Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Brazil

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Brazil

ZAKA zingapo m’mbuyomu, Rúbia (1), yemwe panopa ali ndi zaka 30, anapita kukaona Sandra (2). Sandra ndi mpainiya ndipo pa nthawiyo ankatumikira mu mpingo wina waung’ono kum’mwera kwa Brazil. Ulendo umenewu unachititsa kuti Rúbia asinthiretu moyo wake. Kodi n’chiyani chinamuchititsa chidwi mpaka kufika posintha? Tiyeni timulole Rúbia afotokoze yekha.

“SINDINAMVETSE”

Rúbia anati: “Sandra ananditenga kupita kwa mayi wina amene ankaphunzira naye Baibulo. Phunziro lili mkati, mayiyo anamuuza kuti: ‘Sandra, atsikana atatu kuntchito kwathu akufuna kuphunzira Baibulo ndiye ndangowauza kuti adikire kaye. Paja uli ndi maphunziro okwanira chaka chonsechi eti?’ Sindinamvetse ayi. Kwathu timaguba nthawi yaitali osapeza phunziro ngakhale limodzi. Koma uku anthu ofuna kudziwa Yehova anafunika kuyembekeza kaye kuti nthawi yawo ikwane. Nditangomva zimenezi, mtima sindinaupeze moti ndinkafunitsitsa kuthandiza anthu m’kataunika. Pasanapite nthawi yaitali, ndinasamuka mumzinda umene ndinkakhala n’kupita kumene Sandra ankachita upainiya.”

Kodi Rúbia zinamuyendera bwanji atapita? Iye anati: “Pa miyezi iwiri yokha ndinapeza maphunziro 15 ndipo nanenso ndinayamba kuuza anthu ofuna kuphunzira kuti adikire kaye.”

ANASINTHA MMENE ANKAONERA UTUMIKI

Pa nthawi ina, Diego (3), yemwe ali ndi zaka zoposa 20, anapita kukaona banja lina limene linkachita upainiya ku Prudentópolis, tauni yaing’ono yomwe ili kum’mwera kwa Brazil. Ulendo umenewu unachititsa kuti asinthe mmene ankaonera utumiki. Diego anati: “Sindinkatumikira ndi mtima wonse mu mpingo wathu. Ndinkangolalikira maola ochepa chabe mwezi uliwonse. Koma nditakumana ndi apainiyawa, ndinachita chidwi ndi zimene ankachita mu utumiki. Nditayerekezera ndi zimene ndinkachita, ndinaona kuti iwo akusangalala kwambiri kuposa ineyo chifukwa ankachita zambiri mu utumiki. Pompo ndinafuna kuti nanenso ndizisangalala ndi utumiki.” Izi zitachitika, Diego nayenso anayamba upainiya.

Kodi ndinu wachinyamata amene mumalalikira ndithu ndiponso kupezeka pa misonkhano? Koma kodi pansi pa mtima mumaona kuti mumangochita zinthuzi mosaikirapo mtima ndipo simusangalala? Ngati ndi choncho, n’zotheka kusintha n’kumasangalala ndi utumiki. Mungachite zimenezi pokatumikira kudera limene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri. N’zoona kuti kusiya moyo wawofuwofu kungakhale kovuta. Koma achinyamata ambiri achita zimenezi. Iwo asintha zinthu pa moyo wawo n’cholinga choti achite zambiri potumikira Yehova. Chitsanzo china ndi cha Bruno.

KODI NDIKHALE KATSWIRI WA ZOIMBAIMBA KAPENA MTUMIKI?

Bruno (4), yemwe panopa ali ndi zaka 28, anapita kusukulu yophunzitsa kuimba. Iye ankafuna kukhala mtsogoleri wa gulu loimba ndi zing’wenyeng’wenye. Ankakhoza bwino kwambiri moti pa nthawi zina ankapemphedwa kuti atsogolere gulu lalikulu kwambiri la oimba ndi zing’wenyeng’wenye. Iye ankaoneratu kuti tsogolo lake ndi lowala. Koma Bruno anati: “Mu mtima mwanga ndinkaona kuti munthune ndikusowa chinachake. Ndinkadziwa kuti ndadzipereka kwa Yehova koma sindikumupatsa zonse zimene ndikanatha. Maganizo amenewa ankandivutitsa kwabasi. Ndinapemphera kwa Yehova n’kumuuza nkhaniyi komanso ndinacheza ndi abale angapo okhwima mwauzimu. Nditaiganizira mofatsa nkhaniyi, ndinasiya sukuluyo n’kupita kudera limene kunalibe ofalitsa Ufumu ambiri.” Kodi zotsatira zake zinali zotani?

Bruno anapita kutauni ya Guapiara. M’tauniyi muli anthu pafupifupi 7,000 ndipo ili pa mtunda wa makilomita 260 kuchokera kumzinda wa São Paulo. Komatu Bruno anasintha zambiri. Iye anati: “Ndinkakhala m’nyumba yopanda firiji, TV kapena Intaneti. Komabe pafupi ndi nyumbayi panali kadimba ndiponso munda wa zipatso.” Iye ankatumikira mu mpingo wina waung’ono ndipo kamodzi pa mlungu ankatenga chakudya ndi madzi m’chikwama limodzi ndi mabuku n’kupita kukalalikira kumadera akumidzi. Ankayenda pa njinga yamoto. Anthu amene ankawapeza anali oti sanamvepo uthenga wabwino. Bruno anati: “Ndinali ndi maphunziro 18. Ndinkasangalala kwambiri kuona anthu amene ndikuphunzira nawo akusintha. Ndinkakhala wosangalala kwambiri chifukwa choika Ufumu pa malo oyamba. Apa m’pamene ndinazindikira kuti ndapeza chinthu chomwe chinkasowa pa moyo wanga. Ndikanapitiriza maphunziro a zoimbaimba aja kuti ndipeze chuma, sindikanasangalala chonchi.” Kodi Bruno ankatani kuti azipeza kangachepe kukataunika? Titamufunsa iye anamwetulira n’kunena kuti: “Ndimaphunzitsa anthu kuimba gitala.” Tingati anali asanasiye zoimbaimba.

“SINDIKANATHA KUCHOKA”

Zochitika pa moyo wa Mariana (5), yemwe panopa ali ndi zaka zoposa 25, zikufanana ndi za Bruno. Mariana anali loya koma ankaonanso kuti akusowa chinachake pa moyo wake. Iye anati: “Ndinkamva ngati ‘ndikungothamangitsa mphepo.’” (Mlal. 1:17) Abale ndi alongo ena anamulimbikitsa kuyamba upainiya. Ataiganizira mofatsa nkhaniyi, iye limodzi ndi anzake anaganiza zokathandiza ku mpingo wa ku Barra do Bugres. Mpingowu unali kudera lakumidzi pafupi ndi dziko la Bolivia ndipo unali pa mtunda wa makilomita ambirimbiri kuchokera kumene ankakhala. Anzake amene anapita nawo ndi Bianca (6), Caroline (7), ndi Juliana (8). Kodi zotsatira zake zinali zotani?

Mariana anati: “Ndinkangofuna kukatumikira kuderali kwa miyezi itatu yokha. Koma pamene miyeziyi inkatha, ndinali ndi maphunziro 15. Anthu onsewa ankafunika kuthandizidwa kuti adziwe bwino choonadi. Ndinalephera kulimba mtima n’kuwauza kuti ndikupita. Sindikanatha kuchoka.” Alongo anayi onsewa sanabwerere. Mariana anayamba kusangalala kwambiri pa moyo wake chifukwa cha kusintha kumeneku. Iye anati: “Ndimasangalala kudziwa kuti Yehova akundigwiritsa ntchito kuthandiza anthu kuti asinthe moyo wawo n’kuyamba kuchita zabwino. Ndi mwayi waukulu kugwiritsa ntchito mphamvu ndi nthawi yanga pa zinthu zofunika kwambiri.” Alongo anayi onsewo amamva ngati mmene amamvera Caroline. Iye anati: “Ndikamagona usiku ndimamva bwino chifukwa chodziwa kuti ndachita zonse zimene ndikanatha potumikira Mulungu. Panopa ndimangoganiza mmene ndingathandizire anthu amene ndimaphunzira nawo Baibulo. Ndimasangalala kuwaona akusintha chifukwa chophunzira. M’pake kuti Baibulo limati: ‘Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.’”—Sal. 34:8.

Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona achinyamata ambirimbiri padziko lonse ‘akudzipereka mofunitsitsa’ kuti alalikire uthenga wabwino wa Ufumu m’madera akumidzi. (Sal. 110:3; Miy. 27:11) Yehova amadalitsa kwambiri anthu onse amene amachita zimenezi.—Miy. 10:22.