Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe

Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe

KODI panopa mukuvutika chifukwa cha matenda aakulu, kutha kwa banja kapena kuferedwa? Munthu akakumana ndi mavuto ngati amenewa amasowa chochita koma amafuna zinthu zitasintha. Ndiye kodi mungatani?

CHITSANZO CHA M’BAIBULO: PAULO

Mtumwi Paulo anali mmishonale wakhama ndipo ankayenda m’madera osiyanasiyana. Koma zinthu zinasintha pamene anamangidwa n’kumalonderedwa ndi asilikali kwa zaka ziwiri. M’malo motaya mtima, Paulo anaganizira zimene angathe kuchita. Iye ankaphunzitsa ndiponso kulimbikitsa anthu amene ankabwera kudzamuona. Analembanso makalata angapo amene ali m’Baibulo.—Machitidwe 28:30, 31.

ZIMENE ANJA AMACHITA

Paja tanena kale kuti Anja amangokhala pakhomo. Ndiyeno iye anati: “Matenda a khansa asokoneza kwambiri moyo wanga. Ngati nditayenda ndikhoza kudwala kwambiri, choncho sindipita kuntchito kapena kocheza.” Kodi Anja amatani ndi vuto lakeli? Iye anati: “Ndinangosintha zochita pa moyo wanga. Ndinaganizira zofunika kwambiri n’kulemba ndandanda ya zimene ndingakwanitse kuchita. Zimenezi zandithandiza kwambiri.”

“Ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo.”—Izi n’zimene Paulo ananena pa Afilipi 4:11

ZIMENE MUNGACHITE

Ngati vuto lanu ndi loti simungalisinthe, yesani kuchita izi:

  • Ganizirani zimene mungathe kuchita. Mwachitsanzo, ngati muli ndi matenda, mwina mungathe kumachitabe masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chabwino komanso kupuma mokwanira

  • Khalani ndi zolinga pa moyo wanu. Zolingazo muziike m’zigawo zing’onozing’ono. Ndiyeno tsiku lililonse muzichita zochepa mpaka mudzazikwaniritse.

  • Muziyesetsa kuchita zinazake ngakhale zing’onozing’ono kuti mumtima muzimva kuti mwapanga kenakake. Mwachitsanzo, mungayeretse tebulo, kutsuka mbale kapena kudzisamalira bwinobwino. Muziyesetsa kuchita zinthu zofunika kwambiri chakum’mawa.

  • Ganizirani zabwino zimene mungachite chifukwa cha mavuto anuwo. Mwachitsanzo, panopa mukhoza kumvetsa ndiponso kuthandiza anthu amene akukumana ndi mavuto ngati anuwo.

Mfundo Yofunika: Mavuto ena simungawasinthe koma mukhoza kusintha zimene mumachita mukakumana ndi mavutowo.