Pitani ku nkhani yake

”Ndimachita Zomwe Ndingakwanitse”

”Ndimachita Zomwe Ndingakwanitse”

 Mlongo wina wa ku Germany dzina lake Irma panopa ali ndi zaka pafupifupi 90. Mlongoyu anachita ngozi zikuluzikulu maulendo awiri ndipo anachitidwanso maopaleshoni maulendo angapo moti sangathenso kulalikira kunyumba ndi nyumba ngati mmene ankachitira kale. Komabe, a Irma amalalikira achibale ndi anthu ena powalembera makalata. Iwo amalemberanso anthu makalata omwe cholinga chake n’kuwalimbikitsa komanso kuwatonthoza ngati aferedwa. Anthu ambiri amayamikira akalandira makalatawa ndipo nthawi zambiri amawaimbira foni kuwafunsa kuti awalembera liti kalata ina. A Irma amalandiranso makalata ambiri owathokoza ndipo anthu ambiri amapempha kuti awalemberenso makalata ena. A Irma ananena kuti: “Zimenezi zimandisangalatsa kwambiri ndipo zimandithandiza kuti ndipitirizebe kulalikira.”

 A Irma amalemberanso makalata anthu amene ali kunyumba zosungirako achikulire. Iwo anati: “Mayi wina wachikulire anandiimbira foni kundiuza kuti kalata yomwe ndinamulembera mwamuna wake atamwalira inamulimbikitsa kwambiri. Amasunga kalatayo m’Baibulo lake ndipo nthawi zambiri amaiwerenga madzulo. Mayi winanso amene mwamuna wake anamwalira posachedwapa, ananena kuti kalata yomwe ndinamulembera inamuthandiza kwambiri kuposa ulaliki womwe wansembe analalikira pamwambo wamaliro. Mayiyo anali ndi mafunso ambiri ndipo anandipempha kuti akufuna kubwera kwathu.”

 Mayi wina yemwe amadziwana ndi a Irma anasamukira kudera lina ndipo anapempha kuti amulembere kalata. A Irma anati: “Mayiyu anasunga makalata onse omwe ndinamulemberapo. Ndipo atamwalira, mwana wake wamkazi anandiimbira foni ndipo anandiuza kuti anawerenga makalata onse omwe ndinalemberapo mayi ake ndipo anandiuza kuti angasangalale kwambiri ngati nayenso nditamamulembera makalata okhala ndi mfundo za m’Baibulo.”

 A Irma amasangalala kwambiri ndi utumiki wawowu. Iwo anati: “Ndimapempha Yehova kuti apitirize kundipatsa mphamvu kuti ndizimutumikira. Ngakhale kuti panopa sindingakwanitse kulalikira kunyumba ndi nyumba, koma ndimachita zomwe ndingakwanitse.”