Wolembedwa na Mateyo 5:1-48

  • ULALIKI WA PA PHILI (1-48)

    • Yesu ayamba kuphunzitsa pa phili (1, 2)

    • Zinthu 9 zopangitsa anthu kukhala odala (3-12)

    • Mcele na nyale (13-16)

    • Yesu anabwela kudzakwanilitsa Cilamulo (17-20)

    • Uphungu pa nkhani ya mkwiyo (21-26), cigololo (27-30), kusudzulana (31, 32), malumbilo (33-37), kubwezela (38-42), kukonda adani athu (43-48)

5  Ataona khamu la anthulo, anakwela m’phili. Ndipo atakhala pansi, ophunzila ake anabwela kwa iye.  Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:  “Odala ni anthu ozindikila zosoŵa zawo zauzimu, cifukwa Ufumu wa kumwamba ni wawo.  “Odala ni anthu amene akumva cisoni, cifukwa adzatonthozedwa.  “Odala ni anthu ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.  “Odala ni anthu amene ali na njala komanso ludzu lofuna cilungamo, cifukwa adzakhuta.  “Odala ni anthu acifundo, cifukwa adzacitilidwa cifundo.  “Odala ni anthu oyela mtima, cifukwa adzaona Mulungu.  “Odala ni anthu obweletsa mtendele, cifukwa adzachedwa ana a Mulungu. 10  “Odala ni anthu amene azunzidwa cifukwa ca cilungamo, pakuti Ufumu wa kumwamba ni wawo. 11  “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, na kukunamizilani zoipa za mtundu uliwonse cifukwa ca ine. 12  Kondwelani na kusangalala kwambili, cifukwa mphoto yanu ni yaikulu kumwamba. Pakuti umu ni mmene anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko. 13  “Inu ndinu mcele wa dziko lapansi, koma ngati mcele watha mphamvu, kodi mphamvu yake ingabwezeletsedwe motani? Umakhala wopanda nchito iliyonse, ndipo umangotayidwa kunja kumene anthu amauponda-ponda. 14  “Inu ndinu kuwala kwa dziko. Mzinda wokhala pa phili sungabisike. 15  Anthu akayatsa nyale, saibwinikila na thadza, koma amaiika pa coikapo nyale, ndipo imaunikila onse m’nyumbamo. 16  Mofananamo, onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino na kulemekeza Atate wanu wa kumwamba. 17  “Musaganize kuti n’nabwela kudzawononga Cilamulo kapena zolemba za aneneli. Sin’nabwele kudzaziwononga ayi, koma kudzazikwanilitsa. 18  Ndithudi nikukuuzani kuti ngakhale kumwamba na dziko lapansi zitacoka, kacilembo kocepetsetsa kapena kambali kakang’ono ka cilembo ca m’Cilamulo sikadzacoka mpaka zonse zitakwanilitsidwa. 19  Cotelo aliyense wophwanya limodzi mwa malamulo aang’ono kwambili amenewa, na kuphunzitsa ena kucita zimenezo, adzakhala wosayenela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. Koma aliyense wowatsatila na kuphunzitsa ena malamulowa, adzakhala woyenela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. 20  Pakuti nikukuuzani kuti ngati cilungamo canu siciposa ca alembi na Afarisi, ndithu simudzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba. 21  “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usaphe munthu, aliyense wapha munthu wapalamula mlandu wa kukhoti.’ 22  Komabe ine nikukuuzani kuti aliyense wopitiliza kukwiyila m’bale wake, wapalamula mlandu wa ku khoti. Ndipo aliyense wonena m’bale wake na mawu acipongwe, wapalamula mlandu wa ku Khoti Yaikulu. Koma aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe citsilu!’ adzapita ku Gehena* wa moto. 23  “Conco ngati wabweletsa mphatso yako ku guwa la nsembe, ndipo uli komweko wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, 24  siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo, ndipo pita ukayanjane naye m’bale wakoyo coyamba. Ndiyeno ubwelenso udzapeleke mphatso yako. 25  “Usacedwe kuthetsa nkhani na munthu wokuimba mlandu pamene uli naye pa ulendo wopita ku khoti, kuti mwina iye asakakupeleke kwa woweluza, komanso kuti woweluzayo asakakupeleke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26  Ndithu nikukuuza kuti sudzatulukamo mpaka utalipila kakhobili kothela. 27  “Munamva kuti anati: ‘Usacite cigololo.’ 28  Koma ine nikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kufika pomulakalaka, wacita naye kale cigololo mu mtima mwake. 29  Tsopano ngati diso lako lakumanja likukucimwitsa, ulikolowole na kulitaya. Pakuti ni bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.* 30  Komanso ngati dzanja lako lakumanja likukucimwitsa, ulidule na kulitaya. Pakuti ni bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.* 31  “Komanso paja anati: ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenela kumupatsa cikalata ca cisudzulo.’ 32  Koma ine nikukuuzani kuti, aliyense wosudzula mkazi wake pa cifukwa cosakhala ciwelewele,* amapangitsa mkaziyo kukhala pa mayeselo ocita cigololo, ndipo aliyense wokwatila mkazi wotelo amacita cigololo. 33  “Munamvanso kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usamalumbile koma osacita zimene walumbilazo. M’malo mwake, uzikwanilitsa malumbilo ako kwa Yehova.’ 34  Koma ine nikukuuzani kuti: Musamalumbile n’komwe, kaya mwa kuchula kumwamba cifukwa n’kumene kuli mpando wacifumu wa Mulungu, 35  kapena mwa kuchula dziko lapansi, cifukwa ni copondapo mapazi ake, kapenanso mwa kuchula Yerusalemu cifukwa ni mzinda wa Mfumu yaikulu. 36  Usamalumbile mwa kuchula mutu wako, cifukwa sungakwanitse kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyela kapena lakuda. 37  Muzingotsimikiza kuti mukati ‘Inde,’ akhaledi inde, mukati ‘Ayi,’ akhaledi ayi, cifukwa mawu owonjezela pamenepa amacokela kwa woipayo. 38  “Munamva kuti anati: ‘Diso kulipila diso, dzino kulipila dzino.’ 39  Koma ine nikukuuzani kuti: Usalimbane naye munthu woipa. M’malo mwake, aliyense akakumenya mbama kutsaya lakumanja, mutembenuzilenso linalo. 40  Ndipo ngati munthu afuna kukupeleka ku khoti kuti atenge covala cako camkati, mulole kuti atengenso covala cako cakunja. 41  Ndipo ngati winawake waudindo wakulamula kuti umunyamulile katundu kwa mtunda wa kilomita imodzi, munyamulile kwa mtunda wa makilomita aŵili. 42  Munthu akakupempha cinthu mupatse, ndipo amene afuna kubweleka* cinacake kwa iwe usamumane. 43  “Munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako na kudana naye mdani wako.’ 44  Koma ine nikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu na kupemphelela amene amakuzunzani, 45  kuti muonetse kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, cifukwa iye amawalitsila dzuŵa lake pa anthu abwino na oipa omwe. Komanso amagwetsela mvula anthu olungama na osalungama omwe. 46  Nanga pali phindu lanji ngati mumakonda anthu okhawo amene amakukondani? Kodi si zimene okhometsa misonkho amacita? 47  Ndipo ngati mumapatsa moni abale anu okha, n’ciyani capadela cimene mukucita? Kodi si zimenenso anthu a mitundu ina amacita? 48  Conco inu muyenela kukhala angwilo,* mmene Atate wanu wa kumwamba alili wangwilo.

Mawu a m'Munsi

Malo amene anali kutenthelako zinyalala kunja kwa Yerusalemu. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
M’Cigiriki, por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kubweleka popanda ciwongoladzanja.
Kapena kuti, “kukhala okwanila.”