Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndili ndi mkazi wanga Tabitha, tikulalikira

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu

Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu
  • CHAKA CHOBADWA: 1974

  • DZIKO: GERMAN DEMOCRATIC REPUBLIC

  • POYAMBA: ANKAKHULUPIRIRA KUTI KULIBE MULUNGU

KALE LANGA

Ndinabadwira m’mudzi wotchedwa Saxony, m’dziko limene pa nthawiyo linkatchedwa German Democratic Republic. Banja lathu linali labwino komanso lokondana ndipo makolo anga ankandiphunzitsa makhalidwe abwino. Dziko la German Democratic Republic linali lachikomyunizimu. Choncho anthu ambiri a m’tauni yakwathu sankaona kuti kukhala ndi chipembedzo n’kofunika. Ndipo ine ndinkakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Kuyambira ndili mwana mpaka ndili ndi zaka 18, ndinkatsatira mfundo zachikomyunizimu komanso mfundo yoti kulibe Mulungu.

Ndinkakonda Chikomyunizimu chifukwa chinkanena kuti anthu onse ndi ofanana. Komanso ndinkakhulupirira kuti zinthu monga malo, ziyenera kumagawidwa mofanana kwa anthu onse. Ndinkaona kuti zimenezi zingathandize kuti pasamakhale olemera kwambiri kapena osauka kwambiri. Choncho ndinkagwira ntchito m’bungwe lina la achinyamata lomwe linkalimbikitsa mfundo zachikomyunizimu. Ndili ndi zaka 14 ndinkakonda kugwira ntchito yopanga zinthu kuchokera ku mapepala amene atayidwa. Akuluakulu a m’tauni ya Aue anasangalala kwambiri ndi zimene ndinkachitazi moti anandipatsa mphoto. Zimenezi zinachititsa kuti ndidziwane ndi akuluakulu a ndale ngakhale kuti ndinali ndidakali wachinyamata. Ndinkaona kuti ndikuchita zoyenera ndipo tsogolo langa ndi lowala.

Koma mwadzidzidzi zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wanga. Mu 1989 mpanda wa Berlin unagwetsedwa ndipo dziko la East Germany ndi la West Germany, linakhalanso dziko limodzi. Pa nthawiyi Chikomyunizimu chinatha mphamvu. Pasanapite nthawi ndinazindikira kuti m’boma la German Democratic Republic munkachitika zinthu zambiri zopanda chilungamo. Mwachitsanzo, anthu amene sankatsatira mfundo zachikomyunizimu ankaonedwa kuti ndi anthu wamba. Ndiye ndinkadzifunsa kuti, ‘Zikutheka bwanji? Si paja amene timatsatira Chikomyunizimufe timati anthu onse ndi ofanana? Kodi anthu achikomyunizimu amangonena mfundo zawo pakamwa koma osamachita zomwe amanenazo?’ Zimenezi zinachititsa kuti ndizikhala wosasangalala.

Choncho ndinasiya kukonda Chikomyunizimu ndipo ndinayamba kuphunzira kuimba komanso kujambula zithunzi pamanja. Ndinkaphunzira kuimba nyimbo pasukulu ina ndipo ndinali ndi cholinga choti ndidzapite kuyunivesite kenako n’kukhala woimba komanso katswiri wojambula. Pa nthawiyi ndinasiya kutsatira makhalidwe abwino amene makolo anga anandiphunzitsa aja. Ndinkaona kuti chofunika kwambiri ndi kusangalala ndipo ndinali ndi zibwenzi zingapo. Koma kuimba, luso lojambula komanso moyo wotayirira sizinandithandize kuthetsa nkhawa zanga. Ndipotu zithunzi zimene ndinkajambula zinkachita kuonetseratu kuti ndinali wamantha komanso wankhawa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi munthune ndili ndi tsogolo lotani? Kodi cholinga cha moyo wanga n’chiyani?’

Koma kenako ndinapeza mayankho a mafunso anga, ndipo mayankhowo anandidabwitsa kwambiri. Zimene zinachitika ndi zoti, tsiku lina ndili kusukulu ndinkakambirana ndi ophunzira ena zokhudza zimene munthu angachite kuti akhale ndi tsogolo labwino. Mmodzi mwa ophunzirawo anali mtsikana wina dzina lake Mandy * ndipo anali wa Mboni. Zimene anandiuza pa tsikuli zinandithandiza kwambiri. Anati: “Andreas, ngati ukufuna kudziwa zimene ungachite kuti ukhale ndi tsogolo labwino, ukawerenge bwinobwino Baibulo.”

Ndinaganizadi zokawerenga Baibulo ngakhale kuti ndinkakayikira zoti lingandithandize. Mandy anandiuza kuti ndikawerenge Danieli chaputala 2 ndipo zimene ndinawerengazo zinandikhudza mtima kwambiri. Ulosi wopezeka m’chaputala chimenechi umanena za maulamuliro amphamvu padziko lonse, omwe akhalapo mpaka nthawi yathu ino. Mandy anandisonyezanso maulosi ena a m’Baibulo amene amanena za tsogolo la anthu. Apa tsopano ndinapeza mayankho a mafunso anga. Koma ndinkadzifunsa kuti, ‘Maulosiwa amanena zolondola za m’tsogolo, ndiye ndi ndani analemba maulosi amenewa? Kodi n’kutheka kuti kunja kuno kulidi Mulungu?’

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

Mandy anauza a Horst ndi akazi awo a Angelika kuti aziphunzira nane Baibulo. Banja limeneli linandithandiza kwambiri kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Pasanapite nthawi ndinazindikira kuti a Mboni za Yehova okha ndi amene amakonda kutchula dzina la Mulungu lakuti, Yehova komanso amathandiza ena kudziwa dzinali. (Salimo 83:18; Mateyu 6:9) Ndinaphunziranso kuti Yehova anakonza njira yoti anthu omvera adzakhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. Lemba la Salimo 37:9 limati: “Oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi.” Zinandisangalatsa kwambiri nditadziwa kuti munthu aliyense amene amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, angathe kudzakhala ndi moyo wosatha.

Komabe ndinavutika kuti ndisinthe moyo wanga kuti uzigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndinali wotchuka kwambiri chifukwa cha kuimba komanso luso lojambula, ndipo izi zinachititsa kuti ndikhale wonyada. Choncho ndinafunika kuphunzira kukhala wodzichepetsa. Komanso zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye khalidwe langa lachiwerewere lija. Ndimathokoza kwambiri kuti Yehova ndi woleza mtima, wachifundo komanso amawamvetsa anthu amene akuyesetsa kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kuyambira ndili mwana mpaka ndili ndi zaka 18, ndinkatsatira mfundo zachikomyunizimu komanso ndinkakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Koma kuyambira ndili ndi zaka 18 mpaka pano, Baibulo lakhala likusintha moyo wanga. Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinathetsa nkhawa zokhudza tsogolo langa. Zinandithandizanso kuti ndidziwe cholinga cha moyo wanga. Mu 1993, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo mu 2000 ndinakwatirana ndi Tabitha, yemwenso ndi wa Mboni. Timatha nthawi yambiri tikuthandiza ena kuti adziwe zimene Baibulo limaphunzitsa. Anthu ambiri amene timakumana nawo sakhulupirira kuti kuli Mulungu ndipo anali achikomyunizimu ngati mmene zinalili ndi ineyo.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

Nditayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova, makolo anga anakhumudwa kwambiri. Komabe kenako anazindikira kuti kusonkhana ndi a Mboni kunandithandiza kuti ndisinthe khalidwe langa. Ndimasangalala kwambiri chifukwa panopa makolo angawa akuphunzira Baibulo komanso amasonkhana ndi a Mboni za Yehova.

Ine ndi mkazi wanga Tabitha tili ndi banja labwino kwambiri chifukwa timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo. Mwachitsanzo, kukhala okhulupirika m’banja kwatithandiza kuti tikhale ndi banja lolimba.​—Aheberi 13:4.

Panopa sindikhalanso ndi nkhawa za tsogolo langa. Ndimaona kuti ndili m’gulu lapadziko lonse la abale ndi alongo, omwe ndi anthu a mtendere komanso ogwirizana kwambiri. M’gulu limeneli timaona kuti palibe woposa mnzake. Mfundo imeneyi ndi imene ndakhala ndikukhulupirira kuyambira kale ndipo ndinkalakalaka nditapeza gulu limene limaitsatira.

^ ndime 12 Dzina lasinthidwa.