Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Uchigawenga Udzatha?

Kodi Uchigawenga Udzatha?

 Kukachitika zauchigawenga, mungadzifunse kuti: ‘Kodi Mulungu amatiganizira? N’chifukwa chiyani zinthu ngati zimenezi zimachitika? Kodi uchigawenga a udzatha? Kodi tingatani kuti ndisamachite mantha nthawi zonse?’ Baibulo limapereka mayankho abwino a mafunso amenewa.

Kodi Mulungu amaona bwanji uchigawenga?

 Mulungu amadana ndi zachiwawa komanso uchigawenga. (Salimo 11:5; Miyambo 6:16, 17) Ndipotu Yesu, yemwe amaimira Mulungu, anadzudzula ophunzira ake pamene anachita zachiwawa. (Mateyu 26:50-52) Ngakhale kuti anthu ena amanena kuti akuchita zachiwawa m’dzina la Mulungu, iye sasangalala ndi zimene akuchitazo. Mulungu samva ngakhale mapemphero awo.​—Yesaya 1:15.

 Mulungu amaganizira anthu onse amene akuvutika, kuphatikizapo amene akuvutika chifukwa cha zauchigawenga. (Salimo 31:7; 1 Petulo 5:7) Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu adzathetseratu zachiwawa.​—Yesaya 60:18.

N’chiyani chimachititsa zauchigawenga?

 Baibulo limasonyeza chimene chimachititsa kuti anthu azichita zauchigawenga. Limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Kuyambira kale, anthu audindo akhala akupondereza anthu ena powaopseza. Komanso anthu ena akaopsezedwa amabwezera pochita zauchigawenga.​—Mlaliki 7:7.

Kutha kwa uchigawenga

 Mulungu amalonjeza kuti adzathetsa chilichonse chochititsa mantha komanso zachiwawa ndipo adzabweretsa mtendere padzikoli. (Yesaya 32:18; Mika 4:3, 4) Iye adzachita zotsatirazi:

  •   Adzachotsa zimene zimachititsa zauchigawenga. Mulungu adzachotsa maboma a anthu n’kuika boma lake lolamulira dziko lonse. Wolamulira wa bomali, yemwe ndi Yesu Khristu, adzachitira aliyense zachilungamo ndipo adzathetsa kupondereza kulikonse komanso zachiwawa. (Salimo 72:2, 14) Pa nthawi imeneyo, palibe amene adzachite zauchigawenga. Anthu “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:10, 11.

  •   Kukonza zonse zimene zachitika chifukwa cha uchigawenga. Mulungu adzachiritsa anthu amene apwetekedwa ndi zauchigawenga ndipo adzawathandiza kuti asavutikenso mumtima mwawo. (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:3, 4) Iye amalonjezanso kuti ngakhale akufa adzawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi lamtendere.​—Yohane 5:28, 29.

 Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu adzachita zimenezi posachedwapa. Koma mwina mungadzifunse kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu sanathetse uchigawenga mpaka pano?’ Kuti mudziwe yankho lake, onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

a Nthawi zambiri mawu oti “uchigawenga” amanena za zimene anthu ena amachita poopseza anthu anzawo, makamaka anthu wamba, ndi zachiwawa n’cholinga choti asinthe zinthu pa nkhani ya ndale, chipembedzo kapena zinthu zina. Koma anthu angasiyane maganizo pa nkhani ngati zinthu zinazake zimene zachitika ndi zauchigawenga kapena ayi.