Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Mmene Angakhalile Audindo

Mmene Angakhalile Audindo

KODI KUKHALA MUNTHU WAUDINDO KUTANTHAUZA CIANI?

Anthu audindo amakhala odalilika. Amacita mokhulupilika nchito zonse zimene apatsidwa, komanso panthawi yake.

Ngakhale kuti ana alibe nzelu zaucikulile, akhoza kuyamba kuphunzila kukhala audindo. Buku lakuti Parenting Without Borders limati: “Mwana amayamba kukhala na kamtima kofuna kucita zinthu akakwanitsa miyezi 15. Ndipo pofika miyezi 18, tunzelu tumayamba kubwelamo tofuna kucita zinthu. M’zikhalidwe zambili, makolo amayamba kuphunzitsa ana kugwila nchito pakati pa zaka 5 na 7. Ndipo ambili amakwanitsa bwino kugwila nchito za pakhomo.”

N’CIFUKWA CIANI KULI KOFUNIKA KUKHALA MUNTHU WAUDINDO?

M’madela ena, acinyamata ambili amacoka panyumba pa makolo kuti akadzikhalile okha. Koma zinthu zikawavuta amabwelelanso kudzakhala kwa makolo awo. Nthawi zina izi zimacitika cifukwa cakuti makolo awo sanawaphunzitse mmene angaseŵenzetsele ndalama mwanzelu, nchito za pakhomo, kapena kukwanilitsa maudindo ofunikila a tsiku na tsiku.

Conco, ni bwino kuyambilatu kukonzekeletsa ana anu maudindo a ku ucikulile. Buku lakuti How to Raise an Adult limati: “Si canzelu kulekelela ana kuti azingodalila imwe mpaka atafika zaka 18, kenako n’kuwatayilila kuti akadzionele okha.”

MMENE MUNGAPHUNZITSILE ANA KUKHALA AUDINDO

Muziwapatsa Nchito

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

Mwacibadwa, ana acicepele amakondwela kuseŵenzela pamodzi na makolo awo. Tengelamponi mwayi pa cibadwa cawo cimeneci powapatsako nchito za pakhomo.

Makolo ena safuna kupatsa ana nchito. Amaona kuti popeza ana amapatsidwa kale homuweki yambili ku sukulu, si bwino kuwawonjezelanso mtolo wina wa nchito.

Komabe, ana amene amagwila nchito za pakhomo amacita bwino kusukulu, cifukwa amazoloŵela kupatsidwa nchito na kuzicita panthawi yake. Ndipo buku lakuti Parenting Without Borders limati: “Ngati tinyalanyaza mtima umene ana amakhala nawo wofuna kuthandiza nchito akali aang’ono, adzakula na maganizo akuti kuthandiza ena n’kosafunikila . . . Ndipo angakule na maganizo ofuna kucitilidwa zinthu nthawi zonse.”

Malinga na mawu a m’buku limeneli, ngati ana amagwilako nchito za pakhomo, amaphunzila kukhala othandiza m’malo mwa othandizidwa, opatsa m’malo mwa otenga. Nchito za pakhomo zimathandiza ana kuona kuti ni ofunika m’banja, ndipo amadzimva kuti nawonso alimo na udindo.

Thandizani ana anu kumvetsa kuti akalakwitsa zinthu pamakhala zotsatilapo zake.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Mvela uphungu ndipo utsatile malangizo kuti udzakhale wanzelu m’tsogolo.” —Miyambo 19:20.

Mwana wanu akalakwitsa zinthu, pewani mtima wofuna kumuikila kumbuyo. Mwacitsanzo, ngati wawononga cinthu ca munthu wina mwangozi, osathamangila kumuteteza. M’phunzitseni kuvomeleza zotulukapo zake. Muuzeni kuti apepese, ngakhale kukonza kapena kulipila cimene wawonongaco.

Ngati ana avomeleza zolakwa zawo na zolephela zawo, iwo angaphunzile

  • kukhala oona mtima na kuvomeleza zolakwa

  • kupewa kukankhila ena mlandu

  • kupewa kupeleka zifukwa zodzikhululukila

  • kupepesa pakafunika kutelo