Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULANDIRA MPHATSO YAIKULU IMENE MULUNGU WAPEREKA?

N’chifukwa Chiyani Mphatso Imene Mulungu Watipatsa Ndi Yamtengo Wapatali?

N’chifukwa Chiyani Mphatso Imene Mulungu Watipatsa Ndi Yamtengo Wapatali?

Kodi mumaona kuti mphatso ndi yamtengo wapatali kwambiri ikakhala yotani? Ziyenera kuti zimadalira zinthu 4 izi: (1) munthu amene anakupatsani, (2) chifukwa chimene anaiperekera, (3) zimene anadzimana kuti aipereke ndiponso (4) ngati ndi chinthu chimene mumafunikira kwambiri. Kuganizira mfundo 4 zimenezi kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri dipo, lomwe ndi mphatso yaikulu imene Mulungu anapereka.

NDANI ANAIPEREKA?

Mphatso zina timaziona kuti ndi zamtengo wapatali chifukwa choti anthu amene anatipatsa ndi audindo kapena olemekezeka. Koma mphatso zina, kaya zikhale zazing’ono bwanji, timaona kuti ndi zofunika kwambiri chifukwa chakuti amene anatipatsa ndi wachibale amene timamukonda kwambiri kapena mnzathu amene timamudalira. Umu ndi mmene zinalili ndi mphatso imene Russell anapatsa Jordan, yomwe taifotokoza m’nkhani yapitayi. Koma nanga izi zikugwirizana bwanji ndi mphatso ya dipo?

Choyamba, Baibulo limanena kuti Mulungu “anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Mfundoyi imachititsa kuti mphatsoyo ikhale yamtengo wapatali kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu ndi waudindo komanso wolemekezeka kuposa aliyense. Ponena za Mulungu, munthu wina wolemba Masalimo anati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Choncho palibenso munthu wina wapamwamba kuposa Mulungu amene angatipatse mphatso.

Chachiwiri, Mulungu ndi “Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Zili choncho chifukwa anatipatsa moyo. Komanso iye amatisamalira nthawi zonse ngati mmene bambo angasamalirire ana ake. Polankhula za anthu ake, Mulungu anawatchula kuti Efuraimu ndipo anafunsa kuti: “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa? . . . N’chifukwa chake m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye. Mosalephera ndidzamumvera chisoni.” (Yeremiya 31:20) Umu ndi mmene Mulungu amaoneranso anthu ake amasiku ano. Sikuti iye wangokhala Mlengi wathu chabe koma ndi Atate wathu wokhulupirika komanso Mnzathu wapamtima. N’chifukwa chake, mphatso iliyonse imene angatipatse ndi yamtengo wapatali.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANAIPEREKA?

Mphatso zina zimakhala zamtengo wapatali ngati munthu watipatsa chifukwa choti amatikonda osati chifukwa choti ndi udindo wake. Munthu amene akupereka chinthu ndi mtima wonse sayembekezera kuti nayenso apatsidwe kenakake.

Mulungu anapereka Mwana wake chifukwa choti amatikonda. Baibulo limati: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Kodi Mulungu anali ndi udindo wochita zimenezi? Ayi ndithu. Kungoti Mulungu anasonyeza ‘kukoma mtima kwakukulu’ popereka dipoli.—Aroma 3:24.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti mphatso ya Mulunguyi ndi umboni wa “kukoma mtima kwake kwakukulu”? Baibulo limati: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Mtima wachikondi ndi umene unalimbikitsa Mulungu kuti athandize anthu ochimwa amene analibiretu mtengo wogwira. Anthufe sitinkayenera kupatsidwa mphatsoyi ndipo sitingathe kubwezera Mulungu. Mphatso yake imasonyeza chikondi chachikulu kuposa chilichonse chimene anthu angasonyeze.

KODI ANADZIMANA CHIYANI KUTI AIPEREKE?

Mphatso zina zimakhala zamtengo wapatali chifukwa woperekayo anadzimana zambiri pozipereka. Munthu akalolera kutipatsa chinthu chomwe amachikonda kwambiri, timayamikira kwambiri mphatsoyo.

Mulungu “anapereka Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Palibe munthu wina amene amamukonda kwambiri kuposa mwanayo, yemwe akanapereka. Kwa zaka zambiri zomwe Mulungu ankalenga zinthu, Yesu ankagwira naye ntchito ndipo Mulunguyo ‘ankasangalala naye kwambiri.’ (Miyambo 8:30) Yesu ndi “Mwana wake wokondedwa” komanso “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo.” (Akolose 1:13-15) Palibe anthu ena amene akhala ogwirizana kwambiri ngati mmene zilili ndi Mulungu ndi Mwana wake.

Komabe Mulungu “sanaumire ngakhale Mwana wake.” (Aroma 8:32) Iye anatipatsa mphatso yabwino kwambiri ndipo anadzimana zambiri poipereka.

NDI CHINTHU CHIMENE TIMAFUNIKIRA KWAMBIRI

Mphatso zina zimakhala zamtengo wapatali chifukwa choti ndi chinthu chimene munthu amene wapatsidwayo ankachifuna kwambiri. Mwachitsanzo, kodi inuyo mungamve bwanji ngati mutadwala mwakayakaya ndiye munthu wina n’kukulipirirani kuchipatala chimene simukanatha kuchilipirira? Kunena zoona mphatso imeneyo ingakhale yamtengo wapatali kwambiri.

Baibulo limati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Popeza ndife ana a Adamu, tonsefe timafa ndipo palibe chimene tingachite kuti tisamadwale kapena kufa. Patokha sitingagwirizanenso ndi Mulungu kapena kukhala opanda mlandu. Sitingathenso kudzipatsa moyo kapena kupatsa ena moyo. Baibulo limanena kuti: “Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake, kapena kumuperekera dipo kwa Mulungu.” Limanenanso kuti anthu ‘sangathe kupereka malipiro owombolera moyo mpaka kalekale.’ (Salimo 49:7, 8) Anthufe tinafunika kuthandizidwa chifukwa choti patokha sitingathe kudzipulumutsa.

Chifukwa cha chikondi chake chachikulu, Yehova anapereka zimene tinkafunikira kwambiri kuti tipeze moyo wosatha. Koma kodi dipo limathandiza bwanji kuti tipeze moyo? Baibulo limati: ‘Magazi a Yesu amatiyeretsa ku uchimo wonse.’ Choncho tikamakhulupirira nsembe ya Yesu timakhala ndi mwayi wokhululukidwa machimo komanso woti tidzapeze moyo wosatha. (1 Yohane 1:7; 5:13) Nanga dipo lidzathandiza bwanji anthu amene anamwalira? Baibulo limati: “Popeza imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi [Yesu].”—1 Akorinto 15:21. *

Palibe mphatso imene inaperekedwa ndi munthu wamkulu kwambiri kapena ndi chikondi chachikulu kuposa mphatso ya nsembe ya Yesu. Palibenso amene anadzimana kwambiri kuti atipatse mphatso ngati mmene Yehova anachitira. Komanso palibe mphatso imene ndi yofunika kwambiri kuposa nsembe ya Yesu yomwe imatimasula ku uchimo ndi imfa. Kunena zoona, mphatso ya dipo ndi yamtengo wapatali kuposa mphatso ina iliyonse.

 

^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu choukitsa anthu amene anamwalira, werengani mutu 7 wa buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa www.pr418.com/ny.