likakamba kuti ayi ni ayi, mwana amaphunzila mfundo yofunika mu umoyo yakuti, sitingakhale na zonse zimene tifuna. Dr. David Walsh analemba kuti: “Anthu odziletsa ndiye amakhala na umoyo wokhutila kwambili. Si cikondi kuphunzitsa ana athu kuti angakhale na zilizonse zimene afuna.” *

Kusapatsa mwana wanu ciliconse cimene wafuna, kudzam’thandiza kukhala wodziletsa akadzakula. Mwacitsanzo, adzakana kuseŵenzetsa am’kolabongo, kugonana asanaloŵe m’cikwati, kapena kuloŵa m’makhalidwe ena oipa.

Thandizani ana anu kumvetsa zotulukapo zabwino, kapena zoipa pa zimene angacite.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.”—Agalatiya 6:7.

Mwana wanu afunika kudziŵa kuti zilizonse zimene angacite zili na zotulukapo zake. Ndipo kusadziletsa kungakhale na zotulukapo zoipa. Mwacitsanzo, ngati mwana wanu amakalipa msanga, ena angayambe kum’pewa. Koma ngati amadziletsa mwa kuugwila mtima akakhumudwitsidwa, kapena ngati amayembekeza moleza mtima ngati wina akamba, m’malo mom’dula mawu, anthu amam’konda. Conco, m’thandizeni kumvetsa kuti ngati amadziletsa, akakula adzakhala na umoyo wabwino.

Phunzitsani mwana wanu kuika patsogolo zinthu zofunika.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

Kudziletsa kumatithandiza kupewa kucita zinthu zoipa. Kumatithandizanso kucita zinthu zimene sitikonda kweni-kweni, koma zimene n’zofunika kuzicita. M’pofunika kuphunzitsa mwana wanu kuona kuti ni zinthu ziti zofunika kwambili, na kuti azicita zimenezo coyamba. Mwacitsanzo, angafunike kucita homuweki coyamba akalibe kuyamba kuseŵela.

Khalani citsanzo cabwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Ndakupatsani citsanzo kuti mmene ine ndacitila kwa inu, inunso muzicita cimodzimodzi.” —Yohane 13:15.

Mwana wanu amaona zimene mumacita pakacitika zinthu zokukalipitsani. Onetsani mwa citsanzo canu kuti kudziletsa kumakhala na zotulukapo zabwino. Mwacitsanzo, ngati mwana wanu wacita zinthu zina zoipa, kodi mumacita zinthu mwaukali kapena mumakhala wodekha?

^ par. 20 Kucokela m’buku lakuti, No: Why Kids—of All Ages—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.