Pitani ku nkhani yake

Kuuza Ena Choonadi cha M’Baibulo

Dziwani zimene zimachitikira a Mboni za Yehova akamalalikira uthenga wa choonadi wochokera m’Mawu a Mulungu kwa anthu ambirimbiri.

Mfundo Zothandiza Anthu Ogwira Ntchito Zachipatala Omwe Ali Ndi Nkhawa

Kodi manesi Komanso ogwira ntchito pachipatala china anapeza bwanji mfundo zolimbikitsa pa nthawi ya mliri wa COVID-?

Anapitirizabe Kulalikira Ngakhale M’nthawi ya Mliri

Abale ndi alongo akupitiriza kukhala osangalala komanso kuona zinthu moyenera pamene akusintha njira zouzira ena uthenga wa m’Baibulo.

Madzi Osefukira Anabweretsa Uthenga Wabwino

Kutagwa mvula yamphamvu, anthu a ku Nicaragua anathandizidwa ndi anthu amene sankawayembekezera.

Phunziro la Baibulo Limodzi Linakhala Maphunziro Ambiri

A Mboni za Yehova ku Guatemala anathandiza anthu ambiri achilankhulo cha Chikekchi kuti aphunzire mfundo zoona za m’Baibulo.

M’busa Anapeza Mayankho

M’busa ndi mkazi wake analira kwambiri mwana wawo wamwamuna atamwalira chifukwa cha matenda. Koma posakhalitsa anapeza mayankho ogwira mtima a mafunso omwe anali nawo okhudza imfa.

Ankaganiza Kuti Ndi M’busa

Munthu wina Mboni za Yehova m’dziko la Chile anapeza mwayi wapadera wolalikira uthenga wabwino ndipo anafotokoza kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azimwalira.

Ulendo Wokalalikira kwa Anthu Okhala M’mphepete mwa Mtsinje wa Maroni

A Mboni za Yehova 13 akunyamuka pa ulendo wokalalikira uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo kwa anthu okhala m’madera akutali m’nkhalango ya Amazon ku South America.

A Joseph Anaperekezedwa ndi Apolisi

Kodi apolisi pakachilumba kena anathandiza bwanji a Mboni za Yehova pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?

Anaima Kuti Andithandize

N’chifukwa chiyani achinyamata 5 anaima kuti athandize munthu wina ngakhale kuti kunkagwa sinowo komanso kunkazizira kwambiri?

‘Anachita Zinthu Moona Mtima’

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene zinachititsa kuti wa Mboni za Yehova wina ku South Africa ayesetse mwakhama kubweza kachikwama kamene anatola mu shopu inayake yogulitsa khofi.

“Ndimachita Zomwe Ndingakwanitse”

Ngakhale kuti ali ndi zaka pafupifupi 90, a Irma amalemba makalata ofotokoza mfundo za m’Baibulo ndipo anthu ambiri amakhudzidwa mtima kwambiri akalandira makalatawa.

Auzeni Kuti Mumawakonda

Onani mmene Baibulo linathandizira banja lina kuti likhale logwirizana komanso losangalala kwambiri

“Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”

Anthu monga aphunzitsi ndiponso alangizi ayamba kugwiritsa ntchito mavidiyo a pawebusaiti ya jw.org.

Anamusonyeza Kukoma Mtima

Kodi kusonyeza munthu kukoma mtima kunathandiza bwanji kuti ayambe kuphunzira Baibulo?

Musataye Mtima!

Musamataye mtima n’kumaganiza kuti munthu amene mumamkonda kapena munthu winawake sangaphunzire choonadi. Werengani kuti mudziwe za ena omwe anataya mtima komanso chifukwa chake.

Hulda Anakwaniritsa Cholinga Chake

Kodi Hulda anatani kuti apeze tabuleti yoti izimuthandiza mu utumiki komanso pamisonkhano?

Anabala Zipatso Chifukwa Chokonzekera Bwino

Werengani kuti mudziwe mmene mtsikana wina wazaka 10 ku Chile anagwirira ntchito mwakhama kuti aitanire aliyense ku sukulu kwake amene amalankhula chinenero cha Chimapudunguni ku mwambo wofunika kwambiri.

Tisamaweruze Anthu Chifukwa cha Maonekedwe Awo

Kodi chinachitika n’chiyani wa Mboni za Yehova wina atalalikira kwa munthu amene ankangoyendayenda mumsewu