Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Hulda Anakwaniritsa Cholinga Chake

Hulda Anakwaniritsa Cholinga Chake

MUKANAPITA ku Indonesia zaka zitatu zapitazo, mukanapeza alongo atatu omwe ankagwira ntchito m’mbali mwa nyanja pachilumba chaching’ono cha Sangir Besar. Iwo amadziwika kwambiri ndi ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Koma pa nthawiyi iwo ankagwira ntchito ina.

Chilumba cha Sangir Besar kumpoto kwa Indonesia

Choyamba iwo ankalowa m’madzi kukanyamula miyala ikuluikulu n’kuibweretsa kumtunda. Ina mwa miyalayi inkakhala ikuluikulu ngati mpira. Kenako ankakhala pa timipando n’kumaphwanya miyalayo ndi mahamala kuti ikhale ing’onoing’ono. Akatero ankaika miyalayo m’mabigili n’kupita nayo kumene amakhala. Kenako ankaika miyalayo m’matumba akuluakulu kuti magalimoto azitenga n’kukagwiritsa ntchito pokonza misewu.

Hulda akutola miyala m’mbali mwa nyanja

M’modzi wa alongowo anali Hulda. Chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wake, iye ankagwira ntchitoyo kwa nthawi yaitali kuposa anzakewo. Ankagwiritsa ntchito ndalama zimene ankapeza pogulira zinthu zofunika m’banja lake. Koma pa nthawiyi, iye anali ndi cholinga chinanso pogwira ntchitoyi. Ankafuna kugula tabuleti n’cholinga choti azitha kuona zinthu pa JW Library®. Hulda ankadziwa kuti mavidiyo ndi zinthu zina zopezeka pa JW Library zingamuthandize mu utumiki komanso kuti azimvetsa Baibulo.

Kwa mwezi ndi hafu, Hulda ankagwira ntchito maola awiri m’mawa uliwonse ndipo anaphwanya miyala yodzadza galimoto yaing’ono. Kenako anapeza ndalama zokwanira kukagula tabuleti ija.

Hulda ndi tabuleti yake

Hulda anati, “Ngakhale kuti ndinkatopa komanso ndinatuluka matuza m’manja, ululu wonse unatheratu nditayamba kugwiritsa ntchito tabuletiyi. Inkandithandiza kuti ndizilalikira mogwira mtima komanso ndizikonzekera misonkhano mosavuta.” Iye ananenanso kuti tabuletiyo inamuthandiza kumayambiriro kwa mliri wa COVID-19 chifukwa zinthu zambiri kumpingo sizinkachitika pamasom’pamaso. Tikusangalala limodzi ndi Hulda chifukwa chakuti anakwaniritsa cholinga chake.