Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ndinayamba Kuganizira Kwambiri za Moyo Wanga”

“Ndinayamba Kuganizira Kwambiri za Moyo Wanga”
  • CHAKA CHOBADWA: 1941

  • DZIKO: AUSTRALIA

  • POYAMBA: NDINKASUTA FODYA NDI KUMWA MOWA KWAMBIRI

KALE LANGA:

Ndinakulira ku Warialda, tauni yaing’ono yomwe ili ku New South Wales. Anthu a ku Warialda amaweta nkhosa, ng’ombe komanso amalima tirigu ndi mbewu zina. Tauniyi ndi yabata chifukwa anthu sakonda kuchita zachiwawa.

M’banja mwathu munali ana 10, ndipo ineyo ndinali woyamba. Ndili ndi zaka 13, ndinayamba kugwira ntchito kuti ndizithandiza kusamalira banja lathu. Chifukwa chakuti sindinaphunzire kwambiri sukulu ndinkagwira ntchito kufamu. Ndili ndi zaka 15, ndinayamba kugwira ntchito yoweta mahatchi.

Kugwira ntchito kufamu kunali ndi ubwino komanso mavuto ake. Ubwino wake unali wakuti ntchitoyo inkandisangalatsa chifukwa ndinkakonda kugona kutchire, kuona nyenyezi ndi mwezi usiku komanso ndinkasangalala kumva fungo la maluwa onunkhira a m’tchire. Ndikamaona zimenezi ndinkaganiza zoti pali winawake amene analenga zinthu zonsezi. Koma kugwira ntchitoyi kunandipangitsa kuti nditengere makhalidwe ena oipa. Nthawi zambiri anthu amene ndinkagwira nawo ntchito ankakonda kutukwana komanso kusuta fodya. Zimenezi zinachititsa kuti nditengere makhalidwe amenewa.

Nditakwanitsa zaka 18, ndinasamukira ku Sydney. Ndinkafuna kulowa usilikali koma zinakanika chifukwa chakuti sindinaphunzire kwambiri sukulu. Ndinapeza ntchito ina ndipo ndinakhala ku Sydney chaka chimodzi. Nthawi imeneyi ndi imene ndinakumana koyamba ndi a Mboni za Yehova. Anandiitanira ku misonkhano yawo ndipo nditapita ndinazindikira kuti amaphunzitsa zoona.

Komabe patapita nthawi, ndinaganiza zokayambiranso ntchito yoweta mahatchi. Ndinasamukira ku tauni ya Goondiwindi, ku Queensland. Nditafika kumeneko ndinapeza ntchito koma ndinayamba kumwa mowa.

Ndinakwatira ndipo ndinakhala ndi ana aamuna awiri. Anawo atabadwa ndinayamba kuganizira kwambiri za moyo wanga.  Ndinakumbukira zimene ndinamva pamsonkhano wa Mboni za Yehova ku Sydney, ndipo ndinaona kuti ndikufunika kusintha zinthu zina pa moyo wanga.

Ndinapeza magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe inali ndi adiresi ya ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Australia. Ndinatumiza kalata yopempha kuti munthu wina adzandithandize ndipo pasanapite nthawi yaitali, munthu wina wa Mboni anabwera n’kuyamba kundiphunzitsa Baibulo. Munthuyo anali wachifundo komanso wachikondi.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinaona kuti ndikufunika kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Lemba limene linandikhudza kwambiri ndi la 2 Akorinto 7:1. Lembali limatilimbikitsa kuti: “Tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”

Ndinaganiza zosiya kusuta fodya ndi kumwa mowa kwambiri. Zinali zovuta kwambiri kusintha chifukwa ndinali nditazolowera kuchita zimenezi kwa nthawi yaitali. Koma ndinkafunitsitsa kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Mfundo imene inandithandiza kwambiri ndi imene imapezeka pa lemba la Aroma 12:2, yomwe imati: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusintha makhalidwe anga oipa, ndikufunika ndiyambe kusintha mmene ndimaganizira, n’kuyamba kuona makhalidwe oipawo mmene Mulungu amawaonera. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisiye kusuta fodya komanso kumwa mowa kwambiri.

“Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusintha makhalidwe anga oipa, ndikufunika ndiyambe kusintha mmene ndimaganizira”

Koma ndinavutika kwambiri kuti ndisiye kutukwana. Ndinkadziwa ndithu malangizo a m’Baibulo omwe ali pa Aefeso 4:29, omwe amati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” Komabe sindinasiyiretu kutukwana. Kenako ndinaona kuti kuganizira kwambiri lemba la Yesaya 40:26 kungandithandize. Lembali limanena za nyenyezi zakumwamba. Limati: “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake. Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa, ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa.” Ndinayamba kuganiza kuti ngati Mulungu ali ndi mphamvu zomwe analengera chilengedwe chonse, sangalephere kundipatsa mphamvu zomwe zingandithandize kuti ndizichita zinthu zomukondweretsa. Ndinkayesetsa kuchita khama komanso kupemphera ndipo kenako ndinasiyiratu kutukwana.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Poyamba sindinkakonda kucheza ndi anthu chifukwa kufamu kumene ndinkagwira ntchito kuja kunali anthu ochepa. Koma chifukwa cha zimene ndaphunzira ku misonkhano ya Mboni za Yehova, ndimatha kucheza ndi anthu. Zimenezi zandithandizanso kuti ndiziuza anthu ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:9, 10; 24:14.

Tsopano ndakhala ndikutumikira monga mkulu mu mpingo kwa zaka zingapo. Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza Akhristu anzanga m’njira zosiyanasiyana. Koma phindu lalikulu limene ndapeza ndi lakuti panopa ndikutumikira Yehova limodzi ndi mkazi wanga komanso ana anga.

Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondiphunzitsa, ngakhale kuti sindinaphunzire kwambiri sukulu. (Yesaya 54:13) Ndimaona kuti mawu a pa Miyambo 10:22, ndi oona. Mawuwa amati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa.” Ineyo ndi banja langa tikufunitsitsa kupitirizabe kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso kumutumikira mpaka kalekale.