Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndinu ofunika kwambiri.”​—MATEYU 10:31

Kodi Mulungu Amachita Chidwi ndi Zimene Zimakuchitikirani?

Kodi Mulungu Amachita Chidwi ndi Zimene Zimakuchitikirani?

ZIMENE CHILENGEDWE CHIMATIPHUNZITSA PA NKHANIYI

Mwana akangobadwa, maminitsi 60 oyambirira amakhala ofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zimene mayi angachite posonyeza chikondi kwa mwanayo pa nthawiyi, zingamuthandize kuti akule bwino. *

Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti mayi ayambe kukonda kwambiri mwana wake amene wangobadwa kumene? Pulofesa wina dzina lake Jeannette Crenshaw analemba m’buku lake lina kuti, pali mtundu winawake wa mahomoni omwe amachuluka pa nthawi yobereka. Mahomoniwa amathandiza kuti mayi “azifuna kuthandiza mwana wake” komanso kuti ayambe kumukonda kwambiri. (The Journal of Perinatal Education). N’chifukwa chiyani zimenezi zili zochititsa chidwi?

Yehova Mulungu, * yemwe ndi Mlengi wathu wachikondi, analenga azimayi m’njira yakuti azikonda kwambiri ana awo. Davide anayamikira Mulungu chifukwa choti ‘anamutulutsa kuchokera m’mimba’ n’kuchititsa kuti mayi ake amusamalire mwachikondi. Iye anapemphera kuti: “Ndinaponyedwa m’manja mwanu kuchokera m’mimba. Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.”​—Salimo 22:9, 10.

TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: Ngati Mulungu analenga azimayi m’njira yakuti azichita chidwi ndi ana awo komanso aziwasamalira mwachikondi, kodi si zomveka kuti nayenso amachita chidwi ndi zimene zikuchitika pa moyo wathu monga ana ake kapena kuti “mbadwa” zake?​—Machitidwe 17:29.

BAIBULO LIMASONYEZA KUTI MULUNGU AMACHITA NAFE CHIDWI

Yesu Khristu, yemwe amamudziwa bwino Mlengi wathu kuposa wina aliyense, anaphunzitsa kuti: “Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”​—Mateyu 10:29-31.

Ndi anthu ochepa kwambiri amene amachita chidwi ndi mbalame iliyonse yaing’ono imene aiona, ndipo sachita chidwi n’komwe ndi ‘mbalame imene yagwa pansi.’ Komatu Atate wathu wakumwamba amachita chidwi ndi mbalame iliyonse! Ngakhale zili choncho, munthu ndi wofunika kwambiri kuposa mbalame zochuluka. Apatu phunziro lake ndi loonekeratu. Simuyenera ‘kuchita mantha’ n’kumaganiza kuti Mulungu alibe nanu ntchito. Dziwani kuti iye amachita nanu chidwi komanso amakukondani kwambiri.

Mulungu amachita chidwi ndi zimene zikuchitika pa moyo wathu ndipo amatisamalira mwachikondi

Malemba awa amatitsimikizira mfundo imeneyi

  • “Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.”​—MIYAMBO 15:3.

  • “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”​—SALIMO 34:15.

  • “Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.”​—SALIMO 31:7.

“NDINKAONA KUTI YEHOVA SANDIKONDA”

Kodi kudziwa kuti Mulungu amachita chidwi ndi zimene zikuchitika pa moyo wathu komanso kuti amatiteteza n’kothandiza? Inde n’kothandiza. Umboni wake ndi zimene Hannah * wa ku England ananena. Iye anati:

“Ndinkaona kuti Yehova sandikonda komanso kuti mapemphero anga sakuyankhidwa. Poyamba ndinkaganiza kuti zimenezi zikuchitika chifukwa choti ndilibe chikhulupiriro. Ndinkaona kuti Mulungu akundilanga kapena wandinyanyala ndipo amandiona kuti ndine wosafunika.”

Koma panopa Hannah amaona kuti Yehova amachita naye chidwi komanso amamukonda kwambiri. N’chiyani chinapangitsa kuti asinthe maganizo? Iye anati: “Ndinayamba kusintha pang’onopang’ono. Ndikukumbukira kuti zaka zambiri zapitazo, ndinamvetsera nkhani ya m’Baibulo yonena za nsembe ya Yesu. Nkhaniyi inandilimbikitsa kwambiri komanso inandithandiza kuti ndiyambe kuona kuti Yehova amandikonda. Yehova akayankha mapemphero anga, nthawi zina ndimalira popeza panopa ndinadziwa kuti iye amandikonda kwambiri. Komanso ndaphunzira zambiri zokhudza Yehova kuchokera m’Baibulo ndiponso pamisonkhano yathu yachikhristu. Ndaphunziranso zambiri zokhudza makhalidwe ake komanso mmene amasonyezera kuti amatikonda. Panopa sindikayikira kuti Yehova amatithandiza, kutikonda komanso kusamalira munthu aliyense payekha.”

Zimene Hannah ananenazi n’zolimbikitsa. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu amatimvetsa komanso amadziwa mmene tikumvera tikamakumana ndi mavuto? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.

^ ndime 3 Azimayi ena omwe amadwala matenda osokonezeka maganizo akangobereka, (Postpartum Depression) amalephera kukonda ana awo. Komabe azimayi amenewa sayenera kudziimba mlandu chifukwa cha zimenezi. Bungwe lina linanena kuti, matendawa “amayamba chifukwa cha kusokonekera kwa zinthu zina m’thupi . . . osati chifukwa cha zinthu zimene mayiyo wachita kapena walephera kuchita.” (U.S. National Institute of Mental Health) Kuti mumve zambiri zokhudza matendawa, werengani nkhani yakuti “Understanding Postpartum Depression,” mu Galamukani! yachingelezi ya June 8, 2003.

^ ndime 5 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.​—Salimo 83:18.

^ ndime 15 Mayina ena asinthidwa munkhanizi.