Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 2

Kodi Mulungu Ndani?

Kodi Mulungu Ndani?

1. Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kum’lambila?

Mulungu woona ndi amene analenga zinthu zonse. Iye alibe ciyambi ndipo sazakhala ndi mapeto. (Salimo 90:2) Ndipo uthenga wabwino wopezeka m’Baibo unacokela kwa iye. (1 Timoteyo 1:11) Popeza Mulungu anatipatsa moyo, tiyenela kulambila iye yekha cabe.—Ŵelengani Chivumbulutso 4:11.

2. Kodi Mulungu ali ndi makhalidwe otani?

Palibe munthu anaonapo Mulungu cifukwa iye ni Mzimu. Zimenezi zitanthauza kuti iye ni wapamwamba kwambili kupambana zolengedwa zilizonse zimene zili pa dziko lapansi. (Yohane 1:18; 4:24) Komabe, tingadziŵe makhalidwe a Mulungu mwa kuyang’ana zinthu zimene anapanga. Mwacitsanzo, mitundu yosiyana-siyana ya zipatso ndi maluŵa imationetsa za cikondi cake ndi nzelu zake. Ndipo kukula kwa cilengedwe kumationetsa mphamvu zake.—Ŵelengani Aroma 1:20.

Tingaphunzilenso zambili za makhalidwe a Mulungu mwa kuŵelenga Baibo. Mwacitsanzo, imatiuza zimene Mulungu amakonda ndi zimene sakonda, mmene amacitila zinthu ndi anthu, ndi zimene amacita malinga ndi mikhalidwe yosiyana-siyana.—Ŵelengani Salimo 103:7-10.

3. Kodi Mulungu ali ndi dzina?

Yesu anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9) Ngakhale kuti Mulungu ali ndi maina audindo ambili, dzina lake leni-leni ndi limodzi cabe. Ndipo m’cinenelo ciliconse limachulidwa mosiyana. M’Cinyanja limachulidwa kuti “Yehova.” Koma anthu ena amalichula kuti “Yahweh.”—Ŵelengani Salimo 83:18.

Dzina la Mulungu lacotsedwa m’Mabaibo ambili ndipo aikamo maina audindo akuti Ambuye kapena Mulungu. Koma pamene Baibo inalembedwa, dzina la Mulungu linali kupezeka nthawi zokwana 7,000. Yesu anadziŵikitsa dzina la Mulungu pamene anali kuphunzitsa anthu za Mulungu.—Ŵelengani Yohane 17:26.

Tambani vidiyo Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

4. Kodi Yehova amasamala za ife

Monga tate wacikondi uyu, Mulungu amacita zinthu ndi colinga cakuti atithandize kwa nthawi yaitali

Kodi kuculuka kwa mavuto kumatanthauza kuti Yehova ni Mulungu amene sasamala za ife? Anthu ena amakamba kuti iye amacititsa mavuto pofuna kutiyesa, koma zimenezi si zoona.—Ŵelengani Yakobo 1:13.

Mulungu watilemekeza mwa kutipatsa ufulu wodzisankhila zocita. Kodi sitiyamikila ufulu umene tili nao wosankha kutumikila Mulungu? (Yoswa 24:15) Koma anthu ambili amasankha kucitila anzao zinthu zoipa. Zimenezi zimacititsa kuti anthu ambili azivutika. Zimam’pweteka kwambili Yehova akamaona kupanda cilungamo kumeneko.—Ŵelengani Genesis 6:5, 6.

Yehova ni Mulungu amene amasamala za ife. Iye amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. Posacedwa, Mulungu adzacotsa mavuto limodzi ndi anthu onse amene amawacititsa. Pakali pano, iye ali ndi cifukwa cabwino cololela mavuto kwa kanthawi. Mu Phunzilo 8, tidzaphunzila za cifukwa cimeneco.—Ŵelengani 2 Petulo 2:9; 3:7, 13.

5. Kodi tingamuyandikile bwanji Mulungu?

Yehova amatipempha kuti timuyandikile mwa kukamba naye kupitila m’pemphelo. Amacita cidwi ndi aliyense wa ife. (Salimo 65:2; 145:18) Iye ndi wokonzeka kutikhululukila macimo athu. Amaona khama lathu pofuna kum’kondweletsa, ngakhale kuti nthawi zina timalephela. Conco, mosasamala kanthu za kupanda ungwilo kwathu, ifenso tingakhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.—Ŵelengani Salimo 103:12-14; Yakobo 4:8.

Popeza Yehova watipatsa moyo, tiyenela kum’konda kuposa mmene timakondela munthu wina aliyense. (Maliko 12:30) Pamene tionetsa cikondi cathu kwa Mulungu mwa kuphunzila zambili zokhudza iye, ndi kucita zimene atipempha, tidzamuyandikila kwambili.—Ŵelengani 1 Timoteyo 2:4; 1 Yohane 5:3.