Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Kodi Yesu Kristu Ndani?

Kodi Yesu Kristu Ndani?

1. Kodi Yesu anakhalako bwanji?

Kodi ndi makhalidwe ati amene anacititsa kuti Yesu akhale wofikilika?—MATEYU 11:29; MALIKO 10:13-16.

Mosiyana ndi munthu wina aliyense, Yesu anali kumwamba monga mngelo akalibe kubadwa padziko lapansi. (Yohane 8:23) Iye ndiye woyamba kulengedwa ndi Mulungu, ndipo anathandiza kulenga zinthu zina zonse. Ndi iye cabe amene analengedwa ndi Yehova mwacindunji. Ndiye cifukwa cake amachedwa Mwana “wobadwa yekha” wa Mulungu. (Yohane 1:14) Cifukwanso Yesu anali mneneli wa Mulungu, anachedwanso “Mau.”​—Ŵelengani Miyambo 8:22, 23, 30; Akolose 1:15, 16.

2. N’cifukwa ciani Yesu anabwela padziko lapansi?

Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi mwa kusamutsila moyo wa mwanayo m’mimba mwa namwali waciyuda, Mariya. Pa cifukwa cimeneci, Yesu analibe tate waumunthu. (Luka 1:30-35) Iye anabwela padziko lapansi (1) kudzaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu, (2) kudzapeleka citsanzo ca mmene tingacitile cifunilo ca Mulungu ngakhale panthawi zovuta, ndi (3) kudzapeleka moyo wake wangwilo monga “dipo.”—Ŵelengani Mateyu 20:28.

3. N’cifukwa ciani tifunikila dipo?

Dipo ni malipilo amene amapelekedwa pofuna kuombola munthu amene wauzidwa kuti adzaphedwa. (Ekisodo 21:29, 30) Kucokela paciyambi, sicinali colinga ca Mulungu kuti anthu azikalamba ndi kufa. Kodi timadziŵa bwanji zimenezi? Mulungu anauza munthu woyamba, Adamu, kuti ngati angacite cimene Baibo imacha “chimo,” ndiye kuti adzafa. Conco, Adamu akanakhala kuti sanacimwe, sakanafa. (Genesis 2:16, 17; 5:5) Baibo imati, imfa “inaloŵa” m’dziko kupyolela mwa Adamu. Mwa ici, Adamu anapatsila ana ake ucimo ndi cilango cake ca imfa. Conco, timafunikila dipo kuti timasulidwe ku cilango ca imfa cimene tinatengela kwa Adamu.​—Ŵelengani Aroma 5:12; 6:23.

Kodi ndani akanapeleka dipo lotimasula ku imfa? Tikafa, ndiye kuti talandila cilango ca macimo athu. Palibe munthu wopanda ungwilo amene angalipile macimo a anthu ena.​—Ŵelengani Salimo 49:7-9.

4. N’cifukwa ciani Yesu anafa?

Mosiyana ndi ife, Yesu anali wangwilo. Conco, sakanafunikila kufa kaamba ka macimo ake​—cifukwa analibe chimo lililonse. M’malo mwake, Yesu anafa kaamba ka macimo a anthu ena. Mulungu anaonetsa cikondi cacikulu kwa anthu mwa kutumiza Mwana wake kudzatifela. Yesu nayenso anaonetsa kuti amatikonda mwa kumvela Atate wake ndi kupeleka moyo wake kaamba ka macimo athu.​—Ŵelengani Yohane 3:16; Aroma 5:18, 19.

Tambani vidiyo N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

5. Kodi Yesu acita ciani panthawi ino?

Pamene Yesu anali padziko lapansi, anacilitsa odwala, kuukitsa akufa ndi kuthandiza anthu amene anali ndi mavuto. Mwa kucita zimenezi, anaonetsa zimene adzacitila anthu onse omvela mtsogolo. (Mateyu 15:30, 31; Yohane 5:28) Pambuyo pakuti Yesu wafa, Mulungu anamuukitsa kuti akhale ndi moyo monga munthu wauzimu. (1 Petulo 3:18) Ndiyeno Yesu anayembekezela ku dzanja lamanja la Mulungu mpaka pamene Yehova anam’patsa mphamvu zakuti alamulile dziko lonse lapansi monga Mfumu. (Aheberi 10:12, 13) Tsopano Yesu ali kulamulila kumwamba monga Mfumu, ndipo otsatila ake ali kulengeza uthenga wabwino padziko lonse.​—Ŵelengani Danieli 7:13, 14; Mateyu 24:14.

Posacedwa, Yesu adzagwilitsila nchito mphamvu zake monga Mfumu kuthetsa mavuto onse pamodzi ndi anthu amene amawacititsa. Onse amene amakhulupilila Yesu mwa kumumvela adzakhala ndi moyo m’paladaiso padziko lapansi.​—Ŵelengani Salimo 37:9-11.