Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokwatirana ndi Munthu wa Mtundu Wina?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokwatirana ndi Munthu wa Mtundu Wina?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu amavomereza ukwati wa mwamuna ndi mkazi osiyana mitundu chifukwa amaona kuti anthu a mitundu yonse ndi ofanana. Baibulo limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse.”​—Machitidwe 10:​34, 35.

 Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi n’zothandiza pa nkhani ya kusiyana mitundu ndiponso ukwati.

Anthu a mitundu yonse ndi ana a Adamu ndi Hava

 Anthu onse anachokera kwa anthu oyamba, Adamu ndi Hava. Baibulo limatchula Hava kuti “mayi wa munthu aliyense wamoyo.” (Genesis 3:20) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: ’Kuchokera mwa munthu mmodzi, [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.’ (Machitidwe 17:26) Anthu a mitundu yonse ndi a m’banja limodzi. Koma kodi mungatani ngati anthu a kumene mukukhala amasala anthu a mitundu ina kapena amene akusiyana nawo zinthu zina?

Anthu anzeru ‘amakambirana’

 Ngakhale kuti Mulungu amavomereza ukwati wa anthu osiyana mitundu, anthu ena savomereza zimenezi. (Yesaya 55:​8, 9) Ngati mukuganiza zolowa m’banja ndi munthu wa mtundu wina, mungachite bwino kukambirana mafunso otsatirawa ndi mnzanuyo.

  •   Kodi mungatani kuti musavutike anthu ena kapena achibale anu akanena kapena kuchita zokhumudwitsa?

  •   Kodi muthandiza bwanji ana anu kuti asamavutike kwambiri akamasalidwa?

 Kukambirana mfundo ngati zimenezi kungathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.​—Miyambo 13:10; 21:5.