Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | SARA

Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”

Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”

YEREKEZERANI kuti mukuona Sara ataima penapake n’kumadziwongola, ndipo akuona dzuwa likulowa. Iye amatsogolera bwino antchito ake. Antchitowo amakhala ndi zochita zambiri komanso amagwira ntchito yawo mosangalala. Koma sikuti Sara amangokhala n’kumadikira kuti antchitowo agwire ntchito zonse. Nayenso amagwira ntchito mwakhama. Ndiyeno yerekezerani kuti mukumuona akuwongolanso manja ake chifukwa choti wakhala akusoka hema amene iye ndi banja lake amakhalamo. Hemayo akuoneka wotuwa chifukwa chopsa ndi dzuwa komanso kuvumbidwa ndi mvula. Zimenezi zikukumbutsa Sara za kuchuluka kwa zaka zimene wakhala moyo wosamukasamuka. Sara akuona kuti tsikuli layenda mwachangu ndipo tsopano kunja kwayamba kuda. M’mawa wa tsikuli mwamuna wake Abulahamu * anachoka n’kumusiya ali pakhomo. Tsopano maso a Sara ali kunjira kudikira kuti mwamuna wakeyo abwera nthawi yanji. Kenako akuona mwamuna wakeyo akubwera chapatali akutsika phiri, ndipo Sara akumwetulira.

Panali patatha zaka 10 kuchokera pamene Abulahamu ndi banja lake anawoloka mtsinje wa Firate n’kulowa m’dziko la Kanani. Sara anakhala akuthandiza mwamuna wake pa ulendo wonsewu ngakhale kuti pamene ankanyamuka sankadziwa komwe ankapita. Sara ankachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti mwamuna wakeyo anali ndi mbali yaikulu kuti cholinga cha Yehova, choti atulutse mtundu waukulu, chikwaniritsidwe. Koma kodi Sara anali ndi mbali yotani pa nkhani imeneyi? Iye anali wosabereka ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 75. Mwina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi lonjezo la Yehova loti Abulahamu adzakhala ndi mwana lidzakwaniritsidwa bwanji popeza ndine wosabereka?’ Zinali zomveka ngati Sara ankadzifunsadi funso limeneli kapenanso ngati zinkamuvuta kukhala woleza mtima n’kudikira kuti aone mmene Yehova angayendetsere nkhaniyo.

Nafenso nthawi zina tingamadzifunse kuti, ‘Kodi zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa liti?’ Nthawi zambiri zimakhala zovuta kukhala woleza mtima, makamaka ngati zimene tikuyembekezerazo tikuzilakalaka kwambiri. Ndiye kodi tingaphunzire chiyani kwa mayi wachikhulupiriro cholimba ameneyu?

“YEHOVA ANANDITSEKA KUTI NDISABEREKE”

Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ndi banja lake atangobwerera kumene kuchokera ku Iguputo. (Genesis 13:1-4) Iwo ankakhala dera lina lokwera chakum’mawa kwa Beteli, dera lomwe Akanani ankalitchula kuti Luzi. Sara akaima pamalo amenewa ankatha kuona mbali yaikulu ya Dziko Lolonjezedwa. M’dzikoli munali midzi yambiri komanso misewu yomwe inkapita m’mayiko akutali. Koma zonsezi sizinali kanthu poyerekezera ndi mzinda umene Sara anachokera. Iye anakulira mumzinda wa Uri ku Mesopotamiya, womwe unali ulendo wa makilomita 1,900 kuchokera ku Kanani. Mumzinda umenewu munali misika komanso mashopu ambirimbiri komwe ankagula zinthu mosavutikira. Kumeneko Sara anasiya achibale ake komanso nyumba yabwino kwambiri, yomwe mwina inali ndi madzi a m’mipope. Koma sikuti Sara akakhala ankangoganiza za zinthu zimene anasiyazo. Tikutero chifukwa mayi ameneyu anali woopa Mulungu.

Taganizira zimene mtumwi Paulo analemba patatha zaka 2,000 kuchokera pa nthawiyo. Ponena za chikhulupiriro cha Sara ndi Abulahamu iye anati: “Akanakhala kuti anali kumangokumbukira malo amene anachokera, mpata wobwerera akanakhala nawo.” (Aheberi 11:8, 11, 15) Choncho Sara komanso Abulahamu sankangoganizira zimene anasiya n’kumalakalaka atakhala nazonso. Akanakhala kuti ankachita zimenezi, akanaganiza zobwerera kwawo. Komatu ngati akanabwerera, akanasemphana ndi madalitso amene Yehova ankafuna kuwapatsa. Komanso anthufe sitikanadziwa n’komwe zoti kunali Abulahamu ndi Sara. Koma chifukwa choti sanabwerere, iwo ndi zitsanzo zabwino kwa tonsefe pa nkhani ya chikhulupiriro.

Sara ankaganizira zakutsogolo m’malo momangoganizira zinthu zimene anasiya. Choncho ankathandiza mwamuna wake pa ulendo wonsewu. Iwo ankalongedza mahema, kuyenda ndi ziweto komanso kumanganso mahemawo akafika pamalo atsopano. Sara ankapirira mavuto onse amene ankakumana nawo. Kenako Yehova anauzanso Abulahamu lonjezo loti adzamudalitsa koma sanatchulebe kalikonse za Sara.​—Genesis 13:14-17; 15:5-7.

Patapita nthawi Sara anaona kuti ndi bwino kuti auze Abulahamu za nkhani imene anaiganizira kwa nthawi yaitali. Yerekezerani kuti mukumuona pamene akufuna kuuza mwamuna wake za nkhaniyi. Kodi mukuganiza kuti nkhope yake inkaoneka bwanji pamene ankanena kuti: “Yehova ananditseka kuti ndisabereke ana.” Kenako anauza mwamuna wakeyo kuti agone ndi kapolo wake Hagara kuti abereke mwana. N’kutheka kuti Sara ankanena zimenezi mtima ukumuwawa kwambiri. Mwina zingaoneke zachilendo masiku ano, koma pa nthawiyo sizinali zodabwitsa mwamuna kukwatira mitala kapena kugona ndi mkazi wapambali n’cholinga choti abereke mwana. * Kodi mwina Sara ankaganiza kuti zimenezi zithandiza kuti cholinga cha Yehova chotulutsa mtundu kudzera mwa Abulahamu chikwaniritsidwe? Sitikudziwa, koma chomwe tikudziwa n’choti iye anali wokonzeka kuchita chilichonse kuti cholinga cha Mulungu chikwaniritsidwe. Ndiye kodi Abulahamu anatani? Baibulo limati iye “anamvera mawu” a Sara.​—Genesis 16:1-3.

Nkhaniyi sisonyeza kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti Sara auze mwamuna wake kuti agone ndi kapolo wake. Zimene Sara anachitazi zikungosonyeza kuti ankaganiza ngati mmene anthu ambiri amaganizira. Iye ankaganiza kuti Mulungu ndi amene anachititsa kuti asakhale ndi mwana ndipo sankadziwa kuti Mulunguyo ali ndi njira yothetsera vutoli. Sara ankakhumudwa kwambiri akaganizira vuto lakeli. Komabe zimene anachitazi zinasonyeza kuti sanali wodzikonda. Masiku ano anthu ambiri saganizira za ena ndipo amangofuna kuti zawo ziyende. Ndiye kodi si zochititsa chidwi kuti Sara anali wosadzikonda? Ifenso tikamayesetsa kuika patsogolo zofuna za Mulungu osati zathu, ndiye kuti tikutsanzira chikhulupiriro cha Sara.

“UNASEKA IWE”

Pasanapite nthawi, Hagara anakhala ndi pakati. Mwina izi zinachititsa kuti ayambe kudziona kuti ndi wofunika kwambiri. Choncho anayamba kuchitira chipongwe Sara. Zimenezitu zinali zopweteka kwambiri kwa Sara. Sara anauza Abulahamu za nkhaniyi, ndipo kenako anayamba kuzunza Hagara. Koma Baibulo silinena kuti ankamuzunza bwanji. Kenako Hagara anabereka mwana wamwamuna, dzina lake Isimaeli. (Genesis 16:4-9, 16) Ndiyeno patapita zaka zambiri, Yehova analankhulanso ndi Abulahamu. Pa nthawiyi n’kuti Sara ali ndi zaka 89 ndipo Abulahamu anali ndi zaka 99. Uthenga umene analandira ulendo umenewu unali wosangalatsa kwambiri.

Apanso, Yehova analonjeza bwenzi lake Abulahamu kuti adzachulukitsa mbewu yake. Mulungu anasinthanso dzina lake. Poyamba ankadziwika kuti Abulamu, koma Yehova anamusintha n’kukhala Abulahamu. Dzinali limatanthauza kuti, “Tate wa Mitundu Yambiri.” Pa nthawiyi ndi pamene Yehova anatchula za Sara. Mulungu anasintha dzina lake lakuti Sarai, kutanthauza “Wolongolola,” n’kukhala Sara. Dzina lakuti Sara limatanthauza “Mfumukazi.” Yehova anafotokoza chifukwa chake anamupatsa dzina limeneli. Iye anati: “Ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wochokera mwa iye. Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.”​—Genesis 17:5, 15, 16.

Apa m’pamene zinadziwika kuti pangano limene Yehova anapanga ndi Abulahamu, lakuti adzachulukitsa mbewu yake, lidzakwaniritsidwa kudzera mwa mwana amene Sara adzabereke. Mulungu ananena kuti mwanayo dzina lake lidzakhala Isaki, kutanthauza “Kuseka.” Abulahamu atamva kuti Yehova adzadalitsa Sara pomupatsa mwana, “anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kuyamba kuseka.” (Genesis 17:17) Abulahamu anadabwa atamva zimenezi ndipo anasangalala kwambiri. (Aroma 4:19, 20) Nanga bwanji Sara?

Pasanapite nthawi yaitali, kunyumba kwa Abulahamu kunabwera alendo atatu. Pa nthawiyi n’kuti dzuwa likuswa mtengo. Komabe Abulahamu ndi Sara, ngakhale kuti anali achikulire, anawakonzera chakudya alendowa. Abulahamu anauza Sara kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu ya seya, uukande, ndipo upange makeke ozungulira.” Pa nthawiyo, kuti munthu achereze alendo pankakhala ntchito yambiri. Koma Abulahamu sanasiyire ntchito yonse mkazi wake. Iye anapita kukapha ng’ombe yaing’ono yamphongo n’kukonza chakudya ndi zakumwa za alendowo. (Genesis 18:1-8) Kenako anazindikira kuti alendowo anali angelo. N’kutheka kuti mtumwi Paulo ankaganizira nkhani imeneyi pamene analemba kuti: “Musaiwale kuchereza alendo, pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.” (Aheberi 13:2) Kodi nanunso mungakonde kutsanzira Abulahamu ndi Sara pa nkhani yochereza alendo?

Sara ankakonda kuchereza alendo

Kenako mmodzi wa angelowo anabwereza lonjezo limene Mulungu anauza Abulahamu lakuti Sara adzakhala ndi mwana. Pa nthawiyi n’kuti Sara ali muhema wake ndipo ankamvetsera. Popeza anali wokalamba, ankaona kuti zinali zosatheka kuti akhale ndi mwana, moti analephera kupirira mpaka anayamba kuseka. Iye anati: “Kodi mmene ndatheramu, zoona ndingakhaledi ndi chisangalalo chimenechi, komanso ndi mmene mbuyanga wakalambiramu?” Koma mngeloyo anafunsa Sara funso losonyeza kuti zimene ankaganizazo sizinali zoona. Anamufunsa kuti: “Kodi pali chosatheka ndi Yehova?” Apa Sara anachita mantha ndipo anachita zimene anthu ambiri angachite. Iye anayankha kuti: “Sindinaseketu ine ayi!” Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Ayi! Unaseka iwe.”​—Genesis 18:9-15.

Kodi mfundo yoti Sara anaseka ikusonyeza kuti analibe chikhulupiriro? Ayi ndithu. Baibulo limati: “Mwa chikhulupiriro, Sara nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati ngakhale kuti anali atapitirira zaka zobereka, chifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.” (Aheberi 11:11) Sara ankadziwa kuti Yehova angathe kukwaniritsa chilichonse chimene walonjeza. Kunena zoona, tonsefe masiku ano tikufunika chikhulupiriro ngati chimenechi. Choncho tingachite bwino kumaphunzira Baibulo mwakhama kuti timudziwe bwino Yehova. Tikatero tidzaona kuti Sara anachita bwino kukhala ndi chikhulupiriro. Yehova ndi wokhulupirika ndipo amakwaniritsa zimene walonjeza. Nthawi zina amachita zimenezi modabwitsa kwambiri kapenanso m’njira imene ingatiseketse.

“MVERA MAWU AKE”

Yehova anadalitsa Sara chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba

Sara ali ndi zaka 90 anabereka mwana ndipo anasangalala kwambiri chifukwa kwa nthawi yaitali ankalakalaka atakhala ndi mwana. Pa nthawiyi n’kuti mwamuna wake ali ndi zaka 100. Abulahamu anatchula mwanayo dzina lakuti Isaki, kapena kuti “Kuseka,” monga mmene Mulungu ananenera. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona Sara akumwetulira n’kunena kuti: “Mulungu wandipatsa chifukwa chosangalalira. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane.” (Genesis 21:6) Mphatso imene Yehova anamupatsayi iyenera kuti inachititsa kuti Sara akhale wosangalala mpaka pamene anamwalira. Komabe kukhala ndi mwana kunachititsanso kuti akhale ndi udindo waukulu.

Isaki atakwanitsa zaka 5, banjali linakonza phwando posangalala kuti mwanayo wasiya kuyamwa. Koma paphwandoli Sara anaona kuti chinachake sichili bwino. Baibulo limati iye anaona Isimaeli mwana wa Hagara, yemwe pa nthawiyi anali ndi zaka 19, akuseka Isaki. Uku sikunali kungomuseka posewera naye. Patapita nthawi mtumwi Paulo analemba kuti Isimaeli ankazunza Isaki. Choncho Sara anaona kuti zimene Isimaeli ankachitazi zikanabweretsa mavuto aakulu kwa mwana wakeyo. Iye ankadziwa kuti Isaki sanali mwana wamba. Yehova anali atalonjeza kuti adzagwiritsa ntchito Isakiyo pokwaniritsa cholinga chake. Choncho Sara analimba mtima n’kulankhula ndi mwamuna wake za nkhaniyi. Anamuuza kuti athamangitse Hagara ndi mwana wakeyo.​—Genesis 21:8-10; Agalatiya 4:22, 23, 29.

Ndiye kodi Abulahamu anatani? Baibulo limati: “Abulahamu anaipidwa nazo kwambiri zimenezi chifukwa cha mwana wake.” Iye ankakonda kwambiri Isimaeli ndipo ankaona kuti si bwino kumuthamangitsa. Koma zimenezi zinali zosiyana ndi mmene Yehova ankaionera nkhaniyi. Baibulo limati: “Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Usaipidwe ndi chilichonse chimene Sara wakhala akunena kwa iwe chokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mvera mawu ake, chifukwa amene adzatchedwa mbewu yako adzachokera mwa Isaki.’” Yehova anatsimikizira Abulahamu kuti asamalira Hagara ndi mnyamatayo. Popeza Abulahamu anali wokhulupirika, anamvera zimene Yehova anamuuzazi.​—Genesis 21:11-14.

Sara anali mkazi wabwino ndipo ankathandiza kwambiri mwamuna wake. Sikuti iye ankangouza mwamuna wakeyo zinthu zimene akanakonda kumva. Choncho ataona kuti panali vuto lomwe likanasokoneza banja lawo, mwinanso tsogolo lawo, Sara analimba mtima n’kuuza mwamuna wake za vutolo. Koma tisaganize kuti zimene Sara anachitazi kunali kupanda ulemu. Mtumwi Petulo, yemwenso anali wokwatira, ananena kuti Sara ndi chitsanzo chabwino kwa akazi pa nkhani yolemekeza kwambiri amuna awo. (1 Akorinto 9:5; 1 Petulo 3:5, 6) Kunena zoona, ngati Sara akanangokhala chete, sakanasonyeza ulemu kwa mwamuna wake. Tikutero chifukwa vutoli likanakhudza Abulahamu komanso banja lake lonse. Sara ananena zimene ankafunika kunena, koma mwaulemu.

Akazi ambiri amaona kuti Sara ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yolankhula mwaulemu kwa amuna awo. Nthawi zina akazi amalakalaka Yehova atalowerera pa nkhani inayake n’kuuza amuna awo kuti awamvere ngati mmene zinakhalira ndi Sara. Komabe, iwo amatengera chitsanzo cha Sara pokhala ndi chikhulupiriro, chikondi komanso kuleza mtima.

Yehova anatchula Sara kuti “Mfumukazi,” komabe iye sankayembekezera kuti azipatsidwa ulemu wachifumu

Ngakhale kuti Yehova anatchula Sara kuti “Mfumukazi,” iye sankayembekezera kuti azipatsidwa ulemu wachifumu. Choncho, n’zosadabwitsa kuti pamene anamwalira, ali ndi zaka 127, Abulahamu ‘anamulira’ kwambiri. * (Genesis 23:1, 2) Iye ankamusowa kwabasi mkazi wake wokondedwayu. Sitikukayikira kuti nayenso Yehova amamusowa zedi mayi wokhulupirikayu ndipo adzamuukitsa m’Paradaiso padziko lapansi. Sara akadzaukitsidwa adzasangalala kwambiri. N’chimodzimodzinso onse omwe amayesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha Sara.​—Yohane 5:28, 29.

^ ndime 3 Abulahamu ndi Sara ankadziwika kuti Abulamu ndi Sarai mpaka pamene Mulungu anawasintha mayina. Koma m’nkhaniyi tiziwatchula ndi mayina amene amadziwika nawo kwambiri omwe ndi Abulahamu ndi Sara.

^ ndime 10 Pa nthawiyo Yehova ankalola mitala komanso kukhala ndi akazi apambali. Koma patapita nthawi anapatsa Yesu Khristu mphamvu kuti abwezeretse lamulo lokhudza ukwati, lomwe linalipo m’munda wa Edeni. Lamulo lake linali loti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi.​—Genesis 2:24; Mateyu 19:3-9.

^ ndime 25 Sara ndi mkazi yekhayo amene Baibulo limatchula kuti anali ndi zaka zingati pamene ankamwalira.