Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi mungatani kuti mukhale makolo abwino?

Kodi mumaphunzitsa ana anu kuti azikonda Mulungu?

Makolo akamakondana komanso kulemekezana, ana awo amakula bwino. (Akolose 3:14, 19) Makolo abwino amakonda ana awo komanso amawayamikira ngati mmene Yehova ankachitira ndi Mwana wake.—Werengani Mateyu 3:17.

Yehova, yemwe ndi Atate wakumwamba, amamvetsera atumiki ake ndipo amamvetsa mavuto awo. Inunso muyenera kutengera chitsanzo chake. Ana anu akamakuuzani zinazake, muyenera kumvetsera ngakhale mutakhala kuti simukugwirizana ndi zimene akunenazo. (Yakobo 1:19) Muyeneranso kuyesetsa kuti muzimvetsa mmene ana anuwo akumvera.—Werengani Numeri 11:11, 15.

Mungatani kuti ana anu akule bwino?

Makolonu muli ndi udindo wopatsa ana anu malamulo oti azitsatira. (Aefeso 6:1) Pa nkhani imeneyinso muyenera kutengera chitsanzo cha Yehova. Yehova amatikonda ndipo amatipatsa malamulo omveka bwino. Amatiuzanso zimene zingachitike tikapanda kutsatira malamulowo. (Genesis 3:3) Yehova satikakamiza kutsatira malamulo ake. Koma amatiuza kuti tikatsatira malamulowo, zinthu zidzatiyendera bwino.—Werengani Yesaya 48:18, 19.

Muziyesetsa kuthandiza ana anu kuti azikonda Mulungu. Zimenezi zingawathandize kuti azichita zabwino ngakhale inuyo kulibe. Mulungu amatiphunzitsa potipatsa chitsanzo. Nanunso muzisonyeza chitsanzo chabwino kuti ana anu aziphunzira mosavuta.—Werengani Deuteronomo 6:5-7; Aefeso 4:32; 5:1.