Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani pa Nkhani ya Malilime?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani pa Nkhani ya Malilime?

Yankho la m’Baibulo

 “Kulankhula malilime” inali mphamvu yodabwitsa yomwe Akhristu oyambirira ankapatsidwa ndipo inkawathandiza kulankhula chilankhulo china ngakhale asanachiphunzire n’komwe. (Machitidwe 10:46) Aliyense wodziwa chilankhulocho ankatha kumva zomwe wolankhulayo akunena. (Machitidwe 2: 4-8) Kulankhula malilime inali imodzi mwa mphatso zomwe Mulungu anapereka kwa Akhristu oyambirira pogwiritsa ntchito mzimu woyera.​—Aheberi 2:4; 1 Akorinto 12:4, 30.

 Kodi kulankhula malilime kunayambira kuti ndipo kunayamba liti?

 Anthu anayamba kulankhula malilime koyamba ku Yerusalemu mu 33 C.E m’mawa wa patsiku lomwe Ayuda ankachita Phwando la Pentekosite. Ophunzira a Yesu pafupifupi 120 anali atasonkhana pamodzi ndiyeno “onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana.” (Machitidwe 1:​15; 2:​1-4) Pa nthawiyi khamu la anthu “ochokera mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo” anasonkhana ndipo “aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’chinenero chake.”​—Machitidwe 2:​5, 6.

 Kodi n’chifukwa chiyani anthu ankalankhula malilime?

  1.   Pofuna kusonyeza kuti Mulungu anali kumbali ya Akhristu. Kale, Mulungu ankachita zizindikiro zodabwitsa kwa anthu ake okhulupirika monga Mose, pofuna kusonyeza kuti ali kumbali yawo. (Ekisodo 4:​1-9, 29-​31; Numeri 17:10) Zimenezi zinali zofanana ndi malilime. Kulankhula malilime kunkasonyeza kuti Mulungu ndi amene ankathandiza mpingo wa Akhristu womwe unali utayamba kumene. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malilimewo ndi chizindikiro kwa osakhulupirira, osati kwa okhulupirira.”​—1 Akorinto 14:22.

  2.   Pothandiza Akhristu kuchitira umboni mokwanira. Anthu amene anamva otsatira a Yesu akulankhula malilime pa tsiku la Pentekosite ananena kuti: “Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenero zathu.” (Machitidwe 2:11) Chimenechinso chinali cholinga china chachikulu chifukwa chinathandiza Akhristu “kupereka umboni wokwanira” komanso ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira’ monga mmene Yesu anawalamulira. (Machitidwe 10:42; Mateyu 28:19) Tsiku lomwelo, anthu pafupifupi 3,000 amene anaona zodabwitsazo komanso kumvetsera umboni womwe unkaperekedwa, anakhala ophunzira a Yesu.​—Machitidwe 2:41.

 Kodi panopa anthu amafunikabe kuti azilankhula malilime?

 Ayi. Kulankhula malilime inali imodzi mwa mphatso za mzimu woyera, yomwe inali ya kanthawi kochepa. Ndipotu Baibulo linaneneratu kuti: “Kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya kulankhula malilime, kudzatha.”​—1 Akorinto 13:8.

 Kodi kulankhula malilime kunatha liti?

 Kale, mphatso ya mzimu woyera inkaperekedwa kwa Akhristu ena pogwiritsa ntchito atumwi. Kuti zimenezi zitheke, atumwiwo ankasanjika manja pamutu pa Akhristu okhulupirikawo. (Machitidwe 8:​18; 10:44-​46) Komabe zikuoneka kuti anthu amene ankalandira mzimuwo, sankatha kugawirakonso ena. (Machitidwe 8:​5-7, 14-17) Kuti timvetse mfundo yake, tiyerekeze chonchi, mkulu wa boma akhoza kukhala ndi mphamvu yopereka laisensi yoyendetsera galimoto kwa munthu. Koma munthuyo sangakhalenso ndi mphamvu yoti apereke laisensi kwa munthu wina. N’chimodzimodzinso ndi mphatso ya malilime. Mphatsoyi inatha atumwi komanso anthu ena omwe analandira mzimu woyera atamwalira.

 Nanga bwanji za malilime omwe amalankhulidwa masiku ano?

 Pali umboni wakuti mphatso ya kulankhula malilime inatha chakumapeto kwa zaka 100 zoyambirira. Choncho panopa palibenso amene anganene kuti amalankhule malilime mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. a

 Kodi Akhristu enieni tingawadziwe bwanji?

 Yesu ananena kuti ophunzira ake adzadziwika ndi chikondi. (Yohane 13:34, 35) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu enieni tidzawadziwa ndi chikondi. (1 Akorinto 13:1, 8) Paulo anasonyeza kuti mzimu woyera udzathandiza Akhristu kuti akhale ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” Ndipotu khalidwe loyamba lomwenso ndi lalikulu kwambiri ndi chikondi.​—Agalatiya 5:22, 23.

a Werengani nkhani yakuti, “Kodi Masiku Ano Mulungu Ndi Amene Amachititsa Anthu Kulankhula Malilime?” yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2010 tsa. 29.