Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Madagascar

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Madagascar

MLONGO wina wazaka za m’ma 20 dzina lake Sylviana amene akuchita upainiya ananena kuti: “Ndikamva anzanga akufotokoza zinthu zosangalatsa zimene zinachitika kudera limene anasamukira, ndinkalakalaka nanenso nditasamukira kumene kukufunika apainiya ambiri.” Mlongoyu ananenanso kuti: “Koma ndinkaona kuti sindingakwanitse kukatumikira kudera lina.”

Kodi nanunso mumamva choncho? Kodi mumafuna kukatumikira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri koma n’kumakayikira ngati mungakwanitse? Ngati ndi choncho, musataye mtima. Yehova wathandiza abale ndi alongo ambirimbiri kuti athane ndi mavuto amene ankawalepheretsa kuchita zimenezi. Kuti tidziwe mmene anawathandizira, tiyeni tikambirane zimene zachitika kuchilumba cha Madagascar, chomwe ndi cha nambala 4 pa zilumba zazikulu kwambiri padziko lonse.

Pa zaka 10 zapitazi, abale ndi alongo oposa 70, omwe ndi ofalitsa akhama komanso apainiya ochokera m’mayiko 11, * anapita kukatumikira ku Madagascar. Anthu ambiri akumeneku amalemekeza Baibulo ndipo amavomera kuphunzira. Ofalitsa akomwekunso amasamukira m’madera ena n’cholinga choti athandize kufalitsa uthenga wa Ufumu pachilumba chachikuluchi. Tiyeni tsopano tikambirane za ena mwa anthu amenewa.

ANASIYA KUCHITA MANTHA NDIPO SANATAYE MTIMA

Perrine ndi Louis

Louis ndi mkazi wake Perrine, omwe ali ndi zaka za m’ma 30, anasamuka ku France kupita ku Madagascar. Kwa zaka zambiri banjali linkafuna kuwonjezera utumiki wawo koma Perrine ankakayikira zosamuka. Iye anati: “Ndinkaopa kupita kudera lachilendo. Ndinkaona kuti sindingakwanitse kusiyana ndi achibale anga, mpingo wathu, nyumba yathu, dera lathu komanso moyo umene tinazolowera. Kunena zoona, zimene zinkatilepheretsa kusamuka ndi nkhawa zimene ndinali nazo.” Mu 2012, Perrine analimba mtima ndipo iye ndi mwamuna wake anasamuka. Kodi panopa amamva bwanji ndi zimene anasankha kuchitazi? Iye anati: “Ndikaganizira zimene zachitika pa zaka zimenezi, ndimaona kuti chikhulupiriro changa chalimba kwambiri. Ndaona Yehova akutithandiza pa moyo wathu.” Louis nayenso anati: “Anthu 10 amene tinkaphunzira nawo Baibulo anafika pa Chikumbutso choyamba chimene tinachita nawo titasamukira ku Madagascar.”

Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti azitumikirabe ku Madagascar atakumana ndi mavuto? Iwo ankachonderera Yehova kuti awapatse mphamvu kuti apirire. (Afil. 4:13) Louis anati: “Yehova anayankha mapemphero athu ndipo anatipatsa mtendere. Izi zinatithandiza kuika maganizo athu onse pa zinthu zosangalatsa zimene zinkachitika pa utumiki wathu. Anzathu a ku France ankatitumizira makalata ndi maimelo otilimbikitsa kuti tisasiye utumiki wathu.”​—Afil. 4:6, 7; 2 Akor. 4:7.

Yehova anadalitsa kwambiri Louis ndi Perrine chifukwa cha kupirira kwawo. Louis anati: “Mu October 2014, tinalowa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja * ku France. Timayamikira kwambiri Yehova kuti anatipatsa mwayi wolowa sukuluyi ndipo sitidzaiwala.” Atamaliza maphunzirowa anasangalala kwambiri atauzidwa kuti akapitirize utumiki wawo ku Madagascar.

“MUDZACHITA BWINO NDIPO TIDZASANGALALA KWAMBIRI”

Nadine ndi Didier

Didier ndi mkazi wake Nadine ndi achikulire ndipo anasamuka ku France mu 2010 kupita ku Madagascar. Didier anati: “Titangokwatirana tinkachita upainiya koma kenako tinasiya kuti tilere ana athu atatu. Koma anawa atakula tinaganiza zosamukira kudziko lina.” Nadine anati: “Ndinkakayikira zosamukazi chifukwa sindinkafuna kusiyana ndi ana anga. Koma anawo anatiuza kuti: ‘Mukasamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri mudzachita bwino ndipo tidzasangalala kwambiri.’ Mawu amenewa anatilimbikitsa kwambiri moti tinasamukadi. Panopa tikukhala kutali ndi ana athu koma tikusangalala chifukwa choti timatha kulankhula nawo pafupipafupi.”

Sizinali zophweka kuti Didier ndi Nadine aphunzire Chimalagase. Nadine ananena uku akuseka kuti: “Zinali zovuta kwambiri chifukwa si ife achinyamata.” Koma kodi anakwanitsa bwanji kuchiphunzira? Choyamba anapita kumpingo wachilankhulo chawo chomwe ndi Chifulenchi. Kenako ataona kuti zili bwinoko, anasamukira mumpingo wachimalagase. Nadine anati: “Anthu ambiri amene timawapeza mu utumiki amafunitsitsa kuphunzira Baibulo. Nthawi zambiri amatithokoza chifukwa chopita kukawaphunzitsa. Poyamba sindinamvetse zimenezi moti ndinkangoona ngati ndikulota. Ndimasangalala kwambiri kuchita upainiya m’dera limeneli. Tsiku lililonse kukacha ndimadziuza kuti, ‘Eyaa! Kwacha tsopano ndikalalikire.’”

Didier amaseka akaganizira zimene zinkachitika atangoyamba kuphunzira Chimalagase. Iye anati: “Tsiku lina ndikuchititsa mbali ina pamisonkhano yampingo sindinkamva mayankho amene abale ndi alongo ankapereka. Ndiye aliyense akayankha ndinkangoti, ‘Zikomo kwambiri.’ Koma nditathokoza mlongo wina, anthu amene anali kumbuyo kwake anayamba kundipatsa zizindikiro zoti yankho lake silinali lolondola. Nthawi yomweyo ndinatchula m’bale wina kuti ayankhe ndipo ndikukhulupirira kuti anapereka yankho lolondola.”

ANAVOMERA N’KUPITA KUKAKHALA NAWO

Pamsonkhano wachigawo wa mu 2005, Thierry ndi mkazi wake Nadia anaonera sewero lakuti “Yesetsani Kukwaniritsa Zolinga Zimene Zimalemekeza Mulungu.” Seweroli linkanena za Timoteyo ndipo linawakhudza kwambiri moti ankafunitsitsa kukatumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri. Thierry anati: “Seweroli litatha, tinayamba kuwombera m’manja ndipo ndinanong’oneza mkazi wanga kuti, ‘Ife ndiye tipita kuti?’ Mkazi wanga anandiuza kuti nayenso ankaganiza zomwezo.” Pasanapite nthawi yaitali, anayamba kusintha zina ndi zina kuti akwanitse kusamuka. Nadia anati: “Tinayamba kuchepetsa katundu amene tinali naye mpaka kungotsala ndi wokwana zikwama 4 basi.”

Kumanzere: Nadia ndi Marie-Madeleine; Kumanja: Thierry

Iwo anasamukira ku Madagascar mu 2006 ndipo atangofika anayamba kusangalala kutumikira kumeneku. Nadia anati: “Anthu amene timawalalikira amatisangalatsa kwambiri.”

Koma patapita zaka 6, banjali linakumana ndi vuto linalake. Mayi a Nadia dzina lawo a Marie-Madeleine anavulala. Iwo anagwa n’kuthyoka mkono komanso kuvulala m’mutu. Thierry ndi Nadia atakambirana ndi dokotala, anapempha mayiwo kuti azidzakhala nawo ku Madagascar. Pa nthawiyo n’kuti ali ndi zaka 80 koma anavomera n’kupita kukakhala nawo. Kodi mayiwo akusangalala kukhala ku Madagascar? Iwo anati: “Zimandivuta nthawi zina kuzolowera moyo wakuno. Koma ngakhale kuti ndili ndi mavuto ena, ndimaona kuti ndikuthandizabe mumpingo. Chomwe chimandisangalatsa kwambiri n’chakuti kukhala kunoko kukuthandiza kuti ana anga apitirize utumiki wawo.”

NDINAONA KUTI YEHOVA WANDITHANDIZA

Riana akukamba nkhani m’chilankhulo cha anthu a mtundu wa Antandroy

Chitsanzo china ndi M’bale Riana yemwe ali ndi zaka za m’ma 20. Iye anabadwira kudera lachonde kwambiri ku Alaotra Mangoro chakum’mawa kwa Madagascar. M’baleyu ankakhoza bwino kusukulu ndipo ankafuna maphunziro apamwamba, koma ataphunzira Baibulo anasintha maganizo. Iye anati: “Ndinkachita khama kuti ndimalize msanga maphunziro a ku sekondale ndipo ndinalonjeza Yehova kuti, ‘Ndikangokhoza mayeso ndiyamba upainiya.’” Riana atamaliza sukulu anakwaniritsa lonjezo lake. Iye anachoka kwawo n’kumakakhala ndi m’bale wina amene ankachitanso upainiya. Kenako anapeza ntchito ya masiku ochepa pa mlungu ndipo anayamba upainiya. Riana anati: “Ndinasankha bwino kwambiri.”

Achibale a Riana sanamvetse chifukwa chake anasintha maganizo ofuna maphunziro apamwamba. Iye anati: “Bambo anga, bambo anga aang’ono komanso agogo anga ankandilimbikitsa kuti ndiphunzire kwambiri. Koma sindinafune kusiya upainiya pa chifukwa chilichonse.” Pasanapite nthawi yaitali, anayamba kufunitsitsa kukalalikira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri. Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti akhale ndi cholinga chimenechi? Iye anati: “Akuba analowa m’nyumba yathu n’kundibera zinthu zambiri. Apa tsopano ndinakumbukira mawu a Yesu akuti ‘tiziunjika chuma kumwamba’ ndipo ndinayamba kufuna kuti ndikhale wolemera mwauzimu.” (Mat. 6:19, 20) Ndiyeno anasamukira kudera lina chakum’mwera kwenikweni kwa dzikoli pa mtunda wamakilomita 1,300 kuchokera kwawo. Kudera limeneli mvula siigwa bwino ndipo kumakhala anthu otchedwa Antandroy. Kodi n’chifukwa chiyani anasankha zosamukira kumeneku?

Akuba aja asanabwere, Riana anayamba kuphunzira Baibulo ndi azibambo awiri a mtundu wa Antandroy. Iye anaphunzira mawu ena a m’chilankhulo chawo ndipo anaganizira za kuchuluka kwa anthu a mtunduwu omwe sanamvepo uthenga wa Ufumu. Iye anati: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kusamukira kudera la anthu amenewa.”

Ndiyeno Riana anasamuka koma atafika sanathe kupeza ntchito. Munthu wina anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mwabwera kuno? Anthu amachoka kuno kuti akapeze ntchito kumene mwachokako.” Atangokhalako milungu iwiri, Riana analibiretu kalikonse ndipo anapita kumsonkhano wachigawo asakudziwa kuti agwira mtengo wanji. Tsiku lomaliza la msonkhanowu, m’bale wina anangoika kanthu kenakake m’thumba la jekete yake. Riana anapeza kuti zinali ndalama zokwanira thiransipoti yobwerera kudera lija komanso zinamuthandiza kuyamba kabizinezi kogulitsa yogati. Riana anati: “Ndinaona kuti Yehova wandithandiza ndipo ndinapitiriza kuthandiza anthu amene anali asanamvepo za Yehova.” Riana ankatanganidwanso ndi ntchito zamumpingo. Iye anati: “Ndinkakamba nkhani za onse kawiri pa mwezi. Ndinkaona kuti Yehova akundiphunzitsa pogwiritsa ntchito gulu lake.” Panopa, Riana akulalikirabe kuderali ndipo akuthandiza anthu ambiri amene akufuna kuphunzira za Yehova.

“ADZADALITSIDWA NDI MULUNGU WOKHULUPIRIKA”

Yehova amatitsimikizira kuti “aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupirika.” (Yes. 65:16) Tikamayesetsa kusintha zinthu pa moyo wathu n’cholinga choti tizichita zambiri potumikira Yehova, iye amatidalitsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Sylviana, yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi. Kumbukirani kuti iye ankaona kuti sangakwanitse kusamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri. N’chifukwa chiyani ankaona kuti sangakwanitse? Iye anati: “Mwendo wanga wakumanzere ndi waufupi poyerekezera ndi wakumanja. Choncho ndimayenda motsimphina ndipo ndimatopa msanga.”

Sylviana (kumanzere) ndi Sylvie Ann (kumanja) ali ndi Doratine pa tsiku limene anabatizidwa

Koma mu 2014, mlongoyu anasamuka limodzi ndi mlongo wina wachitsikana wamumpingo wake dzina lake Sylvie Ann. Iwo anapita kumudzi wina womwe uli pa mtunda wa makilomita 85 kuchokera kwawo. Ngakhale kuti pali zinthu zimene zikanamulepheretsa, Sylviana wakwanitsa kuchita zimene ankafuna ndipo Yehova wamudalitsa kwambiri. Iye anati: “Nditangotumikira kuderali chaka chimodzi, mayi wina dzina lake Doratine amene ndinkaphunzira naye anabatizidwa pamsonkhano wadera.”

“NDIKUTHANDIZA”

Zimene anthuwa anena zikusonyeza kuti tikamayesetsa kulimbana ndi zimene zikutilepheretsa kuchita zambiri mu utumiki, timaona Yehova akukwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yes. 41:10) Izi zimatithandiza kuti tizikonda kwambiri Yehova. Komanso tikamadzipereka pomutumikira m’dziko lathu kapena m’dziko lina, timakonzekera ntchito zimene tidzagwire m’dziko latsopano limene tikuyembekezera. Didier, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Tikamatumikira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri timakhala tikukonzekera ntchito imene tidzagwire m’tsogolo.”

^ ndime 4 Abale ndi alongowa anachokera ku Canada, Czech Republic, France, Germany, Guadeloupe, Luxembourg, New Caledonia, Sweden, Switzerland, United Kingdom ndi ku United States.

^ ndime 8 Panopa inalowedwa m’malo ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Atumiki a nthawi zonse oyenerera amene akutumikira m’dziko lina akhoza kufunsira kuti alowe sukuluyi m’dziko lawo kapena m’dziko lina kumene imachitika m’chilankhulo chawo.