Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinali Mnyamata Wovuta Komanso Wokonda Ndewu

Ndinali Mnyamata Wovuta Komanso Wokonda Ndewu
  • CHAKA CHOBADWA: 1974

  • DZIKO: MEXICO

  • POYAMBA: NDINALI MNYAMATA WOVUTA KOMANSO WOKONDA NDEWU

KALE LANGA:

Ndinabadwira mumzinda wa Ciudad Mante womwe uli m’chigawo cha Tamaulipas ku Mexico. Anthu ambiri amumzindawu amakonda kuthandizana ndiponso kugawana zinthu. Koma nthawi imeneyo mzindawu unali woopsa kwambiri chifukwa kunali magulu a zigawenga.

M’banja lathu munali ana 4, anyamata okhaokha, ndipo ine ndinali wachiwiri. Makolo anga anali akatolika ndipo anachititsa kuti nanenso ndibatizidwe m’chipembedzochi. Patapita nthawi, ndinayamba kuimba nawo kwaya kuparishi. Ndinkafuna kusangalatsa Mulungu chifukwa ndinkaopa kuti ndikapanda kutero angadzandiwotche kumoto kwamuyaya.

Ndili ndi zaka 5, bambo anga anangochoka pakhomo. Izi zinandipweteka kwambiri ndipo ndinkadziona ngati wosafunika. Tinkawakonda kwambiri ndipo sindinkamvetsa kuti anatithawa chifukwa chiyani. Mayi anga ankayenera kugwira ntchito kwambiri kuti akwanitse kutisamalira ndipo nthawi zambiri sankapezeka pakhomo.

Ndinkapezerapo mwayi wojomba kusukulu n’kumakacheza ndi achinyamata ena amene anali aakulu kuposa ineyo. Anandiphunzitsa kutukwana, kusuta, kuba ndiponso kuchita ndewu. Ndinkafuna kuti anthu azindiopa, choncho ndinaphunzira masewera a nkhonya, karate ndiponso kugwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana. Ndinayamba kukonda kwambiri ndewu. Ndipo nthawi zambiri tinkawomberana ndi anthu moti maulendo angapo anthuwo ankaganiza kuti ndafa. Ankandisiya mumsewu ndili thapsa, nditasamba magazi. Amayi anga ankandidandaula kwambiri akandipeza choncho ndipo ankanditenga n’kuthamangira nane kuchipatala.

Ndili ndi zaka 16, kunyumba kwathu kunabwera mnzanga wina amene tinkasewera limodzi tili ana ndipo ankafuna kutiuza uthenga wofunika kwambiri. Dzina lake anali Jorge ndipo anatiuza kuti tsopano ndi wa Mboni za Yehova. Iye anayamba kutifotokozera zimene amakhulupirira ndipo anachita zimenezi pogwiritsa ntchito Baibulo. Ndinali ndisanawerengepo Baibulo ndipo ndinasangalala kwambiri kudziwa dzina la Mulungu ndiponso zimene amafuna. Jorge ananena kuti akhoza kumaphunzira nafe Baibulo ndipo tinavomera.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Ndinasangalala kwambiri nditadziwa kuti Baibulo siliphunzitsa kuti anthu oipa adzakawotchedwa kumoto. (Salimo 146:4; Mlaliki 9:5) Zimenezi zinandithandiza kuti ndisiye kuona kuti Mulungu ndi woopsa. M’malomwake ndinayamba kuona kuti Mulungu ndi Atate wachikondi amene amafunira zabwino ana ake.

Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndinayamba kuona kuti ndikufunika kusintha khalidwe langa. Ndinkafunika kukhala wodzichepetsa komanso kusiya khalidwe lokonda ndewu. Lemba limene linandithandiza ndi la 1 Akorinto 15:33, lomwe limanena kuti kugwirizana ndi anthu oipa “kumawononga makhalidwe abwino.” Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusintha khalidwe langa, ndiyenera kusiya kugwirizana ndi anthu amakhalidwe oipa. Choncho ndinayamba kugwirizana ndi a Mboni za Yehova chifukwa ankagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothetsa kusamvana, m’malo momenyana.

Lemba lina limene linandithandiza ndi la Aroma 12:17-19. Lembali limati: “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. . . . Musabwezere choipa . . . Pakuti Malemba amati: ‘“Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,” watero Yehova.’” Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti Yehova adzathetsa zinthu zopanda chilungamo pa nthawi yake ndiponso m’njira yabwino. Patapita nthawi ndinasiya kukonda ndewu.

Sindidzaiwala zimene zinachitika tsiku lina madzulo ndikupita kunyumba. Gulu la anyamata omwe ankakonda kulimbana ndi gulu lathu anayamba kundimenya ndipo mtsogoleri wawo anandimenya kumsana n’kunena kuti, “Bwanji sukubwezera?” Ndinapemphera kwa Yehova mwachidule kuti andithandize kupirira. Ngakhale kuti ndinkafunitsitsa kubwezera, ndinakwanitsa kuthawa. Tsiku lotsatira ndinakumana ndi mtsogoleri wawo uja ali yekha. Nditamuona ndinkafuna kuti ndibwezere zimene anandichita koma ndinapempheranso chamumtima kuti Yehova andithandize kuugwira mtima. Koma ndinadabwa kuona kuti anabwera pafupi n’kundiuza kuti: “Undikhululukire chifukwa cha zimene zinachitika dzulo zija. Inenso ndikufuna nditakhala ngati iweyo. Ndikufuna kuphunzira Baibulo.” Ndinasangalala kwambiri kuti ndinakwanitsa kuugwira mtima chifukwa zinathandiza kuti nayenso ayambe kuphunzira Baibulo.

N’zomvetsa chisoni kuti achibale anga ena sanapitirize kuphunzira Baibulo pa nthawiyo. Koma ine ndinatsimikiza mtima kuti sindisiya kuphunzira Baibulo zivute zitani. Ndinkadziwanso kuti kusonkhana ndi anthu a Mulungu kungandithandize kukhala ndi mtendere wamumtima komanso kupeza anzanga omwe angakhale ngati achibale anga. Ndinapitiriza kusintha khalidwe langa ndipo mu 1991, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Poyamba ndinali waukali, wovuta ndiponso wokonda ndewu. Koma Mawu a Mulungu anandithandiza kuti ndisinthiretu khalidwe langa. Panopa ndimakonda kuuza anthu uthenga wamtendere umene uli m’Baibulo. Kwa zaka 23 ndakhala ndikugwiritsa ntchito nthawi yanga yambiri polalikira uthenga umenewu.

Pa nthawi ina ndinkagwira ntchito yongodzipereka ku ofesi ya Mboni za Yehova, ku Mexico. Ndili kumeneko, ndinakumana ndi mtsikana wina dzina lake Claudia amene anandisangalatsa, ndipo tinakwatirana mu 1999. Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa mkazi wokhulupirika ameneyu.

Tinali mumpingo wa chinenero chamanja cha ku Mexico ndipo tinkathandiza anthu omwe anali ndi vuto losamva kuti aphunzire za Yehova. Kenako tinapemphedwa kuti tisamukire m’dziko la Belize kuti tizikaphunzitsa Baibulo anthu am’dzikolo. Panopa tikutumikirabe kuno ku Belize. Ngakhale kuti tilibe zinthu zambiri, ndife osangalala chifukwa tili ndi zonse zofunika pa moyo ndipo sitinong’oneza bondo chifukwa chobwera kuno.

Patapita nthawi, mayi anga anayambiranso kuphunzira Baibulo ndipo kenako anabatizidwa. Nayenso mchimwene wanga wamkulu, mkazi wake ndiponso ana awo awiri panopa ndi a Mboni za Yehova. Anzanga enanso akale omwe ndinawauza uthenga wa Ufumu wa Mulungu panopa anayamba kutumikira Yehova.

Ndimamva chisoni kuti anthu ena a m’banja lathu anamwalira chifukwa cholephera kusiya khalidwe lokonda ndewu. Inenso ndikanapanda kusintha bwenzi nditafa. Panopa ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza kuti ndimudziwe ndiponso kuti ndikumane ndi atumiki ake omwe anandiphunzitsa moleza mtima komanso mwachikondi mmene ndingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wanga.