Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Kuti Musavutike Kwambiri ndi Masoka Achilengedwe

Zimene Mungachite Kuti Musavutike Kwambiri ndi Masoka Achilengedwe

Masiku ano, masoka achilengedwe akuchitika pafupipafupi ndiponso akukhala oopsa kwambiri. Poona mmene zinthu zililimu, kodi munthu angatani kuti asavutike kwambiri ndi masokawa? Tiyeni tione bwinobwino mfundo zingapo zothandiza zimene munthu angatsatire.

Musakhale kumalo angozi.

Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” (Miyambo 22:3) Amenewa ndi malangizo anzeru omwe angagwire ntchito pa masoka achilengedwe. Ngati chenjezo laperekedwa lakuti m’dera linalake phiri liphulika, madzi asefukira, kapena mugwa mvula yoopsa yophatikizana ndi mphepo yamkuntho, munthu angachite bwino kuchoka m’deralo n’kupita kudera lina labwinopo. Moyo ndi wamtengo wapatali kuposa nyumba kapena katundu wina aliyense.

Kwa anthu ena, n’zotheka kusankha kuti asamakhale m’dera limene mumachitikachitika masoka achilengedwe. Katswiri wina pa nkhani imeneyi anati: “Masoka ambiri achilengedwe amachitika m’malo omweomwewo. Ndipo ndi gawo lochepa kwambiri la dziko lapansili kumene kumachitikachitika masoka. Choncho tingayembekezere kuti ambiri mwa masoka achilengedwe oopsa kwambiri adzachitika m’malo amenewa.” Zimenezi zili choncho makamaka m’madera otsika a m’mbali mwa nyanja kapena madera amene mumachitikachitika zivomezi padziko lapansili. Mukhoza kupewa kuvutika kwambiri ndi masoka achilengedwe ngati mungapewe kukhala m’madera omwe mumachitikachitika masoka, kapena ngati mungasamukire kudera lina labwinopo.

Dziwiranitu zochita.

Ngakhale mutayesetsa kuchita zonse zimene mungathe, nthawi zina mungapezeke kuti mwakhudzidwabe ndi tsoka la mwadzidzidzi. Mungapulumuke mosavuta ndiponso mungapirire tsoka lotero ngati munakonzekereratu. Zimenezi zikugwirizananso ndi malangizo amene ali pa Miyambo 22:3, omwe tawatchula koyambirira aja. Mwachitsanzo, kodi mumasungiratu zinthu zofunika kwambiri zimene mungagwiritse ntchito patagwa tsoka? Buku lina la malangizo okhudza masoka achilengedwe (1-2-3 of Disaster Education) limalimbikitsa kuti ndi bwino kusunga zinthu zotsatirazi: Mankhwala ndi zipangizo zina zothandizira munthu wovulala, madzi a m’botolo, chakudya chomwe sichingawonongeke msanga, ndiponso zikalata zofunika kwambiri. Mungachitenso bwino kukambirana ndi banja lanu lonse za masoka amene angachitike m’dera lanu komanso zimene mungachite pa tsoka lililonse.

Mukhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Zimenezi zimathandiza nthawi zonse. Baibulo limanena kuti Mulungu ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” Vesi linanso limanena kuti iye ndi Mulungu “amene amalimbikitsa osautsika mtima.”​—2 Akorinto 1:3, 4; 7:6.

Ndithudi, Mulungu amadziwa bwino mavuto onse omwe anthu amene amamukhulupirira amakumana nawo. Iye ndi Mulungu wachikondi ndipo amalimbikitsa anthu m’njira zosiyanasiyana. (1 Yohane 4:8) Pemphero, osati lopempha zozizwitsa, koma lopempha mphamvu ya Mulungu ya mzimu woyera, lingatithandize kwambiri pa mavuto alionse. Mzimu woyera ungathandize anthu amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana kukumbukira mavesi a m’Baibulo olimbikitsa ndi otonthoza. Atumiki a Mulungu okhulupirika angamve ngati mmene anamvera Davide, mfumu ya Isiraeli, amene anati: “Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani, sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine. Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.”​—Salimo 23:4.

Akhristu amathandizana pakagwa tsoka

Akhristu amathandizana.

M’nthawi ya atumwi, mneneri wachikhristu wotchedwa Agabo analosera kuti “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo.” Ambiri mwa ophunzira a Yesu a ku Yudeya anavutika kwambiri ndi njalayo. Kodi ophunzira a m’madera ena anatani atamva za vuto limene Akhristu anzawo anakumana nalo? Nkhaniyi imati: “Aliyense wa ophunzirawo, anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.” (Machitidwe 11:28, 29) Iwo anasonyeza chikondi potumiza thandizo kwa abale awowo.

Nawonso Akhristu a Mboni za Yehova amadziwika bwino pa nkhani yothandizana pakagwa masoka aakulu masiku ano. Mwachitsanzo, pamene chivomezi champhamvu kwambiri chinachitika m’dziko la Chile pa February 27, 2010, anthu a Mboni za Yehova anayamba mwamsanga kuthandiza anthu amene anakhudzidwa. Mayi wina dzina lake Karla, yemwe nyumba yake inakokoloka ndi tsunami, anati: “Zinali zotonthoza ndi zolimbikitsa kuona kuti tsiku lotsatira [a Mboni anzathu] anafika kuchokera m’madera ena kudzatithandiza. Zoonadi, Yehova anatitonthoza ndi zinthu zabwino zimene anthu ongodziperekawo anatichitira. Zimenezi zinandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka ndiponso wokondedwa.” Agogo ake aamuna, omwe si a Mboni, ankaonerera pamene thandizoli linali kuperekedwa. Iwo anati: “Izi n’zosiyana kwambiri ndi zimene ndakhala ndikuona kwa zaka zambiri kutchalitchi kwathu.” Zimene anaonazo zinawachititsa kuti apemphe a Mboni za Yehova kuti aziphunzira nawo Baibulo.

“Ndinamva kuti ndine wotetezeka ndiponso wokondedwa”

Kukhala m’gulu la anthu amene amakonda Mulungu kumathandiza kwambiri pa nthawi ya mavuto. Komabe, kodi masoka amene akuchitika padzikoli adzatha? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.