Pitani ku nkhani yake

Anapitirizabe Kulalikira Ngakhale M’nthawi ya Mliri

Anapitirizabe Kulalikira Ngakhale M’nthawi ya Mliri

 Mkatikati mwa mliriwu wa COVID-19, abale ndi alongo athu asintha njira zolalikirira anthu uthenga wa m’Baibulo. M’malo mokalalikira m’malo opezeka anthu ambiri kapenanso kupita kunyumba za anthu, nthawi zambiri akhala akulalikira kudzera pafoni komanso polembera anthu makalata. * Ambiri aona kuti njirazi ndi zothandiza ndipo pali umboni wosonyeza kuti Yehova akudalitsa zomwe zakhala zikuchitikazi. (Miyambo 16:3, 4) Taganizirani izi zomwe zinachitikira abale athu omwe akukhala m’dziko lina lomwe lili pachilumba.

 Kusanagwe mliriwu, mlongo wina dzina lake Helen, ankakonda kupita kunyumba ya mayi wina wachitsikana kukamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo. Koma mayiyo ankakana. Ngakhale zinali choncho, kutangotsala tsiku limodzi kuti tiimitse ntchito zathu zina chifukwa cha mliriwu, Helen anapatsa mayi uja Baibulo komanso buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Titasiya kulalikira kunyumba za anthu, Helen anapemphanso mayi uja kuti aziphunzira naye Baibulo koma anamuuza kuti aziphunzira naye kudzera pafoni. Pa ulendowu mayi uja anavomera. Anasangalala kwambiri ndi phunzirolo moti pasanapite nthawi anapempha Helen kuti aziphunzira naye tsiku lililonse. Mayiyu anayambanso kupezeka pamisonkhano yachikhristu kudzera pafoni. Si zokhazo, kuwonjezera pa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, iye amauzanso ena zomwe amaphunzira.

 Amboni a mumpingo wina, pawokha anakonza zolembera makalata apolisi a m’dera lawo pofuna kuwathokoza chifukwa cha ntchito yofunika yomwe amagwira. Apolisi anadabwa kwambiri atalandira makalatawo. Wapolisi wina anauza Jefferson amene ndi mkulu kuti: “Ndinkaganiza kuti a Mboni za Yehova amadana ndi apolisi.” Jefferson anamulongosolera kuti si zoona kuti Amboni amadana ndi apolisi. Apolisiwo anasangalalanso kwambiri ndi uthenga womwe unalembedwa m’makalatawo moti mpaka anamata makalatawo pageti lolowera kupolisiko. Wapolisi wina ananenanso kuti: “Izi zithandiza kuti anthu ena ayambe kutiona bwino.”

 Edna ndi Ednalyn ndi apainiya okhazikika. * Chifukwa chakuti iwo alibe mwayi wa intaneti, sankatha kupezeka nawo pamisonkhano ya kumpingo yomwe imachitikira pa vidiyokomfelensi. Choncho anaimbira neba wawo wina amene si Wamboni ndi kumupempha kuti agwiritseko ntchito intaneti yake ndi kuti amubwezera ndalama zomwe angawononge. Mayiyo anawakomera mtima n’kuwalola kugwiritsa ntchito intaneti yake kwaulere. Tsiku lina Edna ndi Ednalyn atamupempha kuti aonere nawo misonkhano yathu, mayiyo anavomera. Panopo mayiyo, mwana wake wina komanso zidzukulu zake ziwiri, akuphunzira Baibulo ndi Amboni ndipo amapezeka pamisonkhano nthawi zonse.

 Nthawi ina abale ndi alongo anaitanira maneba awo, anzawo akuntchito komanso anthu ena kuti adzamvetsere nawo nkhani ya onse kudzera pafoni. Mlongo wina amene amagwira ntchito pa chipatala china m’deralo dzina lake Ellaine, ankazengereza kuitanira anzake akuntchito. Ankaganiza kuti madokotala ena akhoza kukhala kuti amadana ndi Amboni. Ngakhale zinali choncho, anatumizira madokotala a pachipatalacho meseji yowaitanira kumsonkhanowo. Komabe, Ellaine anazengerezanso kuitanira banja lina lomwe mwamuna ndi mkazi wake onse ndi madokotala. Ataganizira bwino za nkhaniyo komanso kuipempherera, anawatumizira meseji ija. Mkazi wa dokotala uja anayankha kuti: “Kodi ukufuna kuti tikhale Amboni?” Ellaine anawauza kuti aliyense ndi wolandiridwa ku msonkhanowo osati Amboni okha. Mawa lake, Ellaine anadabwa kuona kuti banja lija ndi limene linafulumira kulumikiza kumsonkhanowo. Ellaine ananena kuti: “Msonkhanowo utatsala pang’ono kutha, mkazi wa dokotala uja anandilembera meseji yondiuza kuti: ‘Kanali koyamba kuti ndipezeke pamsonkhano wa Mboni za Yehova. Unali msonkhano wabwino ndipo wandisangalatsa. Zikomo potiitana.’”

Ellaine

 Ellaine anaitanira madokotala 20 kumsonkhanowo ndipo anasangalala kwambiri kuona kuti madokotala 16 anabwera. Ellaine anagwira mawu a mtumwi Paulo ponena kuti: “Ndasangalala kuti ‘ndinalimba mtima’ kuti ndilalikire ‘uthenga wabwino wa Mulungu’ kwa anzanga akuntchito.”—1 Atesalonika 2:2.

 Nyengo ya mliriyi yakhala yovuta kwa aliyense. Koma abale ndi alongo athu a pachilumbachi komanso a kumayiko ena akhalabe osangalala komanso sanafooke pochita zonse zomwe angathe polimbikitsa ndi kuthandiza anthu ena.—Machitidwe 20:35.

^ A Mboni za Yehova amachita utumiki wawo mogwirizana ndi malamulo okhudza za zofalitsa nkhani.

^ Apainiya ndi atumiki achikhristu a nthawi zonse