Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 6

Kufunika kwa Makhalidwe Abwino

Kufunika kwa Makhalidwe Abwino

KODI ANTHU A MAKHALIDWE ABWINO AMACITA MOTANI?

Anthu a makhalidwe abwino, amasiyanitsa mosavuta cabwino na coipa. Pofuna kusiyanitsa cabwino na coipa, iwo sayendela maganizo awo apanthawiyo. Amayendela mfundo zabwino zowathandiza pa zimene afuna kucita, ngakhale pamene ali kwa okha.

N’CIFUKWA CIANI MAKHALIDWE ABWINO ALI OFUNIKA?

Ana amamvetsela maganizo osiyana-siyana opotoza makhalidwe abwino. Angamvetsele zimenezi kwa anzawo ku sukulu, m’nyimbo, m’mafilimu na m’mapulogilamu a pa TV amene amatamba. Ndipo izi zingapangitse ana amenewa kuyamba kukaikila zimene anaphunzitsidwa za cabwino na coipa.

Imeneyi imakhala vuto yaikulu maka-maka kwa ana azaka pakati pa 13 na 19. Buku lakuti Beyond the Big Talk limakamba kuti pa zaka zimenezi, acicepele amenewa “afunika kudziŵa kuti anthu ambili adzawatuntha kucita zinthu m’njila ina yake kuti ena aziwakonda. Ndiponso afunika kuti azicita zinthu zimene adziŵa kuti n’zoyenela, olo kuti anzawo asagwilizane nazo.” Mwacionekele, ana afunika kuphunzitsidwa na makolo awo, akalibe kufika zaka zosinkhukila.

MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA MAKHALIDWE ABWINO

Khazikitsani mfundo za makhalidwe abwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: ‘Anthu okhwima anaphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikila, kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’—Aheberi 5:14.

  • Muzikamba mawu osiyanitsa cabwino na coipa. Muziseŵenzetsa zocitika za tsiku na tsiku, pothandiza mwana wanu kusiyanitsa cabwino na coipa. Mungamuuze kuti: “Uku ni kuona mtima. Uku si kuona mtima.” “Uku ndiye kukhulupilika. Uku si kukhulupilika.” “Uku ni kukoma mtima. Uku si kukoma mtima.” M’kupita kwa nthawi, mwana wanu adzadziŵa kucita zabwino na kupewa kucita zoipa.

  • Afotokozeleni zifukwa zimene munakhazikitsila mfundo zimenezo. Mwacitsanzo, mungafunse mafunso monga akuti: N’cifukwa ciani kuona mtima n’kwabwino? Kodi kunama bodza kungawononge bwanji maubwenzi? N’cifukwa ciani kuba n’koipa? Thandizani mwana wanu kuphunzitsa cikumbumtima cake kusiyanitsa cabwino na coipa.

    Gogomezani mapindu a kukhala na mfundo za makhalidwe abwino. Mungauze mwana wanu kuti: “Ngati ukhala oona mtima, anthu adzayamba kukudalila.” Mungamuuzenso kuti: “Ngati ukhala wokoma mtima, anthu adzakukonda.”

Banja lanu lizidziŵika na makhalidwe abwino amene munakhazikitsa.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Pitilizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.

  • Banja lanu lizidziŵika na makhalidwe abwino amene munakhazikitsa, kuti muzikamba mosakaikila kuti:

    • “M’banja mwathu sitikamba mabodza.”

    • “Ise siticita ndewo, kapena kukalipila anthu.”

    • “Ise sititukwana.”

Mwana wanu adzadziŵa kuti mfundo zimene munakhazikitsa si malamulo cabe iyayi, koma ni mfundo zimene mufuna kuti banja lanu lizidziŵika nazo.

  • Muzikambilana kaŵili-kaŵili na mwana wanu za makhalidwe abwino a banja lanu. Seŵenzetsani zocitika za tsiku na tsiku pophunzitsa mwana wanu makhalidwe amenewo. Mungayelekezele makhalidwe amene banja lanu limalimbikitsa, na makhalidwe amene amalimbikitsidwa pa TV kapena ku sukulu. Funsani mwana wanu mafunso monga aya: “Kodi iwe ukanacita bwanji apa?” “Nanga banja lathu likanacita bwanji apa?”

Alimbikitseni kukhala na makhalidwe abwino.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.”—1 Petulo 3:16.

  • Yamikilani mwana wanu pa zimene wacita bwino. Ngati mwana wanu aonetsa makhalidwe abwino m’zimene acita, muyamikileni na kumuuza cifukwa cake wacita bwino. Mwacitsanzo, mungamuuze kuti: “Wacita zinthu moona mtima. Ndipo wanikondweletsa.” Komanso ngati wakuululilani kuti wacita cinthu cina coipa, muyamikileni coyamba mocokela pansi pa mtima pa kuona mtima kwake, mukalibe kumuwongolela.

  • Muwongoleleni akalakwitsa. Thandizani ana anu kuvomeleza zotulukapo za zocita zawo. Ana ayenela kudziŵa cimene alakwitsa, na kuwafotokozela mmene khalidwe lawo lasiyanilana na makhalidwe a banja lanu. Makolo ena amaopa kuuza ana awo kuti alakwa, cifukwa safuna kuti awakhumudwitse. Koma ngati muuza mwana wanu zimene walakwa, ndiye kuti mum’thandiza kuphunzitsa cikumbumtima cake, kuti azisiyanitsa mosavuta cabwino na coipa.