Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 11

Kodi Mfundo za m’Baibo Zimatithandiza Bwanji?

Kodi Mfundo za m’Baibo Zimatithandiza Bwanji?

1. N’cifukwa ciani timafunikila citsogozo?

Kodi mfundo za m’Baibo zingatithandize bwanji kuti tipewe ngozi?​—SALIMO 36:9.

Mlengi wathu ni wanzelu kupambana ife. Monga Atate wacikondi, amasamala za ife. Ndiponso, sanatilenge kuti tizidzitsogolela tokha. (Yeremiya 10:23) Conco, monga mmene mwana wamng’ono amafunikila citsogozo ca makolo, ifenso timafunikila citsogozo ca Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Mfundo za m’Baibo zimapeleka citsogozo cimene ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.​—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16.

Malamulo a Yehova ndi mfundo zake zimatiphunzitsa njila yabwino yokhalila pa nthawi ino, ndipo zimationetsa mmene tingakhalile ndi madalitso osatha mtsogolo. Popeza Mulungu ndiye anatilenga, ndi bwino kuti tiziyamikila citsogozo cake ndi kutsatila malamulo ndi mfundo zake.​—Ŵelengani Salimo 19:7, 11; Chivumbulutso 4:11.

2. Kodi mfundo za m’Baibo n’ciani?

Ni mfundo zosasinthika za makhalidwe abwino zimene zimagwila nchito pa nkhani zosiyana-siyana. Koma malamulo a m’Baibo amatha kusintha ndipo amakhala ndi nkhani zake. (Deuteronomo 22:8) Tiyenela kugwilitsila nchito mphamvu yathu yolingalila kuti timvetsetse mmene mfundo ya m’Baibo ingagwilile nchito pa nkhani ina yake. (Miyambo 2:10-12) Mwacitsanzo, Baibo imaphunzitsa kuti moyo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Mfundo imeneyi ingatitsogolele pamene tili kunchito, kunyumba, ndi paulendo. Ingatithandizenso kuti tizipewa ngozi.​—Ŵelengani Machitidwe 17:28.

3. Kodi mfundo ziŵili za m’Baibo zofunika kwambili n’ziti?

Yesu anakambapo za mfundo za m’Baibo ziŵili zofunika kwambili. Mfundo yoyamba imaonetsa colinga ceni-ceni ca moyo wathu, kuti ndico kudziŵa Mulungu, kum’konda, ndi kum’tumikila mokhulupilika. Mfundo yoyamba imeneyi tiyenela kuiganizila pamene tipanga cosankha ciliconse. (Miyambo 3:6) Anthu amene amatsatila mfundo imeneyi amakhala paubwenzi ndi Mulungu. Ndipo io adzapeza cimwemwe ceni-ceni ndi moyo wosatha.​—Ŵelengani Mateyu 22:36-38.

Mfundo yaciŵili ingatithandize kuti tikhale pamtendele ndi anthu ena. (1 Akorinto 13:4-7) Kugwilitsila nchito mfundo yaciŵili imeneyi kumaphatikizapo kutsatila njila ya Mulungu yocitila zinthu ndi anthu ena.​—Ŵelengani Mateyu 7:12; 22:39, 40.

4. Kodi mfundo za m’Baibo zimatithandiza bwanji?

Mfundo za m’Baibo zimaphunzitsa mmene mabanja angakhalile ogwilizana ndi okondana. (Akolose 3:12-14) Mau a Mulungu naonso amachinjiliza mabanja mwa kuwaphunzitsa mfundo ina yowatsogolela yakuti cikwati siciyenela kutha.​—Ŵelengani Genesis 2:24.

Mwa kutsatila mfundo za m’Baibo tingadzichinjilize ife eni pamodzi ndi cuma cathu. Mwacitsanzo, olemba nchito amafuna anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibo za kukhala oona mtima ndi kucita khama. (Miyambo 10:4, 26; Aheberi 13:18) Mau a Mulungu naonso amatiphunzitsa kukhala okhutila ndi zinthu zofunika kwambili ndi kuona ubwenzi wathu ndi Mulungu kukhala cinthu cofunika kwambili kupambana zinthu zakuthupi.​—Ŵelengani Mateyu 6:24, 25, 33; 1 Timoteyo 6:8-10.

Kutsatila mfundo za m’Baibo kungachinjilize thanzi lathu. (Miyambo 14:30; 22:24, 25) Mwacitsanzo, kumvela lamulo la Mulungu loletsa kuledzela kungatichinjilize ku matenda ndi ngozi. (Miyambo 23:20) Yehova amativomeleza kuti tizimwa moŵa, koma osati mopitiiza malile. (Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10) Mfundo za mBaibo zimatithandiza mwa kutiphunzitsa kukhala osamala ndi zocita zathu ndi kuchinjiliza maganizo athu. (Salimo 119:97-100) Cifukwa cacikulu cimene Akristu oona amalemekezela malamulo a Mulungu sicakuti athandizike cabe iyai. Koma amafuna kulemekeza Yehova.​—Ŵelengani Mateyu 5:14-16.