Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Eric ndi Amy

Anadzipereka ndi Mtima Wonse—Ku Ghana

Anadzipereka ndi Mtima Wonse—Ku Ghana

KODI mukudziwa m’bale kapena mlongo aliyense amene anasamukira kudziko kumene kukufunika ofalitsa ambiri? Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘N’chiyani chinawachititsa kuti asamukire kudziko lina? Nanga anakonzekera bwanji kusamukako? Kodi inenso ndingathe kusamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri?’ Kuti mupeze mayankho, mungafunse anthu amene anasamukawo. Choncho tiyeni tione zina zimene anthuwa ananena.

KODI N’CHIYANI CHINAWACHITITSA KUTI ASAMUKE?

N’chiyani chinakupangitsani kuti muganize zokatumikira kudziko lina? Amy, amene tsopano ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo ndi wa ku United States anati: “Kwa zaka zambiri ndinali ndi cholinga chokatumikira kudziko lina, koma pena ndinkaona ngati n’zosatheka.” N’chiyani chinamuthandiza kuti akwaniritse cholinga chakechi? Iye anati: “Mu 2004 banja lina lomwe linkatumikira ku Belize linandiitana kuti ndikachite nawo upainiya kwa mwezi umodzi ndipo ndinapitadi. Ndinasangalala kwambiri moti patangotha chaka chimodzi ndinasamukira ku Ghana n’kumakachita upainiya.”

Aaron ndi Stephanie

Stephanie wa ku United States, anaganiza zoonanso mmene zinthu zilili pa moyo wake ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka za m’ma 20. Iye anaona kuti anali ndi thanzi labwino ndipo analibe udindo wa m’banja. Choncho anazindikira kuti angathe kuchita zambiri potumikira Yehova. Izi zinamuthandiza kuti asamukire ku Ghana. A Filip ndi akazi awo a Ida, kwawo ndi ku Denmark ndipo ali ndi zaka za m’ma 50. Iwo ndi apainiya ndipo ankafunitsitsa kusamukira kudera lomwe kukufunika ofalitsa ambiri. A Filip anati: “Mwayi wopita ku Ghana utapezeka, tinangomva ngati Yehova akutiuza kuti, ‘Pitani, musalephere.’” Mu 2008 anasamukira ku Ghana ndipo anatumikira kumeneko kwa zaka zoposa zitatu.

Brook ndi Hans

Hans ndi mkazi wake Brook ali ndi zaka za m’ma 30. Iwonso ndi apainiya ndipo kwawo ndi ku United States. M’chaka cha 2005 anagwira nawo ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi mphepo yamkuntho. Kenako anapempha kuti akatumikire m’gulu la antchito ya zomangamanga padziko lonse koma sanaitanidwe. Hans anati: “Tili pamsonkhano tinamvetsera nkhani ina imene inanena kuti Mfumu Davide atauzidwa kuti samanga kachisi anasintha zolinga zake. Mfundo imeneyi inatithandiza kwambiri kuzindikira kuti nafenso tingathe kusintha zolinga zathu.” (1 Mbiri 17:1-4, 11, 12; 22:5-11) Brook anawonjezera kuti: “Tinaona kuti Yehova akufuna kuti tigogode khomo lina.”

Hans ndi Brook atamva nkhani zosangalatsa kuchokera kwa anzawo amene akutumikira m’mayiko ena, anaganiza zokachita upainiya kudziko lina. Mu 2012 anasamukira ku Ghana ndipo anathandiza mpingo wachinenero chamanja kwa miyezi 4. Ngakhale kuti kenako anabwerera ku United States, anaona kuti nthawi imene anakhala ku Ghana inawathandiza kuti apitirize kuika Ufumu pamalo oyamba. Kuyambira nthawi imeneyo akhala akuthandiza pa ntchito zomanga maofesi a nthambi ku Micronesia.

ZIMENE AMACHITA POKONZEKERA

Kodi munakonzekera bwanji kusamuka? Stephanie anati: “Ndinawerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhudza kukatumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri. * Ndinakambirananso nkhaniyi ndi akulu ndiponso woyang’anira dera ndi mkazi wake. Koma chofunika kwambiri n’chakuti ndinkauza Yehova nkhaniyi.” Stephanie anayamba kukhala moyo wosalira zambiri ndipo izi zinamuthandiza kuti azisunga ndalama zoti akagwiritse ntchito akadzasamuka.

Hans anati: “Tinkapempha Yehova kuti atitsogolere chifukwa tinkafuna kusamukira kumene iye angafune kuti tipite. Popemphera tinkatchulanso deti limene tinakonza kuti tisamuke.” Banjali linatumiza makalata kumaofesi a nthambi 4. Nthambi yomwe inawayankha ndi ya ku Ghana. Iwo anapita kudzikoli ndipo ankafuna kuti akatumikire kwa miyezi iwiri yokha. Koma Hans anati: “Tinasangalala kwambiri kutumikira mumpingo wa kumeneku moti miyezi iwiri itatha tinakomedwa n’kuwonjezera nthawi.”

Adria ndi George

George ndi mkazi wake Adria ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo kwawo ndi ku Canada. Iwo ankadziwa kuti Yehova amadalitsa anthu amene ali ndi zolinga zabwino ndiponso amene amasankha zinthu mwanzeru. Choncho anayamba kuchita zinthu zowathandiza kuti akwaniritse zolinga zawo. Anacheza ndi mlongo amene anapita kukatumikira ku Ghana ndipo anamufunsa mafunso ambiri. Analemba makalata awiri, n’kutumiza kunthambi ya ku Canada ndi ya ku Ghana. Adria anati: “Tinayamba kusintha zinthu zambiri n’cholinga choti tizikhala moyo wosalira zambiri.” Izi zinawathandiza kuti athe kusamukira ku Ghana mu 2004.

ZIMENE AMACHITA AKAKUMANA NDI MAVUTO

Kodi ndi mavuto ati amene mumakumana nawo, nanga mumatani? Vuto loyamba limene Amy anakumana nalo linali loti ankawasowa kwambiri achibale ake. Iye anati: “Chilichonse m’dzikoli chinali chachilendo.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Ndinkalimbikitsidwa kwambiri achibale anga akaimba foni n’kuyamikira zimene ndikuchita. Ndinkaona kuti ndinachita bwino kusamuka. Kenako tinayamba kulankhulana kudzera pa zinthu monga sikayipi. Popeza tikamalankhulana tinkaonana, ndinasiya kuwasowa kwambiri achibale angawo.” Komanso Amy anayamba kucheza ndi mlongo wina wolimba mwauzimu ndipo anamuthandiza kudziwa zambiri zokhudza chikhalidwe cha kumeneko. Amy anati: “Tinkagwirizana kwambiri moti ndikakhala kuti sindikumvetsa zinazake zokhudza anthu a m’dzikoli, ndinkamufunsa iyeyo. Iye anandithandiza kudziwa zoyenera kuchita ndipo izi zinandithandiza kuti ndizisangalala.”

George ndi Adria ananena kuti atangofika kumene ku Ghana, ankangoona ngati dziko labwerera makedzana. Adria anati: “Kwathu timachapa pa mashini koma kuno tinkachapa pa manja. Kuti uphike chakudya zinkatenga nthawi yaitali kuyerekeza ndi kwathu, komwe timaphika pa magetsi. Koma patapita nthawi tinazolowera ndipo sitinkadandaulanso.” Brook anati: “Ngakhale kuti apainiyafe timakumana ndi mavuto ambiri, timakhala osangalala. Tikamaganizira zinthu zabwino zimene takumana nazo, mitima yathu imadzaza ndi chimwemwe.”

AMAPEZA MADALITSO AMBIRI

N’chifukwa chiyani mumalimbikitsa anthu ena kuti nawonso achite utumiki umenewu? Stephanie anati: “Zimakhala zosangalatsa kwambiri kulalikira kudera limene anthu ambiri amafunitsitsa kudziwa choonadi, moti amafuna kuti uziphunzira nawo tsiku lililonse. Ndimaona kuti ndinachita bwino kwambiri kusamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri.” Mu 2014 Stephanie anakwatirana ndi Aaron ndipo akutumikira pa Beteli ya ku Ghana.

Mlongo winanso amene anasamukira ku Ghana ndi Christine, wa ku Germany ndipo ali ndi zaka za m’ma 30. Asanasamukire ku Ghana ankatumikira ku Bolivia. Iye anati: “Utumiki umenewu wandithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Popeza ndili kutali ndi achibale anga, ndimapemphera kwa Yehova pafupipafupi kuti azindithandiza. Izi zapangitsa kuti akhale mnzanga wapamtima. Ndaonanso kuti n’zoona kuti anthu a Yehova ndi ogwirizana. Utumiki umenewu wandiphunzitsa zambiri.” Posachedwapa Christine anakwatiwa ndi Gideon ndipo onse akutumikirabe ku Ghana.

Christine ndi Gideon

A Filip ndi akazi awo anafotokoza zimene ankachita pofuna kuthandiza anthu amene ankaphunzira nawo Baibulo kuti ayambe kutumikira Yehova. Anati: “Poyamba tinkakhala ndi maphunziro 15 kapena kuposa. Koma kenako tinkaonetsetsa kuti asapitirire 10 kuti tizikhala ndi nthawi yokwanira yowaphunzitsa.” Kodi zimenezi zinkathandiza bwanji? A Filip anati: “Ndinkaphunzira ndi mnyamata wina dzina lake Michael. Ndinkaphunzira naye tsiku lililonse ndipo ankakonzekera bwino moti tinamaliza buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani patangotha mwezi umodzi. Zitatero Michael anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Pa tsiku lake loyamba kulowa mu utumiki, anandiuza kuti: ‘Kodi mungakandithandize kuchititsa maphunziro anga?’ Ndinadabwa kwambiri. Iye anandifotokozera kuti ali ndi maphunziro atatu ndipo ankafuna ndimuthandize kuti azichititsa bwino maphunziro akewo.” Izitu zikusonyeza kuti palidi anthu ambiri ofunika kuwalalikira, moti ophunzira Baibulo, akumakhalanso ophunzitsa Baibulo.

A Ida ndi a Filip

Amy anafotokoza kuti sanachedwe kuzindikira kuti kumene anasamukira kunkafunikadi ofalitsa ambiri. Iye anati: “Titangofika ku Ghana, tinapita kukalalikira pakamudzi kena n’cholinga choti tikafufuze anthu amene ali ndi vuto losamva. Koma tinapeza anthu 8 pamudzi umodzi wokhawo.” Panopa Amy anakwatirana ndi Eric ndipo onse ndi apainiya apadera. Iwo ali mumpingo wa chinenero chamanja. Mpingo wawo umathandiza ena mwa anthu osamva oposa 300 a m’dziko la Ghana ndipo pa anthu amenewa ena ndi ofalitsa. George ndi Adria amaona kuti kutumikira m’dziko la Ghana kunali ngati kuphunzira umishonale. Kenako iwo anaitanidwa kuti akalowe kalasi ya nambala 126 ya Sukulu ya Giliyadi ndipo anasangalala kwambiri. Panopa akutumikira monga amishonale ku Mozambique.

AMACHITA ZONSEZI CHIFUKWA CHOKONDA YEHOVA

N’zosangalatsa kwambiri kuona anthu ambiri ochokera m’mayiko ena akugwira ntchito yokolola limodzi ndi abale ndi alongo a ku Ghana. (Yoh. 4:35) Tingati anthu okwana 120 amabatizidwa mlungu uliwonse ku Ghana. Pali anthu 17 amene anasamukira m’dzikoli. Koma padziko lonse palinso abale ndi alongo ambirimbiri amene ‘anadzipereka’ ndi mtima wonse kuti akathandize kumene kukufunika ofalitsa ambiri. Amachita zonsezi chifukwa chokonda Yehova. Anthu amenewa amasangalatsa kwambiri mtima wa Yehova.​—Sal. 110:3; Miy. 27:11.

^ ndime 9 Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?” ndi yakuti, “Kodi Mungawolokere ku Makedoniya?” mu Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi ya December 15, 2009.