Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 7

Kodi Ufumu wa Mulungu n’Ciani?

Kodi Ufumu wa Mulungu n’Ciani?

1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani?

Kodi n’ciani cimapangitsa Yesu kukhala Mfumu yabwino kwambili?—MALIKO 1:40-42.

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Udzaloŵa m’malo maboma ena onse ndi kucita cifunilo ca Mulungu kumwamba ndi padziko lapansi. Uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu ndi wabwino kwambili. Posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzabweletsa boma labwino limene anthu akhala akufuna. Ndipo udzagwilizanitsa anthu onse amene adzakhala padziko lapansi.—Ŵelengani Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; 24:14.

Ufumu ulionse umakhala ndi mfumu yake. Yehova anasankha Mwana wake, Yesu Kristu, kukhala Mfumu ya Ufumu wake.—Ŵelengani Chivumbulutso 11:15.

Tambani vidiyo Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

2. N’cifukwa ciani Yesu ndi Mfumu yabwino kwambili?

Mwana wa Mulungu ndi Mfumu yabwino kwambili cifukwa ndi wokoma mtima, ndipo ndi wosasunthika pa kucita cabwino. (Mateyu 11:28-30) Ndiponso ali ndi mphamvu zothandiza anthu cifukwa adzalamulila dziko lapansi ali kumwamba. Ataukitsidwa, anabwelela kumwamba kukakhala ku dzanja lamanja la Yehova, n’kumayembekezela kuti akapatsidwe mphamvu. (Aheberi 10:12, 13) Potsilizila pake, Mulungu anam’patsa mphamvu yakuti ayambe kulamulila.—Ŵelengani Danieli 7:13, 14.

3. Kodi ndani adzalamulila pamodzi ndi Yesu?

Kagulu kochedwa “oyela” ndiko kadzalamulila pamodzi ndi Yesu kumwamba. (Danieli 7:27) Oyela oyamba kusankhidwa anali atumwi a Yesu okhulupilika. Yehova wapitiliza kusankha amuna ndi akazi okhulupilika kukhala anthu oyela mpaka masiku ano. Mofanana ndi Yesu, io amaukitsidwa ndi thupi lauzimu.—Ŵelengani Yohane 14:1-3; 1 Akorinto 15:42-44.

Kodi ndi anthu angati amene adzapita kumwamba? Yesu anawacha kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Iwo onse pamodzi adzakwana 144,000. Adzalamulila dziko lapansi pamodzi ndi Yesu.—Ŵelengani Chivumbulutso 14:1.

4. Kodi n’ciani cinacitika pamene Yesu anayamba kulamulila?

Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila mu 1914. * Cimene Yesu anayambilila kucita pamene anakhala Mfumu cinali kuponya Satana ndi ziŵanda zake kudziko lapansi. Satana anakwiya kwambili ndipo anayambitsa mavuto padziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 12:7-10, 12) Kucokela panthawi imeneyo mavuto a anthu aonjezeleka kwambili. Nkhondo, njala, matenda, ndi zivomezi zonse zili mbali ya “cizindikilo” coonetsa kuti posacedwapa Ufumu udzayamba kulamulila dziko lonse lapansi.—Ŵelengani Luka 21:7, 10, 11, 31.

5. Kodi Ufumu wa Mulungu ucita ciani?

Kupitila m’nchito yolalikila, Ufumu wa Mulungu unayamba kale kugwilizanitsa khamu lalikulu la anthu ocokela m’mitundu yosiyana-siyana. Anthu ofatsa mamiliyoni akukhala nzika za Ufumu wa Mulungu wolamulilidwa ndi Yesu. Ufumu wa Mulungu udzawateteza pamene udzaononga dongosolo loipa la zinthu padziko lapansi. Conco, onse amene afuna kulandila madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa ayenela kuphunzila kukhala otsatila Yesu ndi kumumvela.—Ŵelengani Chivumbulutso 7:9, 14, 16, 17.

M’zaka cikwi, Ufumu udzakwanilitsa colinga capoyamba ca Mulungu kulinga kwa anthu. Dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso. Potsilizila pake, Yesu adzabweza Ufumu kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24-26) Kodi muli ndi anzanu amene mungafune kuwauzako za Ufumu wa Mulungu?—Ŵelengani Salimo 37:10, 11, 29.

 

^ ndime 6 Kuti mudziŵe zambili zimene ulosi wa m’Baibo unakambilatu za caka ca 1914, onani pa mapeji 215 mpaka 218 m’buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse.