Pitani ku nkhani yake

Kodi Mumakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?

Ayi. N’zoona kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma sitikhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni chifukwa zinthu zina zokhudza chikhulupirirochi ndi zosemphana ndi zimene Baibulo limanena. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  1. Kutalika kwa masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu zonse. Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni, tsiku lililonse lokhala ndi maola 24. Koma m’Baibulo, mawu akuti “tsiku” akhoza kutanthauza nthawi yaitali.​—Genesis 2:4; Salimo 90:4.

  2. Kodi dzikoli lakhalapo kwa zaka zingati? Anthu ena amaphunzitsa kuti dzikoli langokhala zaka masauzande ochepa kuchokera nthawi imene linalengedwa. Komabe Baibulo limasonyeza kuti dziko lapansili komanso chilengedwe chonse zinalipo masiku 6 olenga amene amatchulidwa m’Baibulo asanafike. (Genesis 1:1) Pa chifukwa chimenechi, a Mboni za Yehova satsutsa zimene asayansi ena apeza, zoti dziko lapansili lakhalapo zaka mabiliyoni ambiri kuchokera nthawi imene linalengedwa.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehovafe timakhulupirira kuti dzikoli linalengedwa ndi Mulungu, sititsutsa zimene asayansi ena amapeza. Timakhulupirira kuti zinthu zolondola zimene asayansi angapeze zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.