Pitani ku nkhani yake

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima Mwanu?

Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima Mwanu?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Ufumu wa Mulungu sikuti umakhala mumtima mwa Mkhristu. a Baibulo limatchula malo enieni amene ufumuwu umapezeka chifukwa limautchula kuti ndi “Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 4:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Taonani mfundo zotsatirazi zimene Baibulo limafotokoza zosonyeza kuti ufumuwu ndi boma lenileni limene likulamulira kuchokera kumwamba.

  •   Ufumu wa Mulungu uli ndi olamulira, anthu amene ukuwalamulira, komanso uli ndi cholinga choti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansili mofanana ndi kumwamba.—Mateyu 6:10; Chivumbulutso 5:10.

  •   Boma la Mulungu, kapena kuti Ufumu, lidzalamulira ‘anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso olankhula zinenero zosiyanasiyana’ padziko lonse lapansi. (Danieli 7:13, 14) Mphamvu za olamulira a Ufumuwu zimachokera kwa Mulungu osati kwa anthu olamuliridwa.—Salimo 2:4-6; Yesaya 9:7.

  •   Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti nawonso ‘adzakhala m’mipando yachifumu’ pamodzi ndi iyeyo mu Ufumu wakumwamba.—Luka 22:28, 30.

  •   Ufumuwu udzawononga adani ake onse.—Salimo 2:1, 2, 8, 9; 110:1, 2; 1 Akorinto 15:25, 26.

 Baibulo siliphunzitsa kuti Ufumu wakumwamba uli mumtima mwanu, kapena kuti umalamulira mumtima wa munthu. Komabe, limasonyeza kuti “mawu a ufumu” kapena ‘uthenga wabwino wa ufumu’ ungathe kusintha mtima wa munthu. Ndipotu pali anthu amene mitima yawo inasinthadi.—Mateyu 13:19; 24:14.

Kodi mawu akuti “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu” akutanthauza chiyani?

 Anthu ena akawerenga Mabaibulo ena pa Luka 17:21, amasokonezeka kwambiri pa nkhani ya malo amene kuli Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limanena kuti “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwa inu.” Koma tiyenera kuona mavesi ena oyandikana ndi vesili kuti timvetse nkhaniyi.

Ufumu wa Mulungu sunali m’mitima ya anthu ankhanza amene ankatsutsa Yesu mpaka kufika pomupha

 Apa Yesu ankalankhula ndi Afarisi, omwe anali gulu la atsogoleri achipembedzo amene ankamutsutsa komanso anakonza nawo chiwembu choti amuphe. (Mateyu 12:14; Luka 17:20) Kodi inuyo mukuona kuti zingakhale zomveka kunena kuti Ufumu wa Mulungu unali m’mitima ya anthu ankhanzawo? Yesu anawauza kuti: “Mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo.”—Mateyu 23:27, 28.

 Mabaibulo ena anamasulira momveka bwino mawu a Yesu opezeka pa Luka 17:21 amenewa, kuti: “Mulungu alikukhazikitsa ufumu wake pakati panu.” (Ndife tadetsa kwambiri mawuwo; Chipangano Chatsopano cholembedwa m’Chichewa chamakono) “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika) Apa Yesu analankhula mawu osonyeza kuti ufumu wakumwamba unali “pakati” pa Afarisiwo chifukwa chakuti Yesuyo, amene anasankhidwa ndi Mulungu kukhala Mfumu, anali pakati pawo.—Luka 1:32, 33.

a Matchalitchi ambiri achikhristu amaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu umakhala mumtima mwa munthu. Mwachitsanzo, akuluakulu a mpingo wa Southern Baptist Convention ku United States ananena kuti Ufumu wa Mulungu ndi mbali ya “ulamuliro wa Mulungu pa moyo ndi mumtima mwa munthu.” Mofanana ndi zimenezi, Papa Benedict wa nambala 16 analemba m’buku lake lina lonena za Yesu kuti: “Ufumu wa Mulungu umabwera mwa munthu, munthuyo akakhala ndi mtima womvetsera.”—Jesus of Nazareth.