Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mukudziwa Mmene Mulungu Analengera Zinthu Zonsezi?

Kodi Mukudziwa Mmene Mulungu Analengera Zinthu Zonsezi?

ANTHU ambiri anawerengapo kapena kumva zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mmene Mulungu analengera zinthu zonse. Nkhani imeneyi inalembedwa zaka 3,500 zapitazo ndipo imayamba ndi mawu akuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”

Koma anthu ambiri sadziwa kuti atsogoleri a matchalitchi komanso anthu ena amene amakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa, amaphunzitsa zabodza zokhudza mmene chilengedwe chinalengedwera. Zimene anthu amenewa amanena sizipezeka m’Baibulo komanso n’zosiyana ndi zimene asayansi amanena. Komabe zapangitsa kuti anthu ena asamakhulupirire zimene Baibulo limanena chifukwa choganiza kuti ndi nthano chabe.

Anthu ambiri sadziwa zoona zenizeni zimene Baibulo limanena zokhudza mmene Mulungu analengera zinthu zonse. Izi n’zomvetsa chisoni chifukwatu Baibulo limanena momveka bwino mmene Mulungu analengera chilengedwechi. Chochititsa chidwi n’choti zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi, zimagwirizana ndi zimene asayansi apeza. Mungadabwe kudziwa kuti pali zambiri zimene Baibulo limanena zokhudza chilengedwechi, zomwe anthu ambiri sazidziwa.

MLENGI SANALENGEDWE

Zimene Baibulo limanena zokhudza chilengedwechi, zimasonyeza kuti pali Mulungu Wamphamvuyonse amene analenga zinthu zonsezi. Kodi iye ndi ndani, ndipo ndi wotani? Baibulo limasonyeza kuti iye ndi wosiyana kwambiri ndi milungu ina imene imalambiridwa ndi anthu a zikhalidwe komanso zipembedzo zosiyanasiyana. Mulungu ameneyu ndi amene analenga zinthu zonse ngakhale kuti anthu ambiri samudziwa kwenikweni.

  • Mulungu si mphepo chabe, amene amangopezeka paliponse m’chilengedwechi popanda cholinga chenicheni. Iye amaganiza, kusangalala kapena kukhumudwa komanso amakhala ndi zolinga.

  • Mulungu ali ndi mphamvu komanso nzeru zopanda malire. N’chifukwa chake anatha kulenga zinthu zogometsa zimene zili m’chilengedwechi.Nzeru komanso mphamvu zake zimaonekera makamaka tikaona mmene analengera zinthu zamoyo.

  • Mulungu analenga zinthu zonse zimene timaonazi. N’zosatheka kuti anthu apange Mulungu pogwiritsa ntchito zinthu zimene Mulunguyo analenga. Choncho, Mulungu ndi mzimu, saoneka ndipo ndi wosiyana kwambiri ndi zinthu zimene timaonazi.

  • Ngakhale patapita nthawi yaitali bwanji, Mulungu adzakhalapobe. Iye anakhalapo kuyambira kalekale ndipo adzakhalaponso mpaka kalekale. Izi zikusonyeza kuti Mulungu sanachite kulengedwa.

  • Mulungu ali ndi dzina ndipo dzinali limapezeka kambirimbiri m’Baibulo. Dzina lake ndi Yehova.

  • Yehova Mulungu amakonda kwambiri anthu komanso amawadera nkhawa.

 KODI MULUNGU ANALENGA CHILENGEDWE CHONSECHI KWA NTHAWI YAITALI BWANJI?

Baibulo limanena kuti Mulungu analenga “kumwamba ndi dziko lapansi.” Mawu amenewa sakusonyeza kuti Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi kwa nthawi yaitali bwanji. Sakusonyezanso kuti Mulungu analenga bwanji zinthu zimenezi. Nanga bwanji za mfundo yofala imene anthu ena amanena, yoti Mulungu analenga zinthu zonse kwa masiku 6 enieni? Anthu amene amakakamira mfundo imeneyi samvetsa bwino zimene Baibulo limanena, ndipo mfundoyi asayansi amaitsutsa kwambiri. Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

Zimene Baibulo limanena sizigwirizana ndi mfundo yoti Mulungu analenga zinthu m’masiku 6 enieni, ngati mmene anthu ena amanenera

  • Zimene Baibulo limanena sizigwirizana ndi mfundo yoti Mulungu analenga zinthu m’masiku 6 enieni, ngati mmene anthu ena amanenera.

  • Nthawi zambiri Baibulo likamanena za “tsiku,” limatanthauza nthawi yotalika mosiyanasiyana. Nthawi zina mawuwa amanena za nthawi yosadziwika kutalika kwake. Nkhani yonena za kulengedwa kwa zinthu imene ili m’buku la Genesis ndi chitsanzo cha zimenezi.

  • Pa nkhani ya m’Baibulo imeneyi, masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu ayenera kuti anali a zaka masauzande ambiri.

  • Pa nthawi imene Mulungu ankayamba kulenga zinthu zosiyanasiyana za padziko lapansili, n’kuti atalenga kale dzikoli komanso zinthu zina.

  • N’zoonekeratu kuti masiku 6 a kulenga si masiku enieni koma ndi nthawi yaitali, yomwe Yehova Mulungu analenga zinthu zapadziko lapansili kuti likhale malo abwino oti anthu azikhalapo.

  • Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kulenga sizitsutsana ndi zimene asayansi amanena zokhudza zaka zimene chilengedwechi chakhalapo.

KODI MULUNGU ANALENGA ZAMOYO PONGOZISINTHA KUCHOKERA KU ZINTHU ZINA?

Anthu ambiri amene sakhulupirira Baibulo amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku tizinthu topanda moyo ndipo amati zimenezi zinangochitika zokha. Amanena kuti pa nthawi ina m’mbuyomo, kanthu kena kangati bakiteriya kanagawikana pakati n’kukhala tinthu tiwiri ndipo tinthuto kalikonse kanagawikananso n’kupanganso tina. Izi zinapitirira kuchitika mpaka tinthuti tinachulukana kwambiri n’kukhala mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo imene ilipoyi. Zimenezi zitakhala zoona, ndiye kuti tingati anthufe tinachokera ku bakiteriya. Komatu tikaganizira mmene thupi la munthu limagwirira ntchito modabwitsa, zimenezi n’zosamveka.

Anthu enanso ambiri amene amati amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu amakhulupirira mfundo imeneyi, yoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Iwo amakhulupirira kuti Mulungu analenga kanthu kenakake kamoyo padziko lapansi ndipo kenako anaotsetsa kuti kanthuka kakusintha n’kusanduka zinthu zamoyo zosiyanasiyana. Koma izi si zimene Baibulo limanena.

Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kulenga sizitsutsana ndi zimene asayansi amanena zokhudza zaka zimene chilengedwe chakhalapo

  • Baibulo limati Yehova Mulungu analenga mitundu yonse ya zinthu zamoyo. Zinthu zimenezi ndi zomera, nyama komanso mwamuna ndi mkazi oyamba, omwe anali angwiro ndipo anali ndi makhalidwe monga nzeru, chilungamo, chikondi komanso ankatha kudzidziwa bwino.

  • Nyama komanso zomera zimene Mulungu analenga zakhala zikusintha n’kutulutsa mitundu yosiyanasiyana, komabe zimatulutsa zinthu za m’gulu lomwelo. Mwachitsanzo ng’ombe zimaberekanso ng’ombe osati mbuzi.

  • Nkhani ya m’Baibulo yonena za kulenga siitsutsana ndi zimene asayansi apeza zoti mitundu ya zamoyo imatulutsa mitundu yosiyanasiyana.

 CHILENGEDWECHI CHIMATIUZA KUTI KULI MLENGI

M’zaka za m’ma 1800, wasayansi wina wa ku Britain, dzina lake Russel Wallace, anagwirizana ndi maganizo a Charles Darwin akuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Komabe iye ananenanso kuti: “Kwa munthu wotha kuona komanso kuganiza, akaganizira za zinthu zomwe zimapezeka mu selo, m’magazi komanso za zinthu zonse zimene zili padzikoli ndi m’chilengedwe chonse . . . , angathe kuzindikira kuti pali winawake amene anazipanga komanso amene amazitsogolera. M’mawu achidule tingati, pali winawake woganiza kwambiri amene anapanga zinthu zonse.”

Pafupifupi zaka 2,000 Wallace asananene mawu amenewa, Baibulo linanena kuti: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Taganizirani za zinthu zapadziko lapansi komanso zinthu zosawerengeka zomwe zili kuthambo. Zinthu zimenezi zinapangidwa modabwitsa kwambiri ndipo kuganizira kwambiri za zinthuzi kungakuthandizedi kudziwa kuti pali Mlengi amene analenga zonsezi.

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Ngati kulidi Mulungu wachikondi amene analenga zinthu zonse, n’chifukwa chiyani amalola kuti zoipa zizichitika? Kodi anatinyanyala? Nanga kodi tsogolo la dzikoli ndi lotani?’ M’Baibulo mulinso mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa. Koma chifukwa cha zimene anthu ena komanso atsogoleri a zipembedzo amaphunzitsa, anthu ambiri sadziwa zolondola pa nkhani zimenezi. A Mboni za Yehova, amene amafalitsa magaziniyi, angakuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Angakuthandizeninso kudziwa zambiri za Mlengi komanso zimene wakonza kudzachitira anthu m’tsogolo.