Pitani ku nkhani yake

Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?

Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo, mawu akuti “kumwamba” amagwiritsidwa ntchito poimira zinthu zitatu: (1) kumwamba kumene timaona; (2) malo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu; ndipo (3) chizindikiro cha malo okwezeka. Komabe, munthu angathe kudziwa tanthauzo loyenera la mawuwa malinga ndi nkhani imene akupezekamo. a

  1.   Kumwamba kumene timaona. Apa, “kumwamba” kukutanthauza mbali ya dziko komwe mphepo imaomba, mbalame zimauluka, mitambo imapanga mvula ndi chipale chofewa ndiponso komwe kumaoneka ziphaliwali. (Salimo 78:26; Miyambo 30:19; Yesaya 55:10; Luka 17:24) Liwuli lingatanthauzenso kuthambo komwe kuli “dzuwa, mwezi ndi nyenyezi.”​—Deuteronomo 4:19; Genesis 1:1.

  2.   Malo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu. Mawu akuti “kumwamba” amatanthauzanso malo amene kumakhala zolengedwa zauzimu ndipo ndi kutali kwambiri kuposa kumwamba komwe timaona ndi maso. (1 Mafumu 8:27; Yohane 6:38) Kumeneku n’kumene kumakhala Yehova Mulungu, yemwe ndi “Mzimu,” komanso angelo omwe ndi zolengedwa zauzimu. (Yohane 4:24; Mateyu 24:36) Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “kumwamba,” ponena za angelo, omwe ndi “mpingo wa oyera.”—Salimo 89:5-7.

     Baibulo limagwiritsanso ntchito mawu oti “kumwamba” ponena za mbali ya malo enieni amene Yehova amakhala, omwe ndi ‘malo ake okhala okhazikika.’ (1 Mafumu 8:43, 49; Aheberi 9:24; Chivumbulutso 13:6) Mwachitsanzo, Baibulo linaneneratu kuti Satana adzachotsedwa kumwamba limodzi ndi ziwanda zake ndipo sadzaloredwanso kupita kumalo enieni amene Yehova amakhala. Komabe, iwo akadali zolengedwa zauzimu.—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

  3.   Chizindikiro cha malo okwezeka. Malemba amagwiritsanso ntchito mawu akuti “kumwamba” kutanthauza malo okwezeka, ndipo nthawi zambiri mawuwa amanena za olamulira. Olamulira amenewa akhoza kukhala:

Kodi kumwamba n’kotani?

 Kumwamba komwe kumakhala zolengedwa zauzimu kumachitika ntchito zosiyanasiyana. Zolengedwazi ndi angelo ambirimbiri “ochita zimene [Yehova] wanena.”—Salimo 103:20, 21; Danieli 7:10. Baibulo limasonyeza kuti kumwamba n’kowala kwambiri. (1 Timoteyo 6:15, 16) Mneneri Ezekieli anaona masomphenya osonyeza kumwamba kowala monyezimira, pomwe masomphenya akumwamba amene Danieli anaona anali ndi “mtsinje wa moto.” (Ezekieli 1:26-28; Danieli 7:9, 10) Kumwamba n’koyera komanso n’kokongola.—Salimo 96:6; Yesaya 63:15; Chivumbulutso 4:2, 3.

 Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza kumwamba zimasonyeza kuti n’kochititsa mantha. (Ezekieli 43:​2, 3) Komabe, n’zosatheka kuti anthu adziwe bwinobwino mmene kumwamba kulili chifukwa chakuti kumakhala zolengedwa zauzimu zokhazokha.

a Mawu a Chiheberi amene amatanthauza “kumwamba” amachokera ku liwu limene limatanthauza “kutalika” kapena “pamwamba.” (Miyambo 25:3) Onani The New Brown, Driver, and Briggs Hebrew and English Lexicon of the Old Testament, tsamba 1029.

b Buku lina linanena kuti kumwamba kwatsopano kotchulidwa pa Yesaya 65:17 kumatanthauza “boma latsopano, ufumu watsopano.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia, voliyumu 4, tsamba 122.