Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Zinawathera Bwanji pa Nthawi Imene Anthu Ambirimbiri Anaphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi ku Germany?

Kodi a Mboni za Yehova Zinawathera Bwanji pa Nthawi Imene Anthu Ambirimbiri Anaphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi ku Germany?

A Mboni za Yehova pafupifupi 1,500 anaphedwa pa nthawi ya ulamuliro wa nkhanza wa chipani cha Nazi. Anthuwa anali m’gulu la a Mboni okwana 35,000 omwe ankakhala ku Germany ndi kumayiko ena omwe anali pansi pa ulamuliro wa chipani cha Nazi. Mpaka pano sitinapeze chifukwa chomveka chimene chinachititsa kuti anthuwa aphedwe. Popeza kuti panopa akatswiri akanafufuzabe, n’kutheka kuti chiwerengerochi chidzakwera komanso tidzamva zina ndi zina.

 Kodi anafa bwanji?

  • Makina ophera anthu omwe ankagwiritsidwa ntchito m’nthawi ya chipani cha Nazi

    Anachita kuphedwa: A Mboni pafupifupi 400 anaphedwa ku Germany komanso kumayiko ena omwe ankalamuliridwa ndi chipani cha Nazi. Ambiri mwa anthu ophedwawa anaimbidwa milandu kukhoti, kuweruzidwa kuti akaphedwe ndipo ena anaphedwa mochita kudulidwa mitu. Enanso milandu yawo sinaweruzidwe n’komwe ku khoti ndipo anangowawombera kapenanso kuwapachika.

  • Ankazunzidwa kwambiri kundende: A Mboni oposa 1,000 anafa m’ndende za m’nthawi ya chipani cha Nazi. A Mboniwa anafa chifukwa chokakamizidwa kugwira ntchito zakalavulagaga, kuvutika ndi njala, kuzizira, kudwala komanso kusowa thandizo loyenera la kuchipatala. Popeza kuti ankazunzidwa kwambiri, ena anafa atangotuluka m’ndende pambuyo pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.

  • Zifukwa zinanso: A Mboni ena ankawatsekera m’zipinda zomwe ankaikamo mpweya wa poizoni n’cholinga choti afe. Komanso madokotala akafuna kuyesa mankhwala enaake akupha, ankayeserera pa a Mboniwo kapenanso kuwabaya jekeseni wakupha.

 N’chifukwa chiyani ankazunzidwa?

A Mboni za Yehova ankazunzidwa chifukwa choti ankatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. Akuluakulu a chipani cha Nazi akawauza kuti asiye kutsatira zimene Baibulo limanena, a Mboniwo ankakana. Iwo ankasankha “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Machitidwe 5:29) Taonani mfundo ziwiri zomwe zinkachititsa a Mboniwa kukana zomwe ankauzidwa ndi akuluakulu a boma.

  1. Kusalowerera ndale. Masiku ano a Mboni za Yehova m’mayiko onse salowerera nawo ndale. Zimenezi ndi zomwenso a Mboni m’nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ankachita. (Yohane 18:36) Iwo ankakana kuchita zinthu zotsatirazi.

  2. Kutsatira zomwe amakhulupirira. Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ankaletsedwa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira, iwo ankapitirizabe kuchita zotsatirazi.

    • Kusonkhana komanso kuchita zinthu zokhudza kulambira.​—Aheberi 10:24, 25.

    • Kulalikira komanso kugawira mabuku othandiza pophunzira Baibulo.​—Mateyu 28:19, 20.

    • Kuchita zinthu mokoma mtima kwa anzawo kuphatikizaponso anthu achiyuda.​—Maliko 12:31

    • Kusonyezabe chikhulupiriro chawo pokana kusainira makalata osonyeza kuti asiya chipembedzo chawo.​—Maliko 12:30.

Pulofesa Robert Gerwarth ananena kuti a Mboni za Yehova ndi “gulu lokhalo lomwe linkazunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira kuchipembedzo chawo, mu ulamuliro wachitatu ku Germany.” a Akaidi ena ankachita chidwi kwambiri ndi a Mboni za Yehova chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba. Mkaidi wina wa ku Austria ananena kuti: “A Mboni sapita nawo kunkhondo. Amalolera kuphedwa m’malo moti iwowo aphe munthu.”

 Anafera kuti?

  • Makampu ozunzirako anthu: A Mboni za Yehova ambiri anafa m’makampu ozunzikirako anthu. Iwo anaikidwa m’makampu monga a ku Auschwitz, Buchenwald, Dachau, Flossenbürg, Mauthausen, Neuengamme, Niederhagen, Ravensbrück komanso ku Sachsenhausen. Pali umboni wakuti ku Sachsenhausen kokha, a Mboni za Yehova pafupifupi 200 anafa.

  • Kundende: A Mboni ena ankazunzidwa mpaka kufa. Ndipo ena ankafa chifukwa chovulazidwa koopsa pa nthawi yomwe ankawapanikiza ndi mafunso.

  • Kumalo opherako anthu: A Mboni za Yehova anaphedwa m’ndende za ku Berlin-Plötzensee, Brandenburg komanso ku Halle/Saale. Panopa ochita kafukufuku apezanso malo ena 70 omwe anapherako a Mboni.

 Mayina a anthu ena omwe anaphedwa

  • Dzina: A Helene Gotthold

    Malo: Plötzensee ku Berlin

    A Helene Gotthold omwe anali ndi ana awiri, anamangidwa kwa maulendo oposa awiri. Mu 1937, apolisi anawachitira nkhanza kwambiri moti mpaka mwana wawo wosabadwa anamwalira. Pa 8 December 1944, anawadula mutu pogwiritsa ntchito makina ophera anthu kundende ya Plötzensee, ku Berlin.

  • Dzina: Gerhard Liebold

    Malo: Ku Brandenburg

    Gerhard wazaka 20 anadulidwa mutu pa 6 May 1943, patadutsa zaka ziwiri kuchokera pamenenso bambo ake anadulidwa mutu m’ndende yomweyo. Iye analemba kalata yotsanzikana ndi mayi ake, mchemwali wake komanso chibwenzi chake ndipo ananena kuti: “Popanda Ambuye, sindikanapeza mphamvu zotha kupirira mavutowa.”

  • Dzina: Rudolf Auschner

    Malo: Halle/Saale

    Pa 22 September 1944, pamene Rudolf ankadulidwa mutu, anali ndi zaka 17 zokha. M’kalata yotsanzikana ndi mayi ake analembamo kuti: “Abale ndi alongo ambiri anaphedwanso chifukwa cha chikhulupiriro chawo moti inenso ndikungoyenera kuchita zomwezo.”

a Buku la Hitler’s Hangman: The Life of Heydrich, tsamba 105.