Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndi Ndani?

Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndi Ndani?

Mulungu anauzira olemba Baibulo osiyanasiyana kuti alembe zimene zingatithandize kuzindikira amene adzakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Wolamulirayo anali woti

  • Adzasankhidwa ndi Mulungu. “Inetu ndakhazika mfumu yanga . . . ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako, ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.”​—Salimo 2:6, 8.

  • Adzabadwira m’banja la Mfumu Davide. “Kwa ife kwabadwa mwana. Ife tapatsidwa mwana wamwamuna . . . Ulamuliro wake . . . udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha pampando wachifumu wa Davide ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika.”​—Yesaya 9:6, 7.

  • Adzabadwira ku Betelehemu. “Iwe Betelehemu . . . , mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira . . . Iye adzakhala wamkulu mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mika 5:2, 4.

  • Anthu adzamukana ndipo adzaphedwa. “Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake. . . . Iye anabayidwa chifukwa cha zolakwa zathu. Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.”​—Yesaya 53:3, 5.

  • Adzaukitsidwa n’kupatsidwa ulemerero. “Simudzasiya moyo wanga m’Manda. Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje. . . . Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.”​—Salimo 16:10, 11.

Yesu Ndi Woyenera Kukhala Wolamulira

Pa anthu onse amene anakhalapo padzikoli, ndi Yesu yekha amene zinthu zomwe zatchulidwazi zinamuchitikira. Ndipotu mngelo anauza Mariya, mayi ake a Yesu, kuti: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, . . . moti ufumu wake sudzatha konse.”​—Luka 1:31-33.

Yesu sanakhalepo wolamulira ali padziko lapansili. Komabe azidzalamulira anthu, iyeyo ali kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Koma kodi n’chiyani chikumupangitsa kukhala wolamulira wabwino kuposa aliyense? Taonani zomwe Yesu anachita ali padzikoli.

  • Ankakonda anthu. Yesu ankathandiza amuna ndi akazi omwe, ana komanso achikulire, mosatengera kumene achokera kapena mmene zinthu zilili pa moyo wawo. (Mateyu 9:36; Maliko 10:16) Munthu wina wakhate atamupempha kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa,” Yesu anamumvera chisoni ndipo anamuchiritsa.​—Maliko 1:40-42.

  • Anatiphunzitsa zomwe tingachite kuti tizisangalatsa Mulungu. Yesu ananena kuti: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” Iye ananenanso kuti tizichitira ena zomwe ifenso tingakonde kuti atichitire. Anasonyezanso kuti kuwonjezera pa zimene timachita, Mulungu amachitanso chidwi ndi zimene timaganiza ndiponso mmene timamvera mumtima. Choncho kuti tizisangalatsa Mulungu, tiyenera kumadziletsa pa zimene timaganiza. (Mateyu 5:28; 6:24; 7:12) Yesu anatsindika mfundo yoti munthu angakhale wosangalala ngati akuphunzira zimene Mulungu amafuna n’kumazichita.​—Luka 11:28.

  • Anatiphunzitsa kukonda ena. Zimene Yesu ankalankhula komanso kuphunzitsa zinkakhudza kwambiri mitima ya anthu amene ankamumvetsera. Baibulo limanena kuti: “Khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro.” (Mateyu 7:28, 29) Iye anawaphunzitsa kuti: ‘Muzikonda adani anu.’ Anapemphereranso ngakhale anthu ena amene anamupha. Iye anati: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”​—Mateyu 5:44; Luka 23:34.

Yesu ndi woyenera kukhala Wolamulira chifukwa ndi amene angathandizedi anthu. Koma kodi adzayamba liti kulamulira?