Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analola Kuti Anthu Ambirimbiri Aphedwe mu Ulamuliro wa Nazi ku Germany?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analola Kuti Anthu Ambirimbiri Aphedwe mu Ulamuliro wa Nazi ku Germany?

 Anthu ambiri amene amafunsa funso limeneli amakhala kuti zinthu zopweteka kwambiri, ngati imfa ya wachibale wawo, zawachitikira ndipo akufuna kulimbikitsidwa. Ena amaona kuti anthu amene anaphedwa mu ulamuliro wa Nazi ndi umboni wa uchimo wa anthu ndipo zimawachititsa kukhulupirira kuti kulibe Mulungu.

Zinthu zolakwika zimene anthu ena amakhulupirira pa nkhani ya Mulungu komanso kuphedwa kwa anthu ambirimbiri mu ulamuliro wa Nazi

 Zimene anthu ena amakhulupirira: N’kulakwa kufunsa chifukwa chimene Mulungu analolera kuti anthu ambirimbiri aphedwe mu ulamuliro wa Nazi ku Germany.

 Zimene Baibulo limanena: Anthu ena okhulupirika anafunsapo Mulungu chifukwa chimene amalolera zinthu zoipa kuchitika. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anafunsa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?” (Habakuku 1:3) Mulungu sanadzudzule Habakuku chifukwa chofunsa mafunso amenewa. Iye analola kuti mafunsowa alembedwe m’Baibulo kuti anthu aziwerenga.

 Zimene anthu ena amakhulupirira: Mulungu samva chisoni anthu akamavutika.

 Zimene Baibulo limanena: Mulungu amadana ndi anthu ochita zoipa ndipo amamva chisoni anthu akamavutika. (Miyambo 6:​16-19) Mulungu “zinam’pweteka kwambiri mumtima” pamene anthu ankachita zachiwawa m’masiku a Nowa. (Genesis 6:​5, 6) N’zosakayikitsa kuti Mulungu anamvanso chisoni komanso kupwetekedwa mtima kuona anthu ambirimbiri akuphedwa mu ulamuliro wa Nazi ku Germany.​—Malaki 3:6.

 Zimene anthu ena amakhulupirira: Mulungu anagwiritsira ntchito nkhanza za ulamuliro wa Nazi pofuna kulanga Ayuda.

 Zimene Baibulo limanena: M’nthawi ya atumwi, Mulungu analola kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwe ndi Aroma. (Mateyu 23:37–24:2) Komabe kuchokera nthawi imeneyi, Mulungu sagwiritsiranso ntchito mtundu wina wa anthu kuti uwononge mtundu wina ndipo samaona kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa wina. Mulungu amaona kuti “palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki.”​—Aroma 10:12.

 Zimene anthu ena amakhulupirira: Zikanakhala kuti kulidi Mulungu, amene anthu amati ndi wachikondi komanso wamphamvu zochuluka, sakanalola kuti anthu ambirimbiri aphedwe mu ulamuliro wa Nazi ku Germany.

 Zimene Baibulo limanena: Ngakhale kuti Mulungu sachititsa kuti anthu azivutika, nthawi zina amatha kulola mavuto kuchitika kwa kanthawi.–Yakobo 1:13; 5:11

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analola Kuti Anthu Ambirimbiri Aphedwe mu Ulamuliro wa Nazi ku Germany?

 Chifukwa chimene Mulungu analolera kuti anthu ambirimbiri aphedwe mu ulamuliro wa Nazi ku Germany n’chofanana ndi chimene walolera kuti anthu azivutika padziko lonse lapansili. Chifukwa chake ndi kufuna kuthetsa nkhani yokhudza woyenera kulamulira anthu yomwe inayamba zaka zambiri m’mbuyomu. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti panopa dzikoli likulamuliridwa ndi Mdyerekezi osati Mulungu. (Luka 4:​1, 2, 6; Yohane 12:31) Ngakhale kuti nkhani zina zimene zili pa gawo lakuti “kuvutika” zimafotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti anthu azivutika, tiyeni tikambirane mfundo ziwiri za m’Baibulo. Mfundozi zitithandiza kudziwa chifukwa chake Mulungu analola kuti anthu ambirimbiri aphedwe mu ulamuliro wa Nazi ku Germany.

  1.   Anthu anagwiritsira ntchito ufulu wawo molakwika. Mulungu anauza Adamu ndi Hava malamulo amene ankafuna kuti azitsatira koma sanawakakamize kuti azimvera. Iwo anafuna kudziwa okha zinthu zabwino kapena zoipa ndipo zinthu zoipa zimene anasankha zinabweretsa mavuto ku mtundu wonse wa anthu. Masiku anonso zinthu zoipa zimene anthu amasankha kuchita zabweretsa mavuto osaneneka kwa anthu ambirimbiri. (Genesis 2:17; 3:6; Aroma 5:12) Zimenezi ndi zogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku limene limati: “Mavuto ambiri amene amachitika padzikoli amayamba chifukwa chakuti anthufe timagwiritsa ntchito molakwika ufulu wosankha zochita umene anthufe tinapatsidwa.” M’malo molanda anthu ufulu wosankha zinthu umene anawapatsa, Mulungu wapatsa anthu mpata woti ayese kuchita zinthu motsatira nzeru zawo.​—Statement of Principles of Conservative Judaism.

  2.   Mulungu ali ndi mphamvu zoukitsa anthu amene anaphedwa mu ulamuliro wa Nazi ku Germany. Mulungu analonjeza kuti adzaukitsa anthu mamiliyoni ambiri amene anamwalira, kuphatikizapo amene anaphedwa mu ulamuliro wa Nazi. Komanso adzathandiza anthu amene anapulumuka pa nkhanza za ulamuliro wa Nazi kuiwala zinthu zoopsa zimene zinachitika pa nthawiyo. (Yesaya 65:17; Machitidwe 24:15) Sitikayikira kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo amenewa chifukwa iye ndi wachikondi.​—Yohane 3:16.

 Anthu ambiri amene achibale awo anaphedwa komanso amene anapulumuka pa nkhanza za ulamuliro wa chipani cha Nazi akukwanitsa kukhulupirira Mulungu komanso amakhala mosangalala. Izi zatheka chifukwa amvetsa chifukwa chake Mulungu amalola zoipa kuchitika komanso mmene adzathetsere mavuto onse.