Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Anasintha Zamoyo Zina Polenga Mitundu Inanso ya Zamoyo?

Kodi Mulungu Anasintha Zamoyo Zina Polenga Mitundu Inanso ya Zamoyo?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Mulungu analenga anthu komanso “mitundu” ya nyama ndi mbewu zosiyanasiyana. a (Genesis 1:12, 21, 25, 27; Chivumbulutso 4:11) Limanenanso kuti anthu onse anachokera kwa Adamu ndi Hava omwe ndi makolo athu oyambirira. (Genesis 3:20; 4:1) Baibulo silimanena kuti Mulungu anagwiritsa ntchito zamoyo zina polenga mitundu inanso ya zamoyo. Komanso silitsutsa zimene asayansi amanena zoti mitundu ya zamoyo imatulutsanso zamoyo zina zofanana ndi zamtundu womwewo.

 Kodi Mulungu analenga zamoyo kuchokera ku zamoyo zina?

 Anthu omwe amakhulupirira kuti Mulungu analenga zamoyo kuchokera ku zamoyo zinanso ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. Ena amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene “amatsogolera zamoyo zonse m’chilengedwechi kuti zizisintha potengera malo amene zili.”

 Maganizo enanso omwe anthu ali nawo angaphatikizeponso akuti:

  •   Zamoyo zonse zinachokera ku zamoyo zinanso zakalekale.

  •   Chamoyo china chikhoza kusinthiratu n’kukhala chamoyo cha mtundu wina watsopano.

  •   Mulungu ayenera kuti ndi amene amachititsa kuti zimenezi zitheke.

 Kodi mfundo yoti zamoyo zinachita kusintha ndi yogwirizana ndi zimene Baibulo limanena?

 Mfundo yoti zamoyo zinachita kusintha ndi yosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena m’buku la Genesis, kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Ndipotu Yesu anagwiritsa ntchito mfundo za m’bukuli potsimikizira kuti ndi zoona. (Genesis 1:26, 27; 2:18-24; Mateyu 19:4-6) Baibulo limanena kuti Yesu asanabwere padziko lapansi ankakhala kumwamba ndi Mulungu ndipo anathandiza Mulunguyo kulenga “zinthu zonse.” (Yohane 1:3) Choncho, mfundo yakuti Mulungu anasintha zamoyo zina polenga mitundu inanso ya zamoyo ndi yosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

 Nanga bwanji zomera ndi nyama zimatha kusintha zikakhala pamalo ena atsopano?

 Baibulo silimafotokoza kuchuluka kwa mitundu inanso ya zamoyo yomwe ingapangidwe kuchokera pa mtundu umodzi wa chamoyo. Komabe, silimatsutsa mfundo yakuti zinyama komanso zomera zina zomwe Mulungu anapanga, zikhoza kusintha maonekedwe pamene zikuberekana kapena chifukwa choti zakakhala malo ena. Ngakhale kuti anthu ena amaona kuti zamoyozi zikasintha potengera malo ndiye kuti mtundu watsopano wa chamoyo umapangidwa, zimenezi sizolondola.

a M’Baibulo mawu akuti “mtundu” amatanthauza zambiri kuposa zimene asayansi amanena. Nthawi zambiri asayansi amanena kuti zamoyo zimasintha n’kukhala mtundu wina wa zamoyo zatsopano. Koma buku la Genesis limasonyeza kuti kwenikweni kumangokhala kusiyana maonekedwe kwa zamoyo zomwe zapangidwa kuchokera m’zamoyo zamtundu womwewo.