Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ankagwiritsa Ntchito Baibulo Poyankha Funso Lililonse

Ankagwiritsa Ntchito Baibulo Poyankha Funso Lililonse
  • CHAKA CHOBADWA: 1950

  • DZIKO: SPAIN

  • POYAMBA: NDINALI SISITERE WAKATOLIKA

KALE LANGA:

Pa nthawi yomwe ine ndinabadwa, makolo anga anali ndi famu yaing’ono kumudzi wina wotchedwa Galicia, kumpoto chakumadzulo kwa Spain. M’banja mwathu tilipo ana 8 ndipo ine ndine wa 4. Banja lathu linali losangalala kwambiri. Pa nthawi imeneyo, mabanja ambiri a ku Spain ankakonda kutumiza mwana mmodzi kapena awiri kusukulu yachikatolika yophunzitsa usisitere. M’banja mwathu atsikana atatu tinasankha zokhala masisitere.

Ndili ndi zaka 13, ndinapita kukakhala pamalo ena a masisitere ku Madrid, komwenso mkulu wanga anali. Koma pamalowa aliyense ankangochita zake. Anthu sankachezerana ndipo tsiku lililonse tinkangokhalira kupemphera. Pamalowa panalinso malamulo ambirimbiri amene tinkafunika kuwatsatira ndipo zinthu sizinkayenda bwino chifukwa cha mavuto azachuma. M’mawa uliwonse tinkasonkhana m’tchalitchi kuti tizisinkhasinkha ngakhale kuti ine pa nthawiyi palibe chilichonse chimene ndikanachisinkhasinkha. Kenako tinkaimba nyimbo zachipembedzo komanso kuchita mwambo wa Misa ndipo zonsezi zinkachitika m’Chilatini. Palibe chimene ndinkatolapo ndipo zonsezi sizinkandithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Panalibe munthu amene anali mnzanga wapamtima. Ngakhale ndikakumana ndi mchemwali wanga, sitinkacheza kapena kuuzana nkhani. Tinkangolonjerana ponena mawu akuti: “Tikuoneni Mariya Woyera.” Masisitere ankangotilola kulankhula kwa mphindi 30 basi tikamaliza kudya. Moyo wa pamalowa unali wosasangalatsa, wosiyana kwambiri ndi mmene tinkakhalira kwathu. Ndinkasowa wocheza naye ndipo nthawi zambiri ndinkalira.

Ndinakhala sisitere ndili ndi zaka 17. Komabe ndinkaona zoti sindinali pa ubwenzi ndi Mulungu. Kunena zoona ndinkangochita zimenezi chifukwa n’zimene makolo anga ankafuna, moti pasanapite nthawi ndinayamba kukayikira ngati ndinachita kuitanidwadi ndi Mulungu kuti ndikhale sisitere. Masisitere ankandiuza kuti munthu amene amakhala ndi maganizo amenewa adzapsa kumoto. Ngakhale ankandiopseza chonchi, ndinapitirizabe kukhala ndi maganizo amenewa. Ndinkadziwa kuti Yesu Khristu sankadzipatula koma ankatanganidwa ndi ntchito yothandiza anthu komanso kuwaphunzitsa. (Mateyu 4:23-25) Ndili ndi zaka 20, ndinayamba kuona kuti palibe chifukwa choti ndipitirizebe kukhala sisitere. Ndinadabwa kwambiri sisitere wamkulu atandiuza kuti ngati ndikukayikira, kuli bwino ndizipita. Ndikuganiza kuti anandiuza zimenezi poopa kuti ndipangitsa kuti enanso ayambe kukayikira. Choncho ndinachokadi n’kupita kunyumba.

Nditafika kunyumba, makolo anga sanakhumudwe kuti ndasiya usisitere. Koma popeza sindinapeze ntchito, ndinasamukira  ku Germany komwe mchimwene wanga ankakhala. Iye anali m’gulu lina la anthu ochokera ku Spain omwe ankamenyera ufulu wa anthu apantchito komanso woti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo. Ndinkasangalala ndikakhala ndi anthu amenewa. Choncho nanenso ndinalowa m’gululi ndipo patapita nthawi ndinakwatiwa ndi munthu wina yemwe analinso m’gululi. Tinkagawa mabuku a gulu lathu komanso kuchita zionetsero ndipo ndinkaona kuti ndikuchita zinthu zothandiza.

Komabe, m’kupita kwa nthawi ndinaona kuti gululi ndi losathandiza chifukwa nthawi zambiri silinkachita zimene linkanena. Maganizo oona kuti gululi ndi losathandiza anakula mu 1971, pamene anyamata ena a m’gulu lathu anawotcha ofesi ya kazembe wa ku Spain ku Frankfurt. Iwo anachita zimenezi chifukwa ankaona kuti ulamuliro wa dziko la Spain unali wopanda chilungamo komanso wankhanza. Koma ndinaona kuti imeneyi si njira yabwino yosonyezera kuti sitikugwirizana ndi zomwe zikuchitika.

Mwana wathu woyamba atabadwa, ndinauza mwamuna wanga kuti ndisiya kupita kumisonkhano ya gulu limeneli. Zitatere, ndinkasowa wocheza naye chifukwa anzanga anasiya kubwera kudzandiona kapena kudzaona mwana wanga. Ndinkadzifunsa kuti Mulungu anatilengeranji anthufe ndipo ndinayamba kukayikira ngati anthufe tingakwanitsedi kusintha zinthu padzikoli.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Mu 1976, a Mboni awiri a ku Spain anabwera pakhomo pathu ndipo anandipatsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Atabweranso, ndinayamba kuwafunsa mafunso ambirimbiri okhudza chifukwa chimene anthufe timavutikira, ufulu wa azimayi komanso chifukwa chake padzikoli palibe chilungamo. Ndinadabwa kwambiri chifukwa anagwiritsa ntchito Baibulo kuyankha mafunso anga onse. Ndinavomera kuti ndiyambe kuphunzira nawo Baibulo.

Poyamba cholinga changa chinali kungofuna kudziwa zambiri basi. Koma zinthu zinasintha pamene ine ndi mwamuna wanga tinayamba kusonkhana ndi a Mboni ku Nyumba ya Ufumu. Pa nthawiyi n’kuti tili ndi ana awiri. A Mboni ankatitenga popita kukasonkhana komanso ankatithandiza kusamalira ana athu tikakhala kumeneko, ndipo chifukwa cha zimenezi ndinayamba kuwakonda kwambiri.

Komabe panali zinthu zina zokhudza chipembedzo zomwe ndinkazikayikirabe. Ndinaganiza zopita ku Spain kukaona makolo. Kumeneko, bambo anga aang’ono, omwe anali wansembe, anandiuza kuti ndisiye kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma a Mboni a ku Spain anandithandizanso kwambiri. Nawonso anagwiritsa ntchito Baibulo kuyankha mafunso anga onse ngati mmene anachitira a ku Germany aja. Ndinaganiza kuti ndikabwerera ku Germany, ndikayambiranso kuphunzira Baibulo. Ngakhale kuti mwamuna wanga anasiya kuphunzira, ine nditabwerera ku Germany, ndinayambiranso kuphunzira Baibulo. Mu 1978, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Kudziwa zolondola zimene Baibulo limaphunzitsa kwandithandiza kudziwa chifukwa chake Mulungu anatilenga. Kwandithandizanso kupeza malangizo abwino othandiza pa moyo wanga. Mwachitsanzo, lemba la 1 Petulo 3:1-4 limalangiza akazi kuti ‘azigonjera’ amuna awo, aziwalemekeza kwambiri, komanso azikhala ndi ‘mzimu wofatsa umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.’ Mfundo imeneyi yandithandiza kukhala mkazi wabwino komanso mayi wabwino.

Tsopano patha zaka 35 kuchokera pamene ndinakhala wa Mboni. Ndimasangalala kutumikira Mulungu limodzi ndi a Mboni anzanga. Ndili ndi ana 5 ndipo ndine wosangalalanso kuti ana anga 4 ndi a Mboninso.