Pitani ku nkhani yake

Auzeni Kuti Mumawakonda

Auzeni Kuti Mumawakonda

 Mayi wina wa Mboni za Yehova ku Bulgaria dzina lake Ong-li ankaphunzira Baibulo ndi mayi wina wachitsikana dzina lake Zlatka, koma mwamuna wake sankaphunzira nawo. Ong-li ananena kuti: “Pamene tinkaphunzira zokhudza moyo wabanja, ndinafotokozera mayiyu ubwino wouza mwamuna kapena mkazi wathu ndi ana athu kuti timawakonda. Zlatka anandiyang’ana momvetsa chisoni ndipo anandiuza kuti iye sanauzepo mwamuna wake kapena mwana wake wamkazi wazaka 9 kuti amawakonda.”

 Zlatka ananena kuti, “Ndine wokonzeka kuwachitira china chilichonse koma mawu amenewo okha sindinganene. Mayi anga sanandiuzepo kuti amandikonda ndipo agogo nawonso sanawauzepo mayi anga kuti amawakonda.” Ong-li anasonyeza Zlatka kuchokera m’Baibulo kuti Yehova anachita kunena kuti amakonda Yesu. (Mateyu 3:17) Ong-li analimbikitsa Zlatka kuti aipempherere nkhaniyi kwa Yehova ndipo akhale ndi cholinga chouza mwamuna wake ndi mwana wake kuti amawakonda.

 Ong-li anati: “Patadutsa masiku awiri, Zlatka anandiuza mosangalala kuti wapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Ndiye mwamuna wake atabwera kuchokera kuntchito, anamuuza kuti pamene amaphunzira Baibulo wazindikira ubwino woti mkazi azilemekeza mwamuna wake komanso kumukonda. Atakhala chete kwa nthawi yochepa, kenako anauza mwamuna wake kuti amamukonda kwambiri. Mwana wake atafika pakhomo, Zlatka anamuhaga ndi kumuuza kuti amamukonda. Zlatka anandiuza kuti: ‘Pano ndikumva kupepuka mumtimamu. Kwa zaka zonsezi zakhala zikundivuta kufotokoza mmene ndikumvera, koma panopa Yehova wandithandiza ndipo sindivutika kufotokoza mmene ndimakondera banja langa.’

Ong-li akupitiriza kuchititsa maphunziro a Baibulo m’dera limene amakhala

 Ong-li anapitiriza kuti: “Patangotha mlungu umodzi, ndinakumana ndi mwamuna wake wa Zlatka ndipo anandiuza kuti: ‘Anthu ambiri anandiuza kuti mkazi wanga asamaphunzire Baibulo ndi inuyo, koma ndikuona kuti banja lathu lapindula kwambiri chifukwa choti akuphunzira Baibulo. Panopa tikusangalala kwambiri komanso timakondana kwambiri.’”