Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Norway

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Norway

ZAKA zochepa zapitazo, m’bale wina dzina lake Roald ndi mkazi wake Elsebeth ankakhala moyo wabwino ku Bergen, womwe ndi mzinda wina waukulu ku Norway. Pa nthawiyo, iwo anali ndi zaka zoposa 45. Iwo limodzi ndi ana awo, Isabel ndi Fabian, ankatumikira mokhulupirika mu mpingo. Roald anali mkulu ndipo Elsebeth anali mpainiya, pamene Isabel ndi Fabian anali ofalitsa akhama.

Koma mu September 2009, iwo anaganiza zokatumikira kudera lakutali kwa mlungu umodzi. Choncho Roald, Elsebeth ndi Fabian, yemwe anali ndi zaka 18, anapita kumpoto kwambiri kudera la Finnmark, m’chigawo cha m’mphepete mwa nyanja cha Nordkyn. Iwo anali kulalikira kumudzi wa Kjøllefjord limodzi ndi abale ndi alongo ena amene anapitanso kudera limeneli kukathandiza ntchito yolalikira. Roald anati: “Kumayambiriro kwa mlunguwu, ndinasangalala kwambiri kuti ndakwanitsa kukonza zinthu n’cholinga choti ndikhale ndi mpata wodzatumikira kuno kwa mlungu wonse.” Koma mlunguwu usanathe, zinthu zinasintha. Kodi zinasintha bwanji?

 ANAPEMPHEDWA MOSAYEMBEKEZEREKA

Roald anafotokoza kuti: “Mosayembekezereka, mpainiya wina yemwe ankatumikira ku Finnmark, dzina lake Mario, anatipempha ngati tingakonde kukatumikira mu mpingo wa m’tauni ya Lakselv, womwe unali ndi ofalitsa okwana 23.” Roald atamva zimenezi, anasowa chonena chifukwa si zimene ankayembekezera. Iye anati: “N’zoona kuti ine ndi Elsebeth tinaganizapo zosamukira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri. Komabe tinkati tidzachita zimenezi ana athu akadzakula n’kuchoka panyumba.” Kwa masiku ochepa amene Roald analalikira kudera lakutalili, anaona kuti anthu ankafuna kuphunzira za Yehova ndipo ankafunikira kuwathandiza pa nthawiyo osati m’tsogolo. Roald anati: “Ndinkaganizira kwambiri zimene tinapemphedwazo ndipo chikumbumtima changa chinkandivutitsa moti ndinkalephera kugona bwinobwino kwa masiku angapo.” Kenako Mario anapita ndi Roald ndi banja lake kutauni ya Lakselv, yomwe ili pa mtunda wa makilomita 240 kum’mwera kwa mudzi wa Kjøllefjord. Mario ankafuna kuti Roald ndi banja lake akaone okha mpingo waung’onowo.

Atafika ku Lakselv, mmodzi wa akulu awiri a mu mpingowo dzina lake Andreas anasonyeza Roald ndi banja lake Nyumba ya Ufumu ndiponso dera lozungulira. Anthu a mu mpingowo anawalandira bwino ndipo anauza Roald ndi Elsebeth kuti angasangalale kwambiri ngati atasamukira kumeneko kukathandiza pa ntchito ya Ufumu. Andreas anawauza kuti anali atakonza kale kumene Roald ndi Fabian angapite kukafunsira ntchito. Kodi Roald ndi banja lake anasankha kuchita chiyani?

ANAYENERA KUSANKHA ZOCHITA

Poyamba, Fabian sankafuna kusamukira kumeneko. Iye sankafuna kusiya anzake apamtima amene anakula nawo limodzi mu mpingo wa kwawo komanso sankafuna kukhala m’tauni yaing’ono. Iye analinso asanamalize maphunziro ake a zamagetsi. Koma Isabel, yemwe anali ndi zaka 21, atafunsidwa maganizo ake pa nkhaniyi, anayankha mosangalala kuti: “Ndakhala ndikufuna kuchita zimenezi kuyambira kalekale.” Kenako, Isabel anati: “Koma ndikayamba kuganiza kwambiri za nkhaniyi, ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi ndi nzerudi kuchita zimenezi? Koma ndisiyedi anzanga? Kapena kodi ndi bwino kungokhalabe mu mpingo wa kwathu chifukwa kuno zinthu n’zosavuta komanso ndazizolowera?’” Koma kodi Elsebeth anati chiyani? Iye anati: “Ndinkaona kuti Yehova wapatsa banja lathu ntchito. Koma ndinkaganizanso za nyumba yathu imene tinali titangoikonza kumene ndiponso katundu amene tinasonkhanitsa pa zaka 25.”

Elsebeth ndi Isabel

Roald ndi banja lake atamaliza kulalikira mlungu umenewu, anabwerera kwawo ku Bergen. Koma ankaganizabe kwambiri za abale ndi alongo a kutauni ya Lakselv, imene ili pa mtunda wa makilomita 2,100 kuchokera kwawo. Elsebeth anati: “Ndinkapemphera kwambiri kwa Yehova ndipo ndinkatumizirana zithunzi ndi anzathu amene tinakumana nawo pa ulendowo komanso kulemberana nawo zochitika za mu utumiki.” Roald anati: “Ndinkafunika kuganiza bwinobwino za kusamukako. Ndinkayenera kuona ngati tingakwanitsedi kusamuka. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi kumeneko, tidzatha kupeza zosowa pa moyo?’ Ndinkapemphera kwambiri kwa Yehova ndiponso kulankhula ndi banja langa komanso abale amene akhala m’choonadi kwa nthawi yaitali.” Fabian anati: “Ndikaganizira kwambiri nkhaniyi, ndinkaona kuti ndilibe chifukwa chomveka chokanira. Ndinkapemphera kwa Yehova mobwerezabwereza ndipo ndinayamba kufuna kusamuka.” Nanga bwanji Isabel? Kuti akonzere zosamuka, anayamba kuchita upainiya kwawo komweko. Atachita upainiya kwa miyezi 6 komanso kuphunzira Baibulo mwakhama, anaona kuti akhoza kukwanitsa kusamuka.

ZIMENE ANACHITA KUTI AKWANITSE CHOLINGA CHAWO

Maganizo ofuna kusamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri atayamba kukula, Roald ndi banja lake anayamba kuchita zinthu zowathandiza kukwanitsa cholinga chimenechi. Roald ankagwira ntchito ya malipiro ambiri imene ankaikonda kwambiri koma anapempha bwana wake kuti atenge tchuti kwa chaka chimodzi. Komabe bwanayo anamupempha kuti azigwira ntchito milungu iwiri n’kukhala pa tchuti milungu 6. Roald anati: “Malipiro anga anatsika kwambiri komabe zinthu zinkayenda.”

Elsebeth anati: “Mwamuna wanga anandipempha kuti ndikapeze nyumba ku Lakselv ndipo nyumba yathu ya ku Bergen tizipangitsa lendi. Kuchita zimenezi sikunali kophweka komabe zinatheka. Patapita nthawi, ana athu anapeza ntchito zaganyu ndipo ankatipatsa ndalama zoyendera ndiponso zogula chakudya.”

Isabel anati: “Popeza tauni imene tinasamukira ndi yaing’ono, ndinkavutika kwambiri kupeza ntchito yoti ndizigwira  kwinaku ndikuchita upainiya. Nthawi zina, ndinkaona kuti n’zosatheka.” Komabe zinatheka chifukwa Isabel ankagwira ganyu iliyonse imene yapezeka moti anagwira maganyu osiyanasiyana okwana 9 pa chaka choyamba. Nanga kodi zinthu zinamuyendera bwanji Fabian? Iye anati: “Kuti ndimalize maphunziro anga a zamagetsi, ndinayenera kugwira ntchitoyi limodzi ndi munthu woidziwa bwino. Ndinachita zimenezi ku Lakselv. Kenako ndinakalemba mayeso n’kukhoza ndipo ndinayamba kugwira ntchitoyi. Koma ndinkaigwira maola ochepa mlungu uliwonse.”

ZIMENE ENA ANACHITA KUTI AWONJEZERE UTUMIKI WAWO

Marelius ndi Kesia akulalikira mzimayi wachisami ku Norway

M’bale wina dzina lake Marelius limodzi ndi mkazi wake Kesia ankafunanso kukatumikira kumene kulibe ofalitsa ambiri. Marelius, yemwe ali ndi zaka 29, anati: “Nditamvetsera nkhani zokhudza upainiya ndiponso apainiya amene anafunsidwa pa misonkhano yachigawo, ndinayamba kuganiza zowonjezera utumiki wanga.” Koma Kesia, yemwe ali ndi zaka 26, sankafuna kusiya achibale ake n’kusamukira kwina. Iye anati: “Sindinkafuna kusiyana ndi anthu amene ndimawakonda.” Komanso Marelius ankagwira ntchito kuti amalizitse ngongole ya nyumba yawo. Iye anati: “Tinkapemphera kwambiri kwa Yehova kuti atithandize kusintha zinthu pa moyo wathu. Iye anatithandizadi ndipo tinakwanitsa kusamuka.” Koma choyamba, iwo anawonjezera nthawi yawo yophunzira Baibulo. Kenako anagulitsa nyumba yawo n’kusiya ntchito zawo zolembedwa ndipo mu August 2011 anasamukira kumzinda wa Alta kumpoto kwa Norway. Kuti azitha kupeza zosowa zawo, Marelius anayamba ntchito yowerengera ndalama ndipo Kesia amagwira ntchito m’sitolo.

M’bale wina dzina lake Knut ndi mkazi wake Lisbeth, omwe ali ndi zaka zoposa 30, analimbikitsidwa atawerenga nkhani za mu Buku Lapachaka za anthu amene ankatumikira kumene kulibe ofalitsa okwanira. Lisbeth anati: “Nkhanizi zinatichititsa kuganiza zokatumikira kudziko lina. Koma ndinkaona kuti munthu wamba ngati ine sindingakwanitse kuchita zimenezi.” Komabe iwo anayesetsa kuti akwanitse cholinga chawochi. Knut anati: “Tinagulitsa nyumba yathu n’kukakhala ndi mayi anga kuti tisunge ndalama. Kenako kwa chaka chimodzi tinasamukira ku mpingo wa Chingelezi ku Bergen komwe tinakakhala ndi mayi a Lisbeth. Tinachita zimenezi kuti tione ngati tingakwanitse kukatumikira kudziko lina.” Pasanapite nthawi, Knut ndi Lisbeth anaona kuti ndi okonzeka kusamukira kwina. Choncho anasamukira kudziko la Uganda, komwe ndi kutali kwambiri ndi kwawo. Miyezi iwiri iliyonse pa chaka, iwo amabwerera kwawo ku Norway kuti akagwire ntchito. Ndalama zimene amapeza zimawathandiza kugula zofunika pa moyo pamene akutumikira ku Uganda kwa miyezi 10 yotsalayo.

“TALAWANI NDIPO MUONE KUTI YEHOVA NDI WABWINO”

“Tsopano m’banja lathu timakondana kwambiri.”—Roald

Kodi anthu amenewa zinthu zinawayendera bwanji? Roald anati: “Ndikuona kuti kudera lakutali kuno, m’banja lathu tikuchitira zinthu zambiri limodzi kuposa mmene tikanachitira kwathu ku Bergen. Tsopano m’banja lathu timakondana kwambiri. Tasangalalanso kuona kuti ana athu akukonda kwambiri Yehova.” Iye ananenanso kuti: “Panopa timaona kuti zinthu  zakuthupi si zofunika kwambiri ngati mmene tinkazionera poyamba.”

Elsebeth anaonanso kuti angachite bwino kuphunzira chinenero china. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? M’gawo la mpingo wa Lakselv muli mudzi wa Karasjok, womwe ndi wa anthu a fuko la Asami. Anthu a m’fuko limeneli amapezeka kumpoto kwa Norway, Sweden, Finland ndi Russia. Kuti athe kulalikira anthuwa bwinobwino, Elsebeth anaphunzira chinenero cha Chisami. Panopa amatha kulankhula zinthu zina ndi zina ndi anthu a chinenerochi. Kodi akusangalala kulalikira m’gawo latsopanoli? Iye anayankha mosangalala kuti: “Ndikuchititsa maphunziro a Baibulo okwana 6. Choncho sindikufunanso kupita kwina.”

Fabian, yemwe panopa akuchita upainiya ndiponso ndi mtumiki wothandiza, anafotokoza kuti iye ndi Isabel anathandiza achinyamata atatu mu mpingo watsopanowu. Achinyamatawo sanali kuchita zambiri mu mpingo. Panopa onse amalimbikira mu utumiki. Awiri anabatizidwa ndipo analembetsa upainiya wothandiza mu March 2012. Mmodzi wa iwo ndi mtsikana yemwe anatsala pang’ono kusiya choonadi ndipo amathokoza kwambiri Fabian ndi Isabel kuti anamuthandiza kuyambiranso kuchikonda. Fabian anati: “Zimene ananenazi zinandilimbikitsa kwambiri. Zimakhala zosangalatsa kwambiri kuthandiza munthu wina.” Isabel anati: “Kutumikira kuno kwandithandiza ‘kulawa ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’” (Sal. 34:8) Iye ananenanso kuti: “Komanso kutumikira kuno n’konjoyetsa kwabasi.”

Marelius ndi Kesia tsopano akukhala moyo wosalira zambiri koma moyo wawo ndi wabwino kwambiri. Panopa mpingo wa ku Alta, kumene iwo anasamukira, uli ndi ofalitsa okwana 41. Marelius anati: “Tikaganiza za mmene tasinthira zinthu pa moyo wathu, timalimbikitsidwa kwambiri. Timathokoza Yehova kuti tili ndi mwayi womutumikira monga apainiya. Palibe chosangalatsa ngati chimenechi.” Kesia anati: “Ndaphunzira kudalira kwambiri Yehova ndipo iye akutisamalira bwino. Ndaonanso kuti kukhala kutali ndi achibale anga kwandithandiza kuti tikakumana, ndizisangalala kwambiri kuposa m’mbuyomu. Sindinanong’oneze bondo ngakhale pang’ono ndi zimene tinasankhazi.”

Knut ndi Lisbeth akuphunzira ndi banja lina ku Uganda

Nanga bwanji Knut ndi Lisbeth ku Uganda? Knut anati: “Zinatitengera nthawi kuti tizolowere zinthu komanso chikhalidwe cha kuno. Nthawi zina timakhala ndi vuto la madzi ndi magetsi. Komanso nthawi zina timakhala ndi vuto la m’mimba. Koma chosangalatsa n’chakuti tili ndi maphunziro ambirimbiri a Baibulo.” Lisbeth anati: “Pafupi ndi kumene timakhala kuli madera amene anthu sanamvepo uthenga wabwino. Ngakhale zili choncho, tikapita kumeneko, timapeza anthu akuwerenga Baibulo ndipo amatipempha kuti tiziwaphunzitsa. Kuphunzitsa Baibulo anthu odzichepetsa ngati amenewa n’kosangalatsa zedi.”

N’zosakayikitsa kuti Mtsogoleri wathu Khristu Yesu, yemwe ali kumwamba, amasangalala kwambiri kuona kuti ntchito yolalikira imene iye anayambitsa ikuchitika m’madera ambiri masiku ano. Anthu onse a Mulungu amasangalala kwambiri kudzipereka ndi mtima wonse kuti amvere lamulo la Yesu lakuti ‘tikaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake.’—Mat. 28:19, 20.