Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kupemphera N’kothandizadi?

Kodi Kupemphera N’kothandizadi?

Mwina mungafunse kuti, ‘Ngati Mulungu amadziwa chilichonse ngakhale zimene timaganiza komanso zofuna zathu, n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera?’ Funsolitu n’lomveka chifukwa Yesu ananena kuti Mulungu “amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:8) Mfumu Davide nayonso inkadziwa zimenezi, ndipo inalemba kuti: “Ndisananene kanthu, Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.” (Salimo 139:4) Ndiye n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kwa Mulungu? Kuti tipeze yankho la funso limeneli, tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mapemphero a anthu amene ankatumikira Mulungu. *

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”Yakobo 4:8

 PEMPHERO LIMATITHANDIZA KUYANDIKIRA MULUNGU

Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Yehova * Mulungu amadziwa chilichonse, limasonyezanso kuti cholinga chake si kungodziwa zinthu zokhudza atumiki ake basi. (Salimo 139:6; Aroma 11:33) Ngakhale kuti Yehova amatha kukumbukira chilichonse, sali ngati kompyuta imene imangosunga zinthu. Yehova amachita chidwi ndi zimene timaganiza chifukwa amafuna kuti timuyandikire. (Salimo 139:23, 24; Yakobo 4:8) N’chifukwa chake Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azipemphera, ngakhale kuti Atate wake amadziwa kale zimene timafunikira. (Mateyu 6:6-8) Tikamauza Mlengi wathu zimene zili mumtima mwathu, ndi pamenenso ubwenzi wathu ndi iye umalimba.

Nthawi zina sitidziwa zimene tinganene m’pemphero. Zikatere, Mulungu amatha kutithandiza ngakhale kuti zimene timafunazo sitinathe kuzifotokoza. (Aroma 8:26, 27; Aefeso 3:20) Nthawi zina Mulungu amayankha mapemphero athu m’njira yosaonekera. Tikazindikira kuti Mulungu watithandiza, timayamba kumuona kuti ndi bwenzi lathu lapamtima.

KODI MULUNGU AMAYANKHA MAPEMPHERO ONSE?

Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amayankha mapemphero a atumiki ake okhulupirika, koma limaperekanso zifukwa zimene sayankhira mapemphero ena. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Aisiraeli ankakonda kuchita zachiwawa. Mulungu anauza mneneri Yesaya kuti awauze kuti: “Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu sayankha mapemphero a anthu amene satsatira malangizo ake kapena amene amapemphera ali ndi zolinga zolakwika.—Miyambo 28:9; Yakobo 4:3.

Komanso Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye angapereke kwa atumiki ake chilichonse chimene apempha? Ayi. Mwachitsanzo, taganizirani za mtumwi Paulo, yemwe anapemphera kwa Mulungu katatu kuti amuchotsere “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7, 8) Zikuoneka kuti Paulo anali ndi vuto la maso. Zimenezi ziyenera kuti zinali zokhumudwitsa kwambiri kwa iye. Paulo anali ndi mphatso yochiritsa ndipo anaukitsapo wakufa. Koma ngakhale kuti anapemphera kangapo konse kuti Mulungu athetse vuto lakeli, Mulungu sanachite zimenezi. (Machitidwe 19:11, 12; 20:9, 10) Ngakhale kuti Mulungu sanayankhe mapemphero ake monga mmene iye ankafunira, Paulo analandira mosangalala thandizo limene Mulungu anamupatsa.—2 Akorinto 12:9, 10.

“Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”—1 Yohane 5:14

N’zoona kuti pa nthawi ina Mulungu anayankha mozizwitsa mapemphero a anthu ena otchulidwa m’Baibulo. (2 Mafumu 20:1-7) Komabe ngakhale pa nthawiyo, zimenezi sizinkachitikachika. Panalinso atumiki ena a Mulungu amene pa nthawi ina anakhumudwa chifukwa choona ngati Mulungu sakuyankha mapemphero awo. Mwachitsanzo popemphera, Mfumu Davide inafunsa Mulungu kuti: “Kodi mudzandiiwala kufikira liti, inu Yehova? Mpaka muyaya?” (Salimo 13:1) Koma munthu wokhulupirika ameneyu atazindikira kuti nthawi zambiri Yehova amamuthandiza akapemphera, anayambanso kumukhulupirira. M’pemphero lomweli iye ananenanso kuti: “Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.” (Salimo 13:5) Mofanana ndi Davide, atumiki a Mulungu nthawi zina amafunikanso kulimbikira kupemphera mpaka Mulungu atayankha pemphero lawolo.—Aroma 12:12.

 KODI MULUNGU AMAYANKHA BWANJI MAPEMPHERO?

Mulungu amatipatsa zinthu zimene tikufunikiradi.

Sikuti nthawi zonse makolo achikondi amapatsa ana awo chilichonse chimene anawo apempha pa nthawi imene akuchifuna. Makolo amachita zimenezi pa zifukwa zoyenera. Mofanana ndi zimenezi, sikuti nthawi zonse Mulungu angayankhe pemphero lathu mmene ifeyo tikufunira komanso pa nthawi yomwe tikufuna. Komabe tingakhale ndi chikhulupiriro choti Mlengi wathu, yemwe ali ngati bambo wachikondi, amatipatsa zinthu zomwe tikufunikiradi ndipo amachita zimenezi pa nthawi yoyenera komanso m’njira yabwino.—Luka 11:11-13.

Nthawi zina Mulungu angayankhe pemphero lathu kudzera pa zimene tingawerenge m’Baibulo

Mulungu angayankhe mapemphero athu m’njira imene sitingaizindikire.

Nanga kodi tingatani ngati tapemphera kuti Mulungu atithetsere vuto linalake koma vutolo silikutha? Kodi tiyenera kuganiza kuti popeza Mulungu sanatichitire chozizwitsa, ndiye kuti basi sanayankhe pemphero lathulo? Ayi. Chifukwa n’kutheka kuti watithandiza m’njira inayake koma ifeyo sitikuzindikira zimenezo. Mwachitsanzo pa nthawi imene tinkafunika thandizo, mwina mnzathu wina anatithandiza. (Miyambo 17:17) N’kutheka kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti mnzathuyo akhudzidwe mtima n’kutithandiza pa vuto lathu. Komanso nthawi zina Mulungu angayankhe pemphero lathu kudzera pa zimene tingawerenge m’Baibulo. Zingachitike kuti tingapeze mfundo inayake imene ingatithandize kuti tipirire mavuto amene tikukumana nawo.—2 Timoteyo 3:16, 17.

Mulungu angagwiritse ntchito anzathu apamtima kuti atithandize pa vuto lathu

Nthawi zambiri Mulungu sachotsa vuto la munthu, koma amangomupatsa mphamvu zoti athe kupirira vutolo. (2 Akorinto 4:7) Mwachitsanzo, Yesu atapempha Atate wake kuti amuchotsere vuto linalake poopa kuti linyozetsa dzina la Atate wakewo, Yehova anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse. (Luka 22:42, 43) Mofanana ndi zimenezi, Mulungu angagwiritsenso ntchito mnzathu wapamtima kuti atilimbikitse pa nthawi imene tili pa mavuto. (Miyambo 12:25) Popeza njira yoyankhira pemphero imeneyi, siyoonekera kwambiri, timafunika kukhala tcheru kuti tizindikire kuti Mulungu wayankha pemphero lathu, chifukwa kupanda kutero tingamaganize kuti sanayankhe.

Mulungu amayankha pa nthawi yoyenera.

Baibulo limanena kuti Mulungu Wamphamvuyonse amakomera mtima anthu odzichepetsa “m’nthawi yake.” (1 Petulo 5:6) Choncho zikamaoneka ngati Yehova akuchedwa kuyankha mapemphero athu ochokera pansi pa mtima, tisamaganize kuti ndi umboni woti Yehova sakudera nkhawa za mavuto athu. Koma tizidziwa kuti popeza Yehova amadziwa zonse, n’zosakayikitsa kuti amayankha mapemphero athu mogwirizana ndi zimene tikufunikiradi.

“Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.”—1 Petulo 5:6

Mwachitsanzo, yerekezani kuti mwana wanu wamng’ono wakupemphani kuti mum’gulire njinga. Kodi mungamugulire nthawi yomweyo? Ngati mukuona kuti sanafike pa msinkhu woti angakwere njinga, mwina simungamugulire pa nthawiyo. Komabe m’tsogolo mukhoza kudzamugulira ngati mukuona kuti kuchita zimenezi kumuthandiza. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu angatipatse ‘zokhumba za mtima wathu’ pa nthawi yoyenera ngati titapitirizabe kupemphera.—Salimo 37:4.

MUSAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMAMVA MAPEMPHERO

Baibulo limalimbikitsa Akhristu oona kuti asamakayikire zoti pemphero limathandiza. Koma ena anganene kuti zimenezi ndi zongonena koma sikuti zimachitikadi. N’zoona kuti ngati tapemphera kwa nthawi yaitali za vuto linalake kapena za zinthu zopanda chilungamo zomwe zikutichitikira, koma vutolo silikutha, tingayambe kuona kuti Yehova akuchedwa kuyankha. Koma tizikumbukira zoti Yesu ananena kuti tiyenera kupitirizabe kupemphera.

 Yesu ananena za fanizo la mkazi wamasiye amene ankapita mobwerezabwereza kwa woweruza kuti amuweruzire nkhani yake n’cholinga choti chilungamo chioneke. (Luka 18:1-3) Ngakhale kuti poyamba woweruzayu anakana, koma kenako anati: “Ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kumangobwera ndi kundisautsa kwambiri.” (Luka 18:4, 5) Mawu oyambirira amene anagwiritsa ntchito pamenepa, amasonyeza kuti woweruzayu anathandiza mkazi wamasiyeyo chifukwa “ankaopa kuti amuwonongera mbiri.” * Ndiye ngati woweruzayu, ngakhale kuti anali munthu wosakonda chilungamo, anathandiza mkazi wamasiyeyu chifukwa choopa kuti mbiri yake iwonongeka, kuli bwanji Mulungu yemwe ndi wachikondi? Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene “amafuulira kwa iye usana ndi usiku.” Monga Yesu ananenera, Mulungu “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.”—Luka 18:6-8.

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”—Luka 11:9

Ngakhale titapemphera kwa nthawi yaitali kuti Mulungu atithandize pa vuto linalake, koma tikuonabe kuti vutolo silikutha, sitiyenera kusiya. Tikamalimbikira kupemphera, timasonyeza kuti tikufunadi kuti Mulungu atichitire zimene tikupemphazo. Komanso tikaona mmene Mulungu wayankhira pemphero lathu, timayamba kumudalira ndipo timamuona kuti ndi bwenzi lathu. Choncho sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzayankha mapemphero athu oyenera ngati tipitirizabe kupempha ndi chikhulupiriro.—Luka 11:9.

^ ndime 3 Ngati tikufuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kuyesetsa kuchita zimene iye amafuna. Tikamachita zimenezi, tidzaona kuti pemphero lingatithandizedi monga mmene tionere m’nkhani ino. Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 5 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 22 Kale mu Isiraeli, Mulungu ankafuna kuti oweruza azisonyeza chifundo makamaka kwa akazi amasiye ndi ana amasiye.—Deuteronomo 1:16, 17; 24:17; Salimo 68:5.