Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 3

Mmene Angakhalile Olimbikila

Mmene Angakhalile Olimbikila

KODI KULIMBIKILA KUMATANTHAUZA CIANI?

Munthu wolimbikila sabwelela m’mbuyo akakumana na zopinga, kapena zofooketsa. Koma pamatenga nthawi kuti munthu akhale na khalidwe limeneli. Nthawi zina, mwana amagwa pophunzila kuyenda, koma amalimbikila. Mofananamo, mwana kuti aphunzile mmene angakhalile na umoyo waphindu, afunika kulimbikila olo akumane na mavuto.

N’CIFUKWA CIANI KULIMBIKILA N’KOFUNIKA?

Ana ena amagwa mphwayi akalephela kukwanilitsa zinazake, akakumana na vuto, kapena akapatsidwa uphungu. Ndipo ena salimbikila olo pang’ono. Komabe, ana afunika kudziŵa mfundo izi:

  • Si nthawi zonse pamene zinthu zidzatiyendela bwino.—Yakobo 3:2.

  • Mavuto amagwela aliyense. —Mlaliki 9:11.

  • Uphungu umathandiza munthu kuti awongolele. —Miyambo 9:9.

Kulimbikila kudzathandiza mwana wanu kulimbana na mavuto mu umoyo.

MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KULIMBIKILA

Mwana wanu akalephela zina zake.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.”—Miyambo 24:16.

Thandizani mwana wanu kuti aziona zinthu moyenela. Mwacitsanzo, kodi angacite ciani akafeluka mayeso ku sukulu? Mwina angacite ulesi na kukamba kuti: “Ine ndine wolephela!”

Conco, kuti mwana wanu akhale wolimbikila, mufunika kum’thandiza mmene angacitile bwino ulendo wotsatila. Mwanjila imeneyi, iye adzagonjetsa vuto imeneyo m’malo molola vutolo kum’gonjetsa.

Koma pewani kum’thetsela vuto mwana wanu. M’malo mwake, m’thandizeni kupeza njila yake yothetsela vuto imeneyo. Mwina mungam’funse kuti, “Kodi ungacite ciani kuti uziimvetsetsa sabujekiti imene imakuvuta?”

Pakagwa mavuto.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

Za kutsogolo sizidziŵika. Munthu amene ni wolemela lelo, mailo angakhale wosauka. Amene ali na thanzi labwino-bwino lelo, mailo angapezeke kuti wadwala. Baibo imakamba kuti: “Anthu othamanga kwambili sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo . . . cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.”—Mlaliki 9:11.

Monga kholo, mumayesetsa kucita zilizonse zimene mungathe kuti muteteze mwana wanu ku zoopsa. Koma n’zosatheka kum’teteza ku mavuto onse a mu umoyo.

N’zoona kuti mwana wanu sangamvetsetse mmene zimakhalila munthu akacotsedwa nchito, kapena mavuto a zandalama. Komabe, mungam’thandize kulimbana na mavuto ena. Monga ubwenzi na mnzake ukasokonezeka, kapena wa m’banja akamwalila. *

Mwana wanu akapatsidwa uphungu.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Mvela uphungu . . . kuti udzakhale wanzelu m’tsogolo.”—Miyambo 19:20.

Sikuti munthu akapatsa mwana wanu uphungu, ndiye kuti amuvutitsa. M’malo mwake afuna kum’thandiza kuti awongolele pa zimene wacita kapena pa khalidwe lake.

Ngati mwaphunzitsa mwana wanu kulandila uphungu, inu monga kholo, komanso mwana wanu mudzapindula. Tate wina dzina lake John anati: “Ngati nthawi zonse ana sawongoleledwa akalakwitsa, iwo sadzaphunzila ciliconse. Adzapitiliza kubweletsa mavuto, ndipo imwe mudzaloŵa nchito yothetsa mavutowo mpaka kalekale. Izi zingapangitse umoyo wa makolo komanso wa mwana kukhala wovuta.”

Kodi mungam’thandize bwanji mwana wanu kupindula na uphungu? Kaya mwana wanu wapatsidwa uphungu kusukulu, kapena kwina kulikonse, pewani kumuuza kuti uphunguwo ni wosayenela. M’malo mwake mungam’funse kuti:

  • “Uganiza n’cifukwa ciani akupatsa uphungu umenewo?”

  • “Nanga ungacite ciani kuti uwongolele?”

  • “Kodi udzacita ciani ukadzakumananso na vuto imeneyi kutsogolo?”

Dziŵani kuti uphungu udzathandiza mwana wanu kukhala na umoyo wabwino lomba, komanso kutsogolo akadzakula.

^ par. 21 Onani nkhani yakuti “Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni,” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2008.